Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb19 November tsamba 3
  • Musamatengere Maganizo a M’dzikoli Mukamakonzekera Ukwati

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Musamatengere Maganizo a M’dzikoli Mukamakonzekera Ukwati
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Mungachite Kuti Tsiku la Ukwati Wanu Likhale Losangalatsa ndi Lolemekezeka Kwambiri
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Maukwati Osangalatsa Amene Amalemekeza Yehova
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Maukwati Olemekeza Yehova
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kodi Paukwati wa Mboni za Yehova Pamachitika Zotani?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
mwb19 November tsamba 3
Chithunzi cha ukwati

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Musamatengere Maganizo a M’dzikoli Mukamakonzekera Ukwati

Akhristu amene akukonzekera kukwatirana amakhala ndi zinthu zambiri zoti asankhe. Nthawi zina angakakamizike kuti adzakhale ndi ukwati wapamwamba potengera maukwati ena a m’dera lawo. Nthawi zinanso anzawo komanso achibale awo angawakakamize kuti adzachite zinazake. Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zomwe zingawathandize kukonzekera bwino tsiku la ukwati wawo kuti asadzadziimbe mlandu kapena kunong’oneza bondo?

ONERANI VIDIYO YAKUTI UKWATI UMENE UMALEMEKEZA YEHOVA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi mfundo za m’Malembawa zinathandiza bwanji Nick ndi Juliana?

    • 1 Akor. 10:31

    • 1 Yoh. 2:15, 16

    • Agal. 5:19-21

    • 1 Tim. 2:9

  • N’chifukwa chiyani Akhristu omwe akufuna kukwatirana ayenera kusankha m’bale wokhulupirika kuti adzakhale “woyang’anira phwando” la ukwati wawo?​—Yoh. 2:9, 10.

  • N’chifukwa chiyani Nick ndi Juliana anasankha kuchita zinthu zosiyana ndi anthu ena paukwati wawo?

  • Kodi ndi ndani ali ndi udindo wosankha mmene mwambo komanso phwando laukwati lidzakhalire?​—w06 10/15 25 ¶10.

Zithunzi za m’vidiyo yakuti, ‘Ukwati Umene Umalemekeza Yehova.’ Nick ndi Juliana ndi akukonzekera kudzakhala ndi ukwati ndipo ali ndi zinthu zambiri zoti asankhe. 1. Aliyense akupemphera ali kwayekha. 2. Tabuleti komanso mapepalawo zikusonyeza zomwe akhala akufufuza. 3. Nick ndi Juliana akukambirana ndi achibale awo zomwe akufuna kuti zidzachitike paukwati wawo. 4. Nick ndi Juliana ali limodzi ndi achibale ndi anzawo ndipo akulemba makadi oitanira anthu ku ukwati.
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena