Mawu a Mulungu Ndi Amphamvu
1. Kodi mutu wa msonkhano wapadera wa chaka cha utumiki cha 2014 ndi woti chiyani?
1 Mosiyana ndi zinthu zimene anthu opanda ungwiro amapanga, Baibulo lili ndi mphamvu zimene zikhoza kusintha maganizo athu ndiponso zochita zathu kuti zikhale zogwirizana ndi zimene Yehova amafuna. Kodi Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu zochuluka bwanji? Kodi tingatani kuti tithe kugwiritsa ntchito mphamvu zimenezi mokwanira pa moyo wathu? Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mphamvu zimenezi mokwanira kuti tithandizire ena? Tikukhulupirira kuti mudzalimbikitsidwa kwambiri mwauzimu pamene mfundo zimenezi zizidzafotokozedwa pa msonkhano wapadera umene udzachitike m’chaka cha utumiki cha 2014. Mutu wake ndi wakuti, “Mawu a Mulungu Ndi Amphamvu,” ndipo watengedwa pa lemba la Aheberi 4:12.
2. Kodi tidzapeze mayankho a mafunso ati?
2 Mudzapeze Mayankho a Mafunso Awa: Pamene mukumvetsera msonkhanowu, mudzapeze mayankho a mafunso amene ali m’munsiwa.
• N’chifukwa chiyani tiyenera kudalira mawu a Yehova (Aheb. 4:12)
• Kodi tingatani kuti tione mphamvu ya mawu a Mulungu ikugwira ntchito pa moyo wathu? (Sal. 34:8)
• N’chiyani chingatithandize kuti tizilengeza za mphamvu ya mawu a Mulungu mu utumiki? (2 Tim. 3:16, 17)
• Kodi tingapewe bwanji kugwa mumsampha wokhulupirira chinyengo champhamvu cha dziko la Satanali? (1 Yoh. 5:19)
• Monga wachinyamata, kodi mungatani kuti zinthu zizikuyenderani bwino mwauzimu? (Yer. 17:7)
• Kodi tingatani kuti tikhalebe amphamvu ngakhale pamene tafooka? (2 Akor. 12:10)
• Kodi chinthu chofunika kwambiri n’chiyani kuti tipitirize kusintha moyo wathu ngakhale titakhala ndi zizolowezi zina zamphamvu kwambiri? (Aef. 4:23)
3. Kuwonjezera pa kumvetsera pulogalamu, kodi tingadzapindulenso bwanji ndi msonkhano wapadera?
3 Tidzapindulatu kwambiri ndi mfundo zothandiza zimenezi. Kuwonjezera pamenepo, msonkhano wapaderawu mofanana ndi msonkhano wadera ndiponso msonkhano wachigawo, udzatipatsa mwayi wodziwana ndiponso kucheza ndi abale ndi alongo a mipingo ina. (Sal. 133:1-3; 2 Akor. 6:11-13) Choncho, mudzapeze nthawi yocheza ndi anzanu akale ndiponso kupeza anzanu atsopano. Ngati mlendo amene mudzakhale naye pamsonkhanowu ndi m’bale woyang’anira chigawo kapena woimira Beteli, bwanji osadzapatula nthawi yocheza naye ndiponso yocheza ndi mkazi wake? Kunena zoona, tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kuyembekezera mwachidwi msonkhano wapaderawu.