Fotokozani Nkhani Imodzi, Koma Asiyireni Magazini Awiri
M’magazini athu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! mumakhala nkhani zosiyanasiyana zomwe anthu ambiri amazikonda. Koma m’malo mofotokozera munthu nkhani zingapo, tingachite bwino kungomufotokozera nkhani imodzi. Ngati timachita chidwi ndi anthu amene tikuwalalikira komanso ngati timakonzekera bwino nkhani zomwe zili m’magazini athu, tingathe kudziwa nkhani mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! imene mwininyumba angachite nayo chidwi. Mwachitsanzo, ngati tafika pakhomo lina ndipo taona zidole za ana, tingathe kukambirana ndi mwininyumba nkhani yokhudza kulera bwino ana. Ngati tapeza abambo, tikhoza kukambirana nawo nkhani zimene amuna ambiri amachita nazo chidwi, monga zokhudza ulamuliro wabwino. Ngakhale kuti tingakambirane nkhani imodzi ndi mwininyumba, ngati ali wachidwi tingamusiyire magazini onse awiri, Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!