CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AKOLOSE 1-4
Vulani Umunthu Wakale N’kuvala Umunthu Watsopano
Kodi mutaphunzira choonadi munasintha makhalidwe amene munali nawo poyamba? Musamakayikire kuti Yehova anasangalala chifukwa cha khama limene munasonyeza kuti musinthe. (Ezek. 33:11) Komabe mumafunika kuyesetsa kuti musayambirenso kuchita makhalidwe oipa komanso kuti mupitirize kusonyeza umunthu watsopano. Yankhani mafunso ali m’munsiwa kuti mudziwe mbali zimene mukufunikira kusintha:
Kodi ndimasungirabe chakukhosi munthu wina yemwe anandilakwira?
Kodi ndimachita zinthu modekha ngakhale zitakhala kuti ndikufulumira komanso ndatopa?
Kodi ndikayamba kuganizira zinthu zolakwika ndimasintha n’kuyamba kuganizira zinthu zabwino?
Kodi ndimadana ndi anthu ena chifukwa cha mtundu wawo kapena kumene anachokera?
Kodi chaposachedwapa ndinapsa mtima kapena kulankhula mawu achipongwe kwa munthu wina?