Zifukwa 12 Zimene Zimatichititsa Kulalikira
N’chifukwa chiyani timalalikira ndiponso kuphunzitsa anthu uthenga wabwino? Kodi timalalikira ndiponso kuphunzitsa anthu amaganizo abwino kuti adzapeze moyo wosatha? (Mat. 7:14) Chimenechi si chifukwa chachikulu chimene timalalikirira ndi kuphunzitsa anthu. Pa zifukwa 12 zimene zaikidwa pansipa, kodi mukuganiza kuti chifukwa chachikulu chimene timalalikira ndi chiti?
1. Ntchito yolalikirayi imathandiza anthu kuti adzapulumuke.—Yoh. 17:3.
2. Uthenga wathu umachenjeza anthu oipa.—Ezek. 3:18, 19.
3. Ntchito yolalikirayi imakwaniritsa zimene zinaloseredwa m’Baibulo.—Mat. 24:14.
4. Kulalikira ndiponso kuphunzitsa anthu Baibulo ndi njira yosonyezera kuti Mulungu ndi wolungama. Palibe munthu amene anganene kuti Yehova adzawononga anthu oipa asanawapatse mwayi wolapa.—Mac. 17:30, 31; 1 Tim. 2:3, 4.
5. Tikamalalikira timakwaniritsa udindo wathu wothandiza anthu amene anagulidwa ndi magazi a Yesu kuti adziwe za Mulungu.—Aroma 1:14, 15.
6. Ntchitoyi imatipangitsa kuti tisakhale ndi mlandu wa magazi.—Mac. 20:26, 27.
7. Kuti tikapulumuke zikudalira kugwira nawo ntchito imeneyi.—Ezek. 3:19; Aroma 10:9, 10.
8. Zimasonyeza kuti timakonda anzathu.—Mat. 22:39.
9. Timasonyeza kuti timatsatira zimene Yehova ndiponso Mwana wake anatilamulira.—Mat. 28:19, 20.
10. Kulalikira n’kofunika kwambiri pa kulambira kwathu.—Aheb. 13:15.
11. Kugwira nawo ntchitoyi kumasonyeza kuti timakonda Mulungu.—1 Yoh. 5:3.
12. Ntchito imeneyi imachititsa kuti dzina la Yehova lilemekezedwe.—Yes. 43:10-12; Mat. 6:9.
Komabe, zimenezi si zifukwa zokhazo zimene timalalikirira. Mwachitsanzo, kulalikira kumalimbikitsa chikhulupiriro chathu. Komanso timakhala antchito anzake a Mulungu. (1 Akor. 3:9) Komabe, chifukwa chachikulu chimene timalalikirira ndi chimene chikupezeka pa nambala 12. Kaya anthu amvetsere kapena ayi, utumiki wathu umalemekeza dzina la Mulungu ndiponso umapangitsa kuti Yehova amuyankhe amene amamutonza. (Miy. 27:11) Tili ndi zifukwa zabwino zotipangitsa kuti tipitirize kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino mwakhama.—Mac. 5:42.