Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w23 August tsamba 32
  • Mfundo Zothandiza Pophunzira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mfundo Zothandiza Pophunzira
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Muzifufuza Zambiri Zokhudza Makhalidwe a Yehova
  • Muzifufuza Mfundo Zothandiza Zomwe Mungagwiritse Ntchito
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Kodi Yehova Ndi Wotani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Ndimotani Mmene Munthu Angakhalire m’Chifanizo cha Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Mmene Mungafufuzire
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
w23 August tsamba 32

Mfundo Zothandiza Pophunzira

Muzifufuza Zambiri Zokhudza Makhalidwe a Yehova

Tikamawerenga Baibulo, tingathe kugwiritsa ntchito zinthu zothandiza pophunzira zosiyanasiyana kuti timvetse zomwe tikuwerengazo. Komabe timafunika kufufuza zambiri. Timafuna kupeza mfundo zothandiza zokhudza makhalidwe a Yehova zomwe zingachititse kuti tizimukonda kwambiri. Kuti tichite zimenezi, tiyenera kumadzifunsa kuti: ‘Kodi zimene ndikuwerenga m’Baibulozi, zikundiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova?’

Tingathe kufufuza umboni wosonyeza kuti Yehova ndi wachikondi, wanzeru, wachilungamo komanso wamphamvu, omwe ndi makhalidwe ake akuluakulu. Komabe Yehova ali ndi makhalidwe ena ambiri kuwonjezera pa amenewa. Kodi mungapeze kuti mfundo zokhudza makhalidwe ake?

Mungapeze makhalidwe enanso oposa 50, mu Watch Tower Publications Index pamutu wakuti “Jehovah,” ndipo kenako pakamutu kakuti “Qualities by Name.” Muzifufuza makhalidwe amene akugwirizana ndi nkhani ya m’Baibulo yomwe mukuwerenga. (Ngati ndi Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani lokha lomwe mungalipeze, pitani pamutu wakuti “Yehova Mulungu,” kenako pakamutu kakuti “Makhalidwe a Yehova.”)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena