Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/15 tsamba 6-7
  • Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo wa 2015

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo wa 2015
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Nkhani Yofanana
  • “Khalani Ndi Khalidwe Labwino Pakati pa Anthu a M’dzikoli”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Khalidwe Lathu Labwino Limalemekeza Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Masiku Atatu Otsitsimulidwa Mwauzimu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Misonkhano Yathu Yachigawo Imafotokoza Mfundo za Choonadi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
km 6/15 tsamba 6-7

Zofunika Kukumbukira pa Msonkhano Wachigawo wa 2015

  • Nthawi ya Msonkhano: Masiku onse atatu, msonkhano uzidzayamba ndi nyimbo zomvetsera pa nthawi ya 8:20 m’mawa. Tonse tiyenera kudzakhala pansi pa nthawi imeneyi kuti msonkhano uyambe bwinobwino. Lachisanu ndi Loweruka msonkhano udzatha 3:55 madzulo, ndipo Lamlungu udzatha nthawi ya 2:45 chakumadzulo.

  • ‘Tamandani Yehova Pomuimbira Nyimbo’: Anthu akale ankaimba nyimbo pofuna kutamanda Yehova. Masiku anonso kuimba nyimbo n’kofunika kwambiri pa kulambira kwathu. (Sal. 28:7) Chigawo chilichonse cha msonkhano wachigawo chimayamba ndi nyimbo zomvetsera. Cholinga cha nyimbozi si kungotisangalatsa koma ndi kutikonzekeretsa maganizo kuti tiphunzire za Yehova komanso kumulambira. Choncho, tcheyamani akanena kuti nyimbo zomvetsera zikuyamba, tiyenera kukhala pansi n’kumamvetsera nyimbozo. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timayamikira khama lomwe abale ndi alongo omwe amakonza nyimbozi anasonyeza. Abale amenewa amapita ku Patterson mumzinda wa New York, kawiri pachaka, kuti akaimbe nyimbozi n’cholinga choti tidzamvetsere pamsonkhano. Nyimbozi zikatha, tonse tiyenera kutamanda Yehova poimba nyimbo yoyambira chigawocho.

  • Koimika Magalimoto: Malo onse ochitira msonkhano adzakhala ndi malo okwanira oimikako magalimoto ndi njinga. Tikukulimbikitsani kudzamvera zimene akalinde amene aikidwa kusamalira utumiki umenewu angakuuzeni. Eniake a magalimoto adzaonetsetse kuti zitseko za magalimoto ndi zokhoma. Nawonso eniake a njinga adzaonetsetse kuti njinga zawo n’zokhoma, asanakakhale pansi.

  • Kusungirana Malo: Si bwino kukankhanakankhana pamalo a msonkhano n’cholinga choti tikapeze malo abwino. Chikondi chimatichititsa kuti tiziganiziranso ena, ndipo izi zimasonyeza kuti ndife Akhristu oona komanso zimathandiza anthu ena kutamanda Mulungu. (Yoh. 13:34, 35; 1 Akor. 13:4, 5; 1 Pet. 2:12) Tingasungire malo anthu okhawo amene tabwera nawo pa galimoto imodzi, amene timakhala nawo nyumba imodzi kapena amene tikuphunzira nawo Baibulo. Musaike zinthu pamalo omwe simunasungire munthu. Zimenezi zingachititse kuti anthu ena aziganiza kuti pamalowo pali munthu. Padzakonzedwa malo okhala anthu okalamba, odwala ndi olumala. Popeza malo amenewa adzakhala ochepa, munthu mmodzi kapena awiri ndi amene ayenera kukhala ndi anthuwa, ngati pakufunika woti aziwasamalira.

  • Valani Modzilemekeza: Tikamapita kumsonkhano tiyenera kuvala moyenera ndi modzilemekeza, osati motengera masitayilo a m’dzikoli. (1 Tim. 2:9) Ngakhale pamene tili kuhotelo kapena pamene tikupuma pambuyo pa pulogalamu ya tsikulo, sitiyenera kuvala motayirira kapena kuvala zovala zolemba mawu osakhala bwino. Kuvala moyenera kudzachititsa kuti tisadzachite manyazi kuvala mabaji a msonkhano komanso kulalikira mwamwayi. Kuvala bwino ndiponso khalidwe lathu labwino pamene tili kumsonkhano, zidzathandiza kuti anthu a mitima yabwino amvetsere uthenga wa m’Baibulo komanso kuti alemekeze Yehova.—Zef. 3:17.

