Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb16 April tsamba 8
  • Ntchito Yoitanira Anthu Kumsonkhano Wachigawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ntchito Yoitanira Anthu Kumsonkhano Wachigawo
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MFUNDO ZOFUNIKA KUZIKUMBUKIRA
  • ZIMENE MUNGANENE
  • TIDZATHANDIZE ANTHU ACHIDWI
  • Ntchito Yoitanira Anthu ku Msonkhano Wachigawo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Msonkhano
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Ntchito Imene Imakhala ndi Zotsatira Zabwino
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa March 17
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
mwb16 April tsamba 8

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Ntchito Yoitanira Anthu Kumsonkhano Wachigawo

Wa Mboni za Yehova waima pafupi ndi kashelefu kamatayala ndipo akulalikira

Chaka chilichonse timayembekezera mwachidwi phwando la chakudya chauzimu lomwe timasangalala nalo pamisonkhano yachigawo. Pofuna kuti anthu enanso adzalawe ubwino wa Yehova, tidzayesetsa kuitanira anthu ambiri kumsonkhano wachigawo. (Sal. 34:8) M’mipingo yonse, mabungwe a akulu adzasankha njira yabwino yomwe mpingo wawo ungatsatire pogawira timapepalati.

MFUNDO ZOFUNIKA KUZIKUMBUKIRA

  • Kodi msonkhano wathu udzachitika liti?

  • Kodi mpingo wathu udzayamba liti ntchito yoitanira anthu kumsonkhano?

  • Kodi ndi masiku ati amene mpingo wathu uzidzachita misonkhano yokonzekera ntchito yoitanira anthu kumsonkhano?

  • Kodi ndikufuna kudzakwaniritsa zolinga ziti pa ntchito yoitanira anthuyi?

  • Kodi ndi anthu ati omwe ndikufuna kudzawaitana?

ZIMENE MUNGANENE

Kapepala Koitanira anthu kumsonkhano wachigawo wa 2016

Pambuyo popereka moni munganene kuti:

“Tikugwira ntchito yomwe ikuchitika padziko lonse yoitanira anthu kumsonkhano wofunika kwambiri. Pakapepalaka talembapo nthawi ndi malo omwe msonkhanowu udzachitikire. Tidzasangalala kwambiri kukhala nanu pamsonkhanowu.”

TIDZATHANDIZE ANTHU ACHIDWI

Magazini ya Galamukani!, Na. 2 2016 | Kodi Baibulo Langokhala Buku Labwino Basi?

Ngakhale kuti tikufunitsitsa kudzaitanira anthu ambiri kumsonkhanowu, tikufunika kudzathandiza anthu omwe asonyeza chidwi kuti aphunzire zambiri.

Kumapeto kwa mlungu, tingadzagawire kapepalaka limodzi ndi magazini.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena