Tiziyesetsa Kuthandiza Anthu Kuti Akhale Ophunzira a Yesu
1. Kodi tingawathandize bwanji anthu kuti adzapulumuke?
1 Lipoti la utumiki la chaka cha 2014 linasonyeza kuti abale ndi alongo akugwira ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu modzipereka kwambiri. (Mat. 24:14) Masiku ano, anthu ambiri akumva uthenga wa m’Baibulo. Izi zikutheka chifukwa cha ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba, m’malo opezeka anthu ambiri komanso ntchito yapadera yogawira timapepala, kuphatikizapo toitanira anthu kumsonkhano kapena ku Chikumbutso. Komabe kuti anthu adzapulumuke, tiyenera kuwathandiza kuti akhale ophunzira a Yesu. Tingachite zimenezi mwa kuphunzira nawo Baibulo.—1 Tim. 2:4.
2. Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati kuti tisamaiwale zoti cholinga chathu n’kuyambitsa maphunziro?
2 Cholinga Chizikhala Kuyambitsa Phunziro: Munthu akasonyeza chidwi, kodi mumalemba zonse zofunika n’cholinga choti mudzabwerereko kukayambitsa phunziro? Nanga mumabwerera mwamsanga kwa anthu oterowo? Kodi pa ulendo woyamba mumayesetsa kusonyeza anthu mmene phunziro la Baibulo limachitikira? Kodi posachedwapa mwauzapo anthu amene mumawapatsa magazini kuti mungathe kumaphunzira nawo Baibulo? Nanga kodi munayamba mwasonyezapo vidiyo yakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? kapena yakuti, Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji? kwa anzanu akuntchito, akusukulu, okhala nawo pafupi, achibale komanso anthu ena? Mukamalalikira pogwiritsa ntchito tebulo kapena kashelefu kamatayala, kodi mumayesetsa kuuza aliyense amene watenga buku lomwe timagwiritsa ntchito pophunzira Baibulo ndi anthu, kuti angathe kumaphunzira Baibulo kwaulere?
3. N’chiyani chingatithandize kuti tizigwira bwino ntchito yophunzitsa anthu choonadi?
3 Yehova ndi Yesu Amatithandiza: Polamula otsatira ake kuti akaphunzitse anthu kuti akhale ophunzira ake, Yesu anayamba ndi mawu akuti, “Pitani.” Izi zikusonyeza kuti tiyenera kuchita khama kupita kwa anthu kukawalalikira komanso kuyamba ifeyo kuwauza uthenga wa m’Baibulo. Komabe Yesu sanatisiye tokha. Iye analonjeza kuti adzakhala nafe limodzi. (Mat. 28:19, 20) Komanso Yehova amatipatsa zinthu zonse zofunika kuti tikwanitse kugwira ntchitoyi. Kuwonjezera pamenepo, amatiphunzitsa mmene tingagwirire ntchito imeneyi ndiponso amatipatsa mzimu wake. (Zek. 4:6; 2 Akor. 4:7) Choncho tingapemphe Yehova kuti atipatse mphamvu komanso mtima wofuna kugwira nawo ntchito yofunikayi.—Afil. 2:13.
4. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuthandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu?
4 Kugwira ntchito yolalikira kumatithandiza kukhala osangalala. Koma timasangalala kwambiri tikaphunzitsa munthu choonadi, n’kumuthandiza kuti ayambe kuyenda nafe mumsewu wopita ku moyo wosatha. (Mat. 7:14; 1 Ates. 2:19, 20) Komanso tikamayesetsa kuthandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu, timasangalatsa Yehova yemwe “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.”—2 Pet. 3:9.