  • Muzidzagwiritsa Ntchito Zipangizo Zamakono Moyenera: Pa nthawi ya msonkhano, tiyenera kutchera foni kapena zipangizo zina moti zisasokoneze ena. Ngati mudzagwiritse ntchito kamera, tabuleti kapena zipangizo zina pojambula zithunzi komanso vidiyo, dzaonetsetseni kuti simukusokoneza komanso kutchingira ena. Tingadzasonyezenso khalidwe labwino ngati titadzapewa kulemba mameseji kapena maimelo msonkhano uli mkati.

  • Tikukulimbikitsani kuti mudzabwere ndi chakudya chamasana, m’malo mochoka pamalo a msonkhano kukagula chakudya pa nthawi yopuma. Mungatenge zakudya monga tchipisi, mpunga, mbatata, chinangwa ndi zakumwa. Koma mowa si wololedwa pamalo a msonkhano.

  • Tingasonyeze kuyamikira ntchito yomwe inagwiridwa pokonzekera msonkhanowu, popereka mwa kufuna kwathu ndalama zothandiza ntchito ya padziko lonse. Polemba cheke, sonyezani kuti ndalamazo zikupita ku, “Association of Jehovah’s Witnesses of Malawi.”

  • Ngati mumamwa mankhwala enaake, muyenera kuonetsetsa kuti mwatenga okwanira chifukwa mankhwala amenewo sadzapezeka pa msonkhano. Anthu amene amadzibaya mankhwala a matenda a shuga ayenera kusamala mmene angatayire majakisoni. Sayenera kutaya m’mabini a pamalo a msonkhano kapenanso kungotaya pamene kumene akugona.

  • Chonde yesetsani kupewa zinthu zimene zingachititse ngozi. Chaka chilichonse kumachitika ngozi ndipo zambiri za ngozi zimenezi zimachitika chifukwa chovala nsapato zazitali. Choncho, ndi bwino kuvala nsapato zimene mungathe kuyenda nazo bwinobwino.

  • Nkhani za msonkhanowu zizidzamasuliridwa m’chinenero chamanja m’malo otsatirawa: Blantyre, Kasungu, Lilongwe, Luchenza, Magawa, Mkanda, Mangochi, Mzuzu, Mnadzi, Nchalo, Nkhata Bay, Songani ndi malo enanso. Pa tsiku loyamba la msonkhanowu padzakhala chilengezo chonena za zimenezi.

  • Zikuku ndi Njinga za Ana: Simukuloledwa kubweretsa zinthu zimenezi pamalo a msonkhano.

  • Perefyumu: Poganizira anthu amene, chifukwa cha mavuto ena, amadana ndi fungo lamphamvu, ndi bwino kusagwiritsa ntchito perefyumu wamphamvu kwambiri.—1 Akor. 10:24.

  • Mafomu a Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43): Pofotokoza za munthu aliyense amene anaonetsa chidwi mutamulalikira mwamwayi pa nthawi ya msonkhano, muzigwiritsa ntchito mafomu a S-43. Mungapereke mafomu osainidwa bwinobwino ku Dipatimenti ya Mabuku kapena kwa mlembi wa mpingo wanu mukabwera ku msonkhanowo.

  • M’malesitilanti: Mukapita kulesitilanti muyenera kusonyeza khalidwe labwino chifukwa zimenezi zimalemekeza Yehova. Tiyenera kuvala zovala zoyenera Mkhristu.

  • Utumiki Wodzipereka: Ngati mukufuna kudzachita nawo utumikiwu, mudzaonane ndi abale a ku Dipatimenti ya Antchito Odzipereka. Ana azaka 16 angathenso kuchita nawo utumikiwu moyang’aniridwa ndi makolo awo kapena munthu wina wachikulire wovomerezedwa ndi makolowo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena