Bokosi la Mafunso
◼ Kodi n’zoyenera kuti mipingo kapena munthu aliyense azigwiritsa ntchito zizindikiro zimene mabungwe a Mboni za Yehova amagwiritsa ntchito?
Chizindikiro chingakhale dzina kapena chinthu china chilichonse chimene mabungwe amagwiritsa ntchito kuti aziwazindikira mosavuta. Chizindikiro cha nsanja chimaimira bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania ndi mabungwe ena a Mboni za Yehova. Bungwe la Christian Congregation of Jehovah’s Witnesses limagwiritsa ntchito chizindikiro cha Baibulo lotsegula m’makalata ake. Mabungwe enanso a Mboni za Yehova ali ndi zizindikiro zawo.
Si bwino kuti mipingo kapena munthu aliyense azigwiritsa ntchito mayina kapena zizindikiro zimenezi kapenanso zinthu zofanana ndi zizindikiro za mabungwe amenewa pa Nyumba za Ufumu, pa zikwangwani, pa makalata kapena pa zinthu zina. Kugwiritsa ntchito zizindikirozi mwa njira imeneyi kungasokoneze akuluakulu a boma, ofalitsa mumpingo komanso anthu ena. Iwo sangathe kusiyanitsa ntchito za mpingowo ndi za mabungwe ena a Mboni za Yehova. Komanso, anthu angamaganize kuti makalatawo achokera kapena avomerezedwa ndi likulu la Mboni za Yehova kapena ofesi ya nthambi.
Chizindikiro cha bungwe la Watch Tower kapena chizindikiro china chofanana ndi chimenechi, sichiyenera kuikidwa pa Nyumba za Ufumu zimene zimangidwe m’tsogolo muno ngakhale zitakhala kuti nyumbazo zamangidwa ndi bungwe la Watch Tower. Koma mipingo imene ili kale ndi Nyumba ya Ufumu yokhala ndi zizindikiro zimenezi sikufunika kusintha mwamsanga chifukwa kuchita zimenezi ndi ntchito yaikulu ndipo kungafune nthawi ndi ndalama zambiri. Komabe, mungasinthe ngati mukuona kuti ntchito yake si yambiri komanso siiwononga ndalama zambiri. Apo ayi, mungadzasinthe pamene mukukonzanso Nyumba ya Ufumu yanu kapena chikwangwani chake.