Mlongo akuphunzira Baibulo komanso kusinkhasinkha
Zitsanzo za Ulaliki
GALAMUKANI!
Funso: Kodi Baibulo ndi mawu ochokeradi kwa Mulungu? Kapena mumaliona ngati buku lomwe munangolembedwa maganizo a anthu?
Lemba: 2 Tim. 3:16
Perekani Magaziniyo: Galamukani! iyi ikufotokoza zinthu zitatu zotsimikizira kuti Baibulo linachokeradi kwa Mulungu.
KUPHUNZITSA CHOONADI
Funso: Kodi tiyenera kuiona bwanji mphatso ya moyo?
Lemba: Chiv. 4:11
Zoona Zake: Popeza moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, timaulemekeza kwambiri. Timayesetsa kupewa ngozi ndipo sitingachite mwadala zinthu zilizonse zimene zingawononge moyo wa munthu wina chifukwa timadziwa kuti moyo ndi mphatso yamtengo wapatali.
KODI N’CHIYANI CHINGATHANDIZE KUTI BANJA LIKHALE LOSANGALALA?
Funso: Taonani funso limene lili pa kapepalaka komanso mayankho amene aperekedwa. Kodi inuyo mungayankhe bwanji?
Lemba: Luka 11:28
Perekani Kapepalako: Kapepalaka kakufotokoza zimene banja lanu lingachite kuti lizikhala losangalala komanso chifukwa chake tiyenera kukhulupirira zimene Baibulo limanena.
LEMBANI ULALIKI WANUWANU
Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.