Kulalikira Kumafuna Kupirira
1 Kwa zaka zoposa 30, mtumwi Paulo anali wosangalala chifukwa ntchito yake yaikulu inali yolalikira. Ntchito iliyonse yaphindu imakhala ndi mavuto ake, ndipo ndi mmenenso zinalili ndi ntchito ya Paulo yolalikira. (2 Akor. 11:23-29) Komatu Paulo sanabwerere m’mbuyo. (2 Akor. 4:1) Iye anadziwa kuti Yehova ndi amene angamupatse mphamvu zoti apirire kuti athe kukwaniritsa utumiki wake. (Afil. 4:13) Chifukwa cha chitsanzo chake cha kukhulupirika ndi kupirira, Paulo ananena kuti: “Khalani otsanzira ine, monga inenso ndili wotsanzira Khristu.”—1 Akor. 11:1.
2 Kupirira Mayesero Masiku Ano: Tsiku lililonse abale athu ambiri amanyozedwa, kutsutsidwa, kapena kudedwa ndi achibale awo, anzawo a kuntchito kapena anzawo a kusukulu. (Mat. 10:35; Yoh. 15:20) Mwina umu ndi mmene zililinso ndi inuyo. N’kutheka kuti tsiku ndi tsiku mukuvutika ndi matenda kapena mukuyesetsa kulimbana ndi zinthu zimene zikuyesa kupirira kwanu ndiponso chikhulupiriro chanu. Tingapeze mphamvu mwa kutengera zitsanzo za atumiki okhulupirika akale komanso Akhristu anzathu masiku ano amene akumana ndi kuthana ndi mavuto amenewa.—1 Pet. 5:9.
3 Tingapezenso mphamvu kuti tikhalebe olimba muutumiki ngati tikuyesetsa ‘kuvala zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu.’ (Aef. 6:10-13, 15) Pemphero ndi lofunikanso kwambiri kuti tipirire. Mulungu amapereka mzimu wake woyera kuti utithandize kupirira mayesero. (2 Akor. 6:4-7) Kuti tipambane pankhondo yauzimuyi tiyenera kumvera malangizo a Mulungu onena kuti tizikonza mzimu wathu kuti uzikhala watsopano. (Sal. 119:24, 85-88) Monga mmene mwana angawerengere mobwerezabwereza kalata yochokera kwa bambo ake amene amam’konda, tiyenera kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kuti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova. Tikamachita phunziro laumwini nthawi zonse timapeza nzeru zotithandiza kupirira mayesero ndipo timalola nzeru ya Mulungu kutitsogolera pa zosankha zathu komanso timakhalabe okhulupirika kwa Yehova.—Miy. 2:10, 11.
4 Kupirira Kumabweretsa Madalitso: Monga mmene zinalili ndi Paulo kukhulupirika kwathu komanso kupirira kwathu muutumiki kumasangalatsa mtima wa Yehova ndipo kumabweretsa madalitso kwa ifeyo komanso kwa anthu ena. (Miy. 27:11) Tiyeni tipitirizebe kuchita utumiki komanso kusonyeza kuti chikhulupiriro chathu n’cholimba kwambiri ndipo ndi “chamtengo wapatali kuposa golide amene amawonongekabe ngakhale kuti anadutsa m’moto.”—1 Pet. 1:6, 7.