Magazini Athu Amakonzedwa Kuti Azifika Pamtima Anthu Onse
1. Kodi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amatsanzira bwanji mtumwi Paulo?
1 Mtumwi Paulo ankasinthasintha njira zolalikirira uthenga wabwino kuti athandize “anthu osiyanasiyana.” Masiku anonso kapolo wokhulupirika ndi wanzeru akugwiritsa ntchito magazini athu kuti alalikire uthenga wabwino kwa anthu azikhalidwe ndiponso zikhulupiriro zosiyanasiyana. (1 Akor. 9:22, 23) Kuti tizigwiritsa ntchito bwino magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, ndi bwino kudziwa anthu amene amawalembera magaziniwa.
2. Kodi Galamukani! imakonzedwa kuti izifika pamtima anthu ati?
2 Galamukani!: Magaziniyi cholinga chake ndi kuthandiza anthu ofanana ndi amene mtumwi Paulo analankhula nawo ku Atene. (Mac. 17:22) Anthu amenewa sankadziwa zambiri za Chikhristu ndipo ankadziwa zinthu zochepa za m’Malemba. N’chimodzimodzi ndi anthu amene amawaganizira pokonza magazini ya Galamukani! Magaziniyi amakonzera anthu amene sadziwa zambiri kapena sadziwa n’komwe za Baibulo. Angakhale anthu amene sadziwa kalikonse kokhudza ziphunzitso zachikhristu, amene amakayikira za chipembedzo kapena amene sadziwanso kuti Baibulo ndi lothandiza. Cholinga chachikulu cha Galamukani! ndi kutsimikizira owerenga kuti Mulungu woona alipo. Cholinga chinanso cha magaziniyi ndi kuthandiza anthu kuti azikhulupirira Baibulo ndiponso kuwathandiza kumvetsa kuti Mboni za Yehova n’zosiyana ndi magulu ena azipembedzo.
3. Kodi magazini ya Nsanja ya Olonda yogawira ndiponso yophunzira, amalembera ndani?
3 Nsanja ya Olonda: Magazini yogawira amaikonzera anthu amene amalemekeza Mulungu ndiponso Malemba. Anthu amenewa amadziwako za Baibulo koma samvetsa molondola zimene Baibulo limaphunzitsa. Iwo ndi ofanana ndi anthu amene Paulo anawatchula kuti ndi “oopa Mulungu.” (Mac. 13:14-16) Magazini yophunzira ya Nsanja ya Olonda, kwenikweni amakonzera Mboni za Yehova. Paulo ankaona kuti amene ankawerenga makalata ake anali anthu omwe ankadziwa Malemba ndiponso choonadi molondola. (1 Akor. 1:1, 2) N’chimodzimodzinso ndi nkhani za m’magazini yophunzira. Nkhanizi amalembera anthu amene amapezeka pamisonkhano ya mpingo, amene amadziwa zimene Mboni zimaphunzitsa komanso mawu amene zimagwiritsa ntchito.
4. N’chifukwa chiyani tiyenera kudziwa bwino magazini iliyonse imene tikugawira mu utumiki?
4 Ngakhale kuti timagawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! nthawi imodzi, nthawi zambiri timafotokoza magazini imodzi pamene tikugawira. Choncho, khalani ndi cholinga chodziwa bwino magazini iliyonse. Mukatero, pogawira magaziniwa mudzatha kufotokoza bwino magazini imene mukuona kuti ingakhale yogwirizana ndi anthu amene mwakumana nawo.