“Ndikapita Sindiwapeza”
Kodi munayamba mwanenapo mawu amenewa ponena za munthu wina yemwe anaonetsa kuti ali ndi chidwi? Kusapezanso munthu wotereyu kungapangitse kuti mulephere kuthirira mbewu za choonadi zomwe munadzala. (1 Akor. 3:6) Ofalitsa ena akapita kangapo kunyumba ya munthu wachidwi amene anacheza naye koma osam’peza, amalemba kakalata n’kumusiyira panyumba yake kapena amakalemba kalata n’kumutumizira. Ofalitsa ena akaona kuti mwina sadzam’pezanso munthuyo pakhomo, amamupempha nambala ya foni yake n’kumufunsa kuti, “Ndingadzakulembereni meseji?” Tingawerengere ulendo wobwereza ngati talalikira munthu pogwiritsa ntchito kalata, imelo, meseji kapena kumuimbira foni. Njira zimenezi zingathandize kuti tipitirizebe kukambirana ndi munthu wachidwi ngakhale kuti sakupezeka pakhomo.