Muzidzipereka Polimbikitsa Ena Kuchita Zabwino
Lemba la Aheberi 10:24 limatiuza kuti, “tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino.” Abale ndi alongo athu angalimbikitsidwe akaona chitsanzo chathu chabwino komanso zinthu zosonyeza chikhulupiriro zimene timachita. Choncho, muziuza ena zinthu zolimbikitsa zomwe mwakumana nazo. Athandizeni kuona kuti mukusangalala kwambiri kutumikira Yehova. Koma mukamachita zimenezi, pewani kuwayerekezera ndi ena kapena ndi inuyo. (Agal. 6:4) Cholinga chanu chikhale kuwalimbikitsa pa “chikondi ndi ntchito zabwino,” osati kuwachititsa kuti azidziimba mlandu. (Onani buku la Sukulu ya Utumiki tsamba 158, ndime 4.) Tikamakondana, zingakhale zosavuta kuti tizithandizana komanso kuti tizigwira bwino ntchito yolalikira.—2 Akor. 1:24.