Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb19 April tsamba 4-5
  • Kodi Muchikonzekera Bwanji Chikumbutso?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Muchikonzekera Bwanji Chikumbutso?
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Nkhani Yofanana
  • B12-A Wiki Yomaliza ya Moyo wa Yesu Padziko Lapansi (Gawo 1)
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • B12-B Wiki Yomaliza ya Moyo wa Yesu Padziko Lapansi (Gawo 2)
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Ndandanda Yowerengera Baibulo pa Nyengo ya Chikumbutso cha 2023
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Ndandanda Yowerengera Baibulo pa Nyengo ya Chikumbutso cha 2022
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
mwb19 April tsamba 4-5

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Muchikonzekera Bwanji Chikumbutso?

Kuyambira chaka chino, tizikhala ndi nthawi yambiri yokonzekera Chikumbutso cha imfa ya Yesu. Chikumbutso chikakhala m’kati mwa mlungu, sitizikhala ndi msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu. Komanso ngati chingakhale kumapeto kwa mlungu, sitizikhala ndi nkhani ya onse komanso Phunziro la Nsanja ya Olonda. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji nthawi imeneyi? Mofanana ndi zomwe zinkachitika m’nthawi ya atumwi, pali zambiri zimene tingachite pokonzekera mwambowu. (Luka 22:7-13; km 3/15 1) Komabe, tiyeneranso kukonzekeretsa mtima wathu. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

  • Tiziganizira kufunika kopezeka pa mwambowu.​—1 Akor. 11:23-26

  • Tizipemphera komanso kuganizira mmene ubwenzi wathu ndi Yehova ukuyendera.​—1 Akor. 11:27-29; 2 Akor. 13:5

  • Tiziwerenga komanso kuganizira Malemba omwe amafotokoza za kufunika kwa mwambo wa Chikumbutso.​—Yoh. 3:16; 15:13

Ofalitsa ena amawerenga Baibulo komanso kuganizira mavesi a pa nyengo ya Chikumbutso opezeka m’kabuku ka Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku. Ena amawerenga mavesi a m’Baibulo omwe ali patchati chili m’munsichi. Komanso ena amawerenganso nkhani za mu Nsanja ya Olonda zokhudza Chikumbutso komanso zofotokoza chikondi chimene Yehova ndi Yesu anatisonyeza. Njira iliyonse imene mungasankhe ingakuthandizeni kuyandikira kwambiri Yehova ndi Mwana wake.

Zimene Zinachitika pa Mlungu Womaliza wa Moyo wa Yesu Padziko Lapansi (Gawo 1 ndi 2)
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena