CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MALIKO 13-14
Pewani Msampha Woopa Anthu
N’chifukwa chiyani atumwi anakodwa mumsampha woopa anthu?
Ankadzidalira kwambiri. Mwachitsanzo Petulo ankaona kuti iyeyo adzakhalabe wokhulupirika kwa Yesu kuposa atumwi enawo
Iwo analephera kukhalabe maso komanso anasiya kupemphera
Yesu ataukitsidwa, n’chiyani chinathandiza atumwi kuti asamaope anthu n’kumalalikirabe ngakhale kuti ankatsutsidwa?
Anamvera machenjezo a Yesu ndipo zotsatira zake analimba mtima pamene ankatsutsidwa komanso kuzunzidwa
Anadalira Yehova komanso anapemphera.—Mac. 4:24, 29
Kodi ndi zochitika ziti zimene zingachititse kuti kulimba mtima kukhale kovuta?