Nthawi Zonse Khalani Wokonzeka Kuyambitsa Phunziro la Baibulo
1. Kodi kukwaniritsa ntchito imene Yesu anatipatsa, yolembedwa pa Mateyo 28:19, 20, kumaphatikizapo chiyani?
1 Yesu anatipatsa ntchito ‘yopanga ophunzira ndi kuwaphunzitsa.’ (Mat. 28:19, 20) Choncho, tikufuna kuti nthawi zonse tizikhala okonzeka kuyambitsa phunziro la Baibulo. Kuti tikhale ndi maphunziro a Baibulo, sitiyenera kungodalira tsiku limodzi pa mwezi limene linaikidwa loyambitsa maphunziro a Baibulo. Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kuyambitsa phunziro la Baibulo.
2. Kodi tingapemphe ndani kuti tiyambe kuphunzira nawo Baibulo?
2 Apempheni Kuti Muyambe Kuphunzira Nawo Baibulo: Tikamakonda kupempha anthu kuti tiyambe kuphunzira nawo Baibulo, sizingakhale zovuta kupeza munthu woti tiziphunzira naye. (Mlal. 11:6) Kodi munayesapo kuyambitsa phunziro mwachindunji? Abale ndi alongo a mumpingo wina wa ku United States anayesetsa kuchita zimenezi kwa mwezi wathunthu. Iwo anayambitsa maphunziro a Baibulo okwanira 42 ndipo anasangalala kwambiri. Musaganize kuti anthu achidwi amene mumawapeza mu utumiki amadziwa kuti cholinga chanu chimakhala kuyambitsa phunziro la Baibulo. Pa ulendo wobwereza wotsatira mungachite bwino kuwalimbikitsa kuti muyambe kuphunzira nawo Baibulo. Ngati angakane, musadandaule koma pitirizani kuwayendera kuti chidwi chawo chikule. Kodi mwapemphapo anthu amene mumakhala nawo pafupi, achibale, ogwira nawo ntchito ndiponso anzanu akusukulu kuti muziphunzira nawo Baibulo? Mungafunse anthu amene mukuphunzira nawo Baibulo ngati ali ndi anzawo kapena achibale amene angafunenso kuphunzira Baibulo.
3. Kodi tili ndi kapepala kati kamene kangatithandize kuyambitsa maphunziro a Baibulo, ndipo tizikagwiritsa ntchito bwanji?
3 Kapepala Kamene Kangathandize: Kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? kamathandiza kwambiri poyambitsa maphunziro a Baibulo. Mungapatse eninyumba kapepalaka, kaya alandira mabuku ena kapena ayi. Mungakaperekenso kwa anthu m’dera lochitira malonda, kwa anthu amene mukukumana nawo mumsewu, ndiponso mungakaphatikize m’makalata amene mwalembera anthu ena komanso mungapatse anthu pa ulendo wobwereza. Mungakasiyenso panyumba imene simunapezepo munthu. Mapepalawa mungawatenge mukakhala pa ulendo, pokagula zinthu kapena popita kuntchito. Mawu amene ali patsamba lomalizira la kapepalaka amafotokoza kuti munthu atha kuyamba kuphunzira Baibulo ndipo amafotokozanso mwachidule za buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.
4. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji kapepala ka Kudziwa Choonadi poyambitsa phunziro la Baibulo?
4 Mukapatsa munthu kapepala kameneka, mungamusonyeze mafunso amene ali patsamba loyamba ndipo mungamufunse kuti, “Kodi ndi funso liti limene lakuchititsani chidwi?” Ndiyeno, kambiranani yankho limene lili m’kapepalako. Kenako werengani kapena kufotokoza mawu amene ali patsamba lomalizira, onena za phunziro la Baibulo. Mungamusonyezenso kumene angapeze mfundo zinanso zokhudza funso limene anasankhalo m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Mufunseni ngati angafune kuti buku limeneli likhale lake ndipo mupangane naye zodzabweranso kuti mudzapitirize kukambirana.
5. N’chifukwa chiyani nthawi zonse tiyenera kukhala okonzeka kuyambitsa phunziro la Baibulo?
5 Mugawo lathu mudakali anthu amene akufunitsitsa kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsadi. Nthawi zonse tikamakhala okonzeka kuyambitsa phunziro la Baibulo, tidzathandiza anthu ambiri kuyenda panjira yopita ku moyo wosatha.—Mat. 7:13, 14.