Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb20 November tsamba 7
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​— Kulalikira Pogwiritsa Ntchito Foni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​— Kulalikira Pogwiritsa Ntchito Foni
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzisiya Funso Loti Mudzakambirane pa Ulendo Wotsatira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • “Ndikapita Sindiwapeza”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Yesetsani Kudziwa Bwino Webusaiti Yathu ya JW.ORG
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Kugwiritsa Ntchito Autilaini
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20 November tsamba 7
M’bale wachinyamata akuchita ulaliki wapafoni ndi banja lachikulire. 1. M’bale akulankhula ndi munthu wabizinezi pafoni 2. Munthu wabizinezi akumvetsera uthenga umene m’baleyo akumulalikira.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu Mu Utumiki​-Kulalikira Pogwiritsa Ntchito Foni

KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Kulalikira pogwiritsa ntchito foni ndi njira yofunika pochitira “umboni mokwanira za uthenga wabwino.” (Mac 20:24)a Imatithandiza kulalikira kwa munthu pamene zingakhale zovuta kumulalikira pamasom’pamaso.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • M’bale yemwe uja akukonzekera ulaliki wapafoni poona malemba amene angagwiritse ntchito ndipo akulemba notsi zachidule.

    Tizikonzekera. Tizisankha nkhani yoyenera. Kenako tizilemba autilaini ya zimene tikufuna kunena. Mwina mungalembenso kauthenga kakafupi kamene munganene ngati munthu sanayankhe foni koma foniyo ikulola kuti musiye uthenga. Zimathandiza kukhala patebulo muli ndi autilaini ndi zinthu zina zofunika pafupi monga chipangizo chomwe mwatsegula JW Library® kapena jw.org®

  • M’bale wachinyamata akuthandiza m’bale wachikulire amene akulankhula ndi munthu wina pafoni.

    Tizikhala omasuka. Tizilankhula mwachibadwa, kumwetulira ndiponso kugwiritsa ntchito manja ngati kuti tikulankhula ndi munthu pamasom’pamaso. Tizipewanso kuimaima polankhula. Komanso zimathandiza kuchita utumikiwu ndi anthu ena. Mwininyumba akafunsa mafunso, tizibwereza mokweza mafunsowo kuti mnzathu azitithandiza kupeza mayankho

  • M’bale wachinyamata akutumiza linki ya vidiyo ya pa jw.org

    Tizisiya funso loti tidzayankhe pa ulendo wobwereza. Munthu akasonyeza chidwi tingamusiyire funso loti tidzayankhe tikadzaimbanso. Tinganenenso kuti tikhoza kukamusiyira buku kapena magazini, kutumiza pa imelo kapena m’njira ina. Apo ayi, tinganene kuti tikhoza kumutumizira vidiyo kapena nkhani inayake pa foni kapena pogwiritsa ntchito chipangizo china. Ngati n’zotheka, tingamuuze zinthu zina zimene angapeze pawebusaiti yathu.

a Ngati n’zololeka kulalikira pogwiritsa ntchito foni m’dera lanu, muzitsatira malamulo okhudza kusunga chinsinsi cha anthu ena.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena