Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb20 April tsamba 7
  • “Chotsani Milungu Yachilendo”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Chotsani Milungu Yachilendo”
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Kuchita Zamatsenga Kuli ndi Vuto Lililonse?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Lolani Kuti Yehova Akuthandizeni Polimbana ndi Mizimu Yoipa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani pa Nkhani ya Kukhulupirira Zamizimu?
    Galamukani!—2017
  • Tizikhala Odzipereka kwa Yehova Yekha
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20 April tsamba 7
Munthu akutaya nekilesi yokhudzana ndi zamizimu.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Chotsani Milungu Yachilendo”

Yakobo ankadziwa kuti ayenera kulambira Yehova yekha ngakhale kuti pa nthawiyo Mulungu anali asanapereke lamulo loletsa kulambira mafano. (Eks 20:3-5) Yehova atamuuza kuti abwerere ku Beteli, iye anauza anthu onse amene anali naye kuti achotse mafano awo. Ndiyeno Yakobo anawononga mafano onse kuphatikizaponso ndolo zomwe anthu ankavala ngati zithumwa. (Ge 35:1-4) N’zoonekeratu kuti Yehova anasangalala ndi zimene Yakobo anachitazi.

Kodi masiku ano tingasonyeze bwanji kuti timalambira Yehova yekha? Tiyenera kupewa chilichonse chokhudzana ndi kulambira mafano kapena kukhulupirira mizimu. Zimenezi zikuphatikizapo kuchotsa chilichonse chokhudzana ndi matsenga komanso kukhala osamala ndi zosangalatsa zomwe timakonda. Mwachitsanzo, mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndimakonda mabuku komanso mafilimu onena za mavampaya, mizukwa kapena zinthu zina zamatsenga? Kodi zosangalatsa zomwe ndimakonda zimandichititsa kuganiza kuti nkhani zamatsenga, kulodzana kapena kutemberera ena zilibe vuto?’ Tiyenera kupeweratu chilichonse chimene Yehova amadana nacho.​—Sl 97:10.

ONERANI VIDIYO YAKUTI “TSUTSANI MDYEREKEZI,” KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Mwana wagona pabedi ndipo wavala chithumwa pamkono. Mayi ake akucheza ndi banja lomwe limawaphunzitsa Baibulo.

    Kodi Palesa anakumana ndi vuto lotani?

  • Banja lija limodzi ndi mayi yemwe amaphunzira naye Baibulo akukumana ndi akulu kuti awathandize.

    N’chifukwa chiyani ndi nzeru kupempha thandizo kwa akulu ngati ifeyo, munthu amene timaphunzira naye Baibulo kapenanso munthu amene tikumudziwa akuvutitsidwa ndi ziwanda?

  • Mayi yemwe akuphunzira Baibulo akuotcha chithumwa cha mwana wake pa sitovu.

    Tsutsani Mdyerekezi ndipo yandikirani Mulungu.​—Yak 4:7, 8

    Kodi ndi zinthu ziti zomwe anthu amene akufuna kuti Yehova aziwateteza ayenera kupewa?

  • Kodi Palesa anachita chiyani atathandizidwa ndi akulu?

  • Kodi m’dera limene mukukhala, ndi zinthu ziti zimene muyenera kupewa kuti musamavutitsidwe ndi ziwanda?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena