Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w24 February tsamba 32
  • Muzifufuza Mfundo Zothandiza Zomwe Mungagwiritse Ntchito

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzifufuza Mfundo Zothandiza Zomwe Mungagwiritse Ntchito
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Nkhani Yofanana
  • Mfundo Zothandiza Pophunzira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?—Gawo 1: Kuganizira Mozama Mfundo za M’baibulo
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Muziuza Ena Zimene Mwaphunzira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Pitirizani Kufunafuna Monga Chuma Chobisika
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
w24 February tsamba 32

Mfundo Zothandiza Pophunzira

Muzifufuza Mfundo Zothandiza Zomwe Mungagwiritse Ntchito

Tikamawerenga Baibulo, tingathe kupeza mfundo zothandiza pofufuza zambiri zokhudza nkhani yomwe tikuwerenga. Ndiye kodi tingatani kuti tizipindula kwambiri?

Muzifufuza mozama nkhani za m’Baibulo. Mwachitsanzo, muzifufuