Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/13 tsamba 1
  • Kodi Tingakonzekere Bwanji Mawu Oyamba Okopa Chidwi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tingakonzekere Bwanji Mawu Oyamba Okopa Chidwi?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Mawu Oyamba Ogwira Mtima
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzikonzekera Mawu Oyamba
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 12/13 tsamba 1

Kodi Tingakonzekere Bwanji Mawu Oyamba Okopa Chidwi?

1. Kodi kuyamba ndi mawu akopa chidwi n’kofunika bwanji?

1 Kafungo koutsa mudyo ka chakudya chophikidwa bwino kamapangitsa munthu kufuna kudya chakudyacho. N’chimodzimodzinso ndi mawu oyamba okopa chidwi. Munthu akhoza kuyamba kufuna kuti tikambirane naye mfundo za m’Malemba ngati talankhula mawu oyamba okopa chidwi. Mawuwa akhoza kukhala aafupi mosiyanasiyana komanso zimene tinganene sizingakhale zofanana nthawi zonse. Komabe mofanana ndi chakudya chokoma mmene chimakonzedwera, mawu oyamba nawonso ayenera kukonzekeredwa bwino pasadakhale. (Miy. 15:28) Kodi tingatani kuti mawu athu oyamba azikhala okopa chidwi?

2. Kodi mungakonzekere bwanji mawu oyamba okopa chidwi?

2 Muzisankha Nkhani Zimene Anthu Angachite Nazo Chidwi: Mawu athu oyamba ayenera kukhala okopa chidwi chifukwa kupanda kutero munthu amene tikumulalikirayo akhoza kutiuza kuti sakufuna kuti tikambirane naye. Choncho mukamakonzekera, ganizirani nkhani zimene anthu a m’dera lanu angachite nazo chidwi. Kodi amachita chidwi ndi nkhani zokhudza ulamuliro wabwino, nkhondo kapena zimene anthu angachite kuti akhale ndi banja losangalala? Nthawi zambiri anthu amakonda kunena maganizo awo pa nkhani inayake, choncho ganizirani za funso lomwe mungawafunse. Mwinanso mungagwiritse ntchito zitsanzo za ulaliki zopezeka mu Utumiki Wathu wa Ufumu ndipo mungazisinthe mwina ndi mwina kuti zigwirizane ndi anthu a m’dera lanu. Nthawi zina mungamayeserere ena a maulaliki amenewa pa Kulambira kwa Pabanja.

3. Kodi tingatani kuti mawu athu oyamba akhale ogwirizana ndi chikhalidwe komanso chipembedzo cha anthu a m’dera lathu?

3 Ganizirani za Chikhalidwe ndi Chipembedzo Chawo: M’madera ena, mukangofika pakhomo la munthu, mumafunika kunena chimene mwabwerera. Koma m’madera ena amaona kuti ndi kupanda ulemu ngati munthu angofikira kunena chimene wabwerera, asanapereke moni komanso kufunsa zina ndi zina zokhudza moyo wa anthu a pakhomopo. Pamene m’madera ena, zimakhala zosavuta kuyamba kukambirana ndi munthu pogwiritsa ntchito Baibulo ngati munthuyo ali kale m’chipembedzo chachikhristu. (Mac. 2:14-17) Koma ngati munthuyo sali m’chipembedzo chachikhristu kapena alibe n’komwe chipembedzo, ndi bwino kuyamba kutchula Baibulo pa ulendo wobwereza osati woyamba.—Mac. 17:22-31.

4. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikamanena mawu oyamba?

4 Mawu Oyamba: Muziyesetsa kukonzekera bwino mawu oyamba. Mawu aafupi komanso osavuta kumva ndi amene nthawi zambiri amakhala abwino. Chinthu china chofunika kwambiri ndi mmene timalankhulira mawu oyambawo. Muzilankhula mwansangala komanso muzimwetulira mwaubwenzi ndipo zimenezi zingasonyeze kuti muli ndi chidwi ndi munthuyo. Kutsatira malangizo amene ali m’nkhaniyi kungatithandize kuti tizikonzekera mawu oyamba okopa amene angapangitse anthu a m’dera lathu kukhala ndi chidwi chofuna kudya “patebulo la Yehova.”—1 Akor. 10:21.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena