Muzilengeza za Mphamvu ya Mawu a Mulungu mu Utumiki
Ngati munthu wavomera kuti timuuze uthenga wabwino, tiyenera kugwiritsa ntchito mpata umenewo kulengeza za mphamvu ya Mawu a Mulungu. Tingachite zimenezi powerenga naye Baibulo. Mfundo imeneyi inafotokozedwa bwino pa msonkhano wadera wa chaka chatha. Woyang’anira dera anakamba nkhani ya mutu wakuti, “Muzilengeza za Mphamvu ya Mawu a Mulungu mu Utumiki.” Kodi mukukumbukira mfundo zomwe zinakambidwa m’nkhaniyi?
N’chifukwa chiyani Mawu a Yehova ndi amphamvu kwambiri kuposa mawu athu?—2 Tim. 3:16, 17.
Kodi Mawu a Mulungu amathandiza bwanji anthu kusintha mmene amaganizira, zolinga zawo, zimene amakhulupirira ndiponso khalidwe lawo?—Onani Nsanja ya Olonda ya June 15, 2012, tsamba 27 ndime 7.
Tikawerenga Baibulo ndi munthu mu utumiki, kodi tingamuthandize bwanji kuti aziona kuti Mawu a Mulungu ndi othandiza kwambiri?—Onani buku la Sukulu ya Utumiki tsamba 148 ndime 3-4 komanso Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2013, tsamba 6 ndime 8.
N’chifukwa chiyani n’zofunika kuti tizifotokoza komanso kukambirana ndi munthu malemba amene tawerenga ndipo tingachite bwanji zimenezi?—Mac. 17:2, 3; onaninso buku la Sukulu ya Utumiki tsamba 154 ndime 4 mpaka tsamba 156 ndime 5.