MUTU WA MWEZI UNO: “Lalikira mawu. Lalikira modzipereka.”—2 TIM. 4:2.
Muzigwiritsa Ntchito Mpata Uliwonse Kulalikira Uthenga wa Ufumu
1. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Davide anachita?
1 Mfumu Davide analephera kuchita zinthu zina chifukwa cha mmene zinthu zinalili pa moyo wake. Koma zimenezi sizinachititse kuti angokhala osachita chilichonse. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Davide ankafuna kumanga nyumba ya Yehova. Koma Yehova sanamulole kuchita zimenezi. Zitatere, Davide sanangosiya osachita chilichonse. M’malomwake anapereka zinthu zoti zidzathandize Solomo kumanga nyumbayo. (1 Maf. 8:17-19; 1 Mbiri 29:3-9) Choncho, m’malo momangoganizira zomwe sakanatha kuchita, Davide anaganizira zomwe akanatha kuchita ndipo anachita zimenezo. Kodi chitsanzo cha Davide chingatithandize bwanji pa ntchito yolalikira?
2. Kodi mungatani kuti mudziwe ngati mungakwanitse kuchita upainiya?
2 Muzichita Zimene Mungakwanitse: Abale ndi alongo ambiri asintha zinthu zina pa moyo wawo n’cholinga choti akhale apainiya othandiza kapena okhazikika. (Mat. 6:22) Kodi inunso mungakwanitse kuchita zimenezi? Mutaganizira mofatsa nkhaniyi komanso kupemphera, mwina mungaone kuti “khomo lalikulu la mwayi wautumiki” lakutsegukirani. Mukaona kuti n’zotheka, musalole kuphonya mwayi umenewu.—1 Akor. 16:8, 9.
3. Kodi tingagwiritse ntchito mipata iti ngati sitingathe kuchita upainiya chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wathu?
3 Koma kodi mungatani ngati simungakwanitse kuchita upainiya chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wanu? Ganizirani zinthu zina zimene mungakwanitse kuchita. Mwachitsanzo, ngati mumagwira ntchito, mukhoza kumalalikira anthu amene mumagwira nawo ntchito. Ngati mukudwala matenda enaake, ndipo mumapitapita kuchipatala, mungathe kumalalikira anthu ogwira ntchito kuchipatalako. Musaiwalenso kuti anthu omwe sangathe kuchita zambiri mu utumiki chifukwa cha matenda kapena chifukwa choti ndi okalamba, akhoza kumapereka mphindi 15 pa mwezi. Mukamalemba malipoti anu, musamaiwale kuphatikizapo nthawi yomwe munalalikira mwamwayi komanso zilizonse zimene munagawira, kuphatikizapo timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso kapena kumsonkhano. Mungadabwe kuona kuti nthawi yomwe munalalikira mwamwayi ndi yambiri ndithu.
4. Kodi inuyo mukufunitsitsa kuchita chiyani?
4 Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wanu, muziyesetsa kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kukhala wosangalala chifukwa chodziwa kuti mukuchita zonse zimene mungathe kuti muzilalikira za Ufumu.—Maliko 14:8; Luka 21:2-4.