“Nzeru Imatsimikizirika Kukhala Yolungama mwa Ntchito Zake”
1. Kodi anthu ena amaiona bwanji ntchito yathu?
1 Nthawi zina anthu satilandira bwino mu utumiki wathu chifukwa sadziwa zoona zenizeni za Mboni za Yehova kapena chifukwa chakuti anamva nkhani zonama zokhudza ife. Mwina amachita zimenezi chifukwa cha zoipa zimene anthu ofalitsa nkhani amanena. M’madera ena, anthu amanena kuti ndife “gulu loopsa lampatuko.” Kodi tizitani tikakumana ndi anthu olankhula zoipa ngati zimenezi?
2. N’chiyani chingatithandize kusakhumudwa anthu akatinenera zoipa?
2 Musakhumudwe: Kawirikawiri anthu sankamvetsa ntchito ya Yesu ndi atumiki ena a Yehova m’nthawi za atumwi ndipo ankawanenera zoipa. (Mac. 28:22) Komabe, sanachite manyazi ndi utumiki wawo chifukwa cha zimenezi. Yesu anati: “Nzeru imatsimikizirika kukhala yolungama mwa ntchito zake.” (Mat. 11:18, 19) Iye anapitiriza kuchita chifuniro cha Atate wake mwakhama podziwa kuti anthu ofunafuna choonadi adzazindikira phindu la uthenga wabwino. Tingapewe kukhumudwa tikakumbukira kuti ngakhale Mwana wa Mulungu anakumananso ndi anthu omunenera zoipa.
3. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa anthu akamatinenera zoipa ndi kutitsutsa?
3 Yesu ananena kuti dziko lidzadana ndi otsatira ake monga mmene linadanirana naye. (Yoh. 15:18-20) Choncho anthu akamatinenera zoipa ndiponso kutitsutsa sitiyenera kudabwa. Koma tiyenera kuyembekezera kuti zinthu zimenezi zidzawonjezereka pamene mapeto akuyandikira ndiponso pamene mkwiyo wa Satana ukukulirakulira. (Chiv. 12:12) Zimenezi ndi zosangalatsa chifukwa ndi umboni wosonyeza kuti dziko la Satana latsala pang’ono kutha.
4. Kodi tizichita chiyani ngati munthu sanatilandire bwino tikafuna kumuuza uthenga wabwino?
4 Yankhani Mokoma Mtima: Ngati munthu sanatilandire bwino mu utumiki tiyenera kumuyankha mokoma mtima ndiponso mofatsa. (Miy. 15:1; Akol. 4:5, 6) Ngati zingatheke ndipo ngati munthuyo angalole, tingamufotokozere kuti anthu amalankhula zinthu zambirimbiri zonama zokhudza Mboni za Yehova. Mwinanso tingamufunse chifukwa chimene wanenera zimene wanenazo. Tikamulankhula mofatsa angayambe kuona kuti zimene wamva zokhudza Mboni za Yehova ndi zonama ndipo Mboni zikadzabweranso mwina angadzamvetsere uthenga wawo. Koma ngati mwininyumba wakwiya kwambiri, mwina ndi bwino kungomutsanzika mwaulemu n’kuchoka. Komabe, kaya anthu ena amationa bwanji, tikudziwa kuti Yehova amayamikira utumiki wathu.—Yes. 52:7.