CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 34-37
Khulupirira Yehova Ndipo Chita Zabwino
“Usapse mtima chifukwa cha anthu ochita zoipa”
Musasiye kutumikira Yehova poona kuti anthu oipa zinthu zikuwayendera bwino. M’malo mwake, muziganizira zimene mungachite potumikira Yehova komanso madalitso amene Iye adzakupatseni
“Khulupirira Yehova ndipo chita zabwino”
Muzikhulupirira kuti Yehova angakuthandizeni kuthana ndi mavuto ndiponso nkhawa zanu. Komanso angakuthandizeni kukhalabe okhulupirika
Muzigwira mwakhama ntchito yolengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu
“Sangalala mwa Yehova”
Muzikhala ndi nthawi yowerenga Baibulo ndiponso kusinkhasinkha n’cholinga choti mumudziwe bwino Yehova
“Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako”
Muzikhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova angakuthandizeni kuthana ndi vuto lina lililonse
Muzisonyezabe khalidwe labwino anthu akamakutsutsani, kukuzunzani komanso kukunenerani zinthu zabodza
“Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umuyembekezere ndi mtima wako wonse”
Muzipewa kuchita zinthu mopupuluma chifukwa zingachititse kuti musamasangalale komanso zingasokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova
“Ofatsa adzalandira dziko lapansi”
Yesetsani kukhala ofatsa ndi kuyembekezera Yehova modzichepetsa kuti adzachotse zosalungama zonse zomwe zikukuchitikirani
Muzithandiza Akhristu anzanu komanso kulimbikitsa amene ali ndi nkhawa powakumbutsa kuti dziko latsopano lili pafupi kwambiri
Ufumu wa Mesiya udzabweretsa madalitso osaneneka