Ndandanda ya Mlungu wa March 2
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 2
Nyimbo Na. 5 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 9 ndime 8-20 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Rute 1-4 (Mph. 8)
Na. 1: Rute 3:14-18 ndi 4:1-6 (Osapitirira mph. 3)
Na. 2: Tsanzirani Mtumwi Paulo Potumikira Mulungu—bt tsa. 63-64 ndime 13-15 (Mph. 5)
Na. 3: Mfumu Khristu ndi Wodzichepetsa ndiponso Wamphamvu—igw tsa. 8 ndime 5–tsa. 9 ndime 4 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: Khalani “Odzipereka pa Ntchito Zabwino”—Tito 2:14.
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini a March. Nkhani yokambirana. Yambani ndi kuchita chitsanzo cha mmene tingagawirire magaziniwa pogwiritsa ntchito zitsanzo za ulaliki zimene zili patsamba lino. Limbikitsani ofalitsa onse kuti awerenge magaziniwa n’cholinga choti awadziwe bwino.
Mph. 10: “Muzidzipereka Polimbikitsa Ena Kuchita Zabwino.” Nkhani yokambirana. Fotokozani kuti mfundo ya mutu wa mwezi wa February taikambirana kwambiri m’nkhani zosiyanasiyana za utumiki.
Mph. 10: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene anapindulira pogwiritsa ntchito malangizo a m’nkhani yakuti, “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Kulalikira Pogwiritsa Ntchito Intakomu Kapena M’madera a Chitetezo Chokhwima.” Ngati n’zotheka kudera lanu, funsani omvera kuti afotokoze zimene anachita kuti alalikire kwa munthu pogwiritsa ntchito intakomu.
Nyimbo yatsopano yakuti: “Inu Ndinu Yehova” ndi Pemphero
Kumbukirani kuti, muyenera kuika nyimboyi kuti onse aimvetsere kenako muibwerezenso kuti onse aimbe nawo nyimboyi. Ngati simungathe kuchita dawunilodi nyimboyi pa webusaiti yathu, mungaimbe nyimbo nambala 46.