Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb22 March tsamba 13
  • Mavuto Onse Ali Ndi Tsiku Lothera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mavuto Onse Ali Ndi Tsiku Lothera
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amatithandiza Tikamakumana ndi Mayesero
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Pitirizani Kukhala Oleza Mtima
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Kodi Mukhoza Kuyembekezera Moleza Mtima?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Tiziyembekezera Yehova Moleza Mtima
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwb22 March tsamba 13
Zithunzi: Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Anthu Ogwirizana M’dziko Limene Anthu Ake Sagwirizana.” 1. Gulu la abale ndi alongo achikuda okhaokha ali pamsonkhano. 2. Abale akuda ndi azungu limodzi ndi azikazi awo anajambulitsa chithunzi ali limodzi. 3. Alongo awiri amisinkhu komanso mitundu yosiyana akulalikira limodzi pamalo wopezeka anthu ambiri.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Mavuto Onse Ali Ndi Tsiku Lothera

Mavuto akhoza kutifooketsa, makamaka ngati atenga nthawi yaitali. Davide ankadziwa kuti mavuto amene ankakumana nawo kuchokera kwa Mfumu Sauli adzatha, ndipo adzakhala mfumu monga mmene Yehova analonjezera. (1Sa 16:13) Chikhulupiriro chinamuthandiza Davide kuti akhale woleza mtima n’kumayembekezera Yehova.

Tikamakumana ndi mavuto, tikhoza kuchita zinthu mochenjera, mwanzeru komanso tingagwiritse ntchito luso lathu la kuganiza kuti tithane ndi mavuto amene tikukumana nawowo. (1Sa 21:12-14; Miy 1:4) Komabe, mavuto ena sangathe ngakhale titachita zinthu zonse zimene tingakwanitse zomwe ndi zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Pa zochitika ngati zimenezi tiyenera kukhala oleza mtima n’kumayembekezera Yehova. Posachedwapa, iye athetsa mavuto onse ndipo ‘apukuta misozi yonse’ m’maso mwathu. (Chv 21:4) Kaya mavuto athu atha chifukwa choti Yehova walowererapo, kapena pa zifukwa zina, mfundo yosatsutsika ndi imodzi: Mavuto onse ali ndi tsiku lothera. Imeneyitu ndi mfundo yolimbikitsa kwambiri.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ANTHU OGWIRIZANA M’DZIKO LIMENE ANTHU AKE SAGWIRIZANA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi ndi mavuto otani omwe Akhristu a kummwera kwa United States ankakumana nawo?

  • Kodi anasonyeza bwanji kuleza mtima komanso chikondi?

  • Kodi anatani kuti aike maganizo awo onse pa “zinthu zofunika kwambiri”?​—Afi 1:10

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena