“Mawu Awa . . . Azikhala Pamtima Pako”
Makolo ali ngati abusa. Ali ndi udindo wosamalira bwino ana awo chifukwa anawo akhoza kusochera n’kugwidwa mosavuta. (Miy. 27:23) Koma kodi makolo angasamalire bwanji ana awo? Ayenera kupeza nthawi yambiri yocheza nawo kuti adziwe zimene zili mumtima mwa anawo. (Miy. 20:5) Kenako ayenera kumanga ndi zomangira zosagwira moto n’cholinga choti alimbitse chikhulupiriro cha ana awowo. (1 Akor. 3:10-15) Vidiyo yakuti, “Mawu Awa . . . Azikhala Pamtima Pako” imasonyeza kufunika kochita kulambira kwa pabanja nthawi zonse. Choncho tikukulimbikitsani kuti muonere vidiyoyi, limodzi ndi banja lanu kenako n’kukambirana mafunso otsatirawa:
(1) Kodi n’chiyani chinachititsa kuti banja la a Roman lisamakonde zinthu zauzimu? (2) N’chifukwa chiyani njira imene M’bale Roman anatsatira poyamba sinathandize kuti banja lake lizichita kulambira kwa pabanja nthawi zonse? (3) Kodi ndi njira ya m’Malemba iti yomwe makolo akaitsatira imathandiza kuti alere bwino ana awo? (Deut. 6:6, 7) (4) N’chiyani chingathandize kuti anthu azilankhulana bwino m’banja? (5) Kodi ana amafuna kuti makolo awo azichita chiyani? (6) Kodi M’bale ndi Mlongo Barrow anathandiza bwanji banja la a Roman? (Miy. 27:17) (7) Kodi mwamuna ayenera kukonzekereratu zinthu ziti kuti kulambira kwa pabanja kukhale kothandiza? (8) Kodi M’bale Roman anatani kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino m’banja lake? (9) N’chifukwa chiyani kuchita kulambira kwa pabanja mlungu uliwonse pa nthawi imene tinagwirizana n’kofunika? (Aef. 6:4) (10) Fotokozani zinthu zimene zingachititse kuti kulambira kwa pabanja kuzikhala kothandiza. (11) Kodi M’bale Roman anachita bwanji zinthu moleza mtima koma mwamphamvu, pofuna kuthandiza Marcus kuti adziwe kufunika kochita zinthu zabwino? (Yer. 17:9) (12) Kodi M’bale ndi Mlongo Roman anakambirana mfundo zotani ndi Rabecca pofuna kumuthandiza kuti asankhe bwino zinthu pa nkhani yochita chibwenzi ndi Justin? (Maliko 12:30; 2 Tim. 2:22) (13) Kodi M’bale ndi Mlongo Roman anasintha zinthu ziti pa moyo wawo, zomwe zikusonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova? (Mat. 6:33) (14) Kodi vidiyoyi ikusonyeza bwanji kufunika koti amuna azitsogolera mabanja awo pa zinthu zauzimu? (1 Tim. 5:8) (15) Inuyo monga makolo, mwatsimikiza mtima kuchita chiyani?
MAWU KWA MAKOLO: Vidiyoyi yachokera pa sewero lomwe tinaonera pamsonkhano wachigawo wa 2011. Pa nthawi imeneyo, kodi munaona zinthu zina zomwe munafunika kusintha zokhudza kulambira kwanu kwa pabanja? Kodi panopo pali zimene muyenera kusintha? Ngati pakufunika kusintha zinthu zina, mungachite bwino kuipempherera nkhaniyi chifukwa zingathandize kuti banja lanu lidzapeze moyo wosatha.—Aef. 5:15-17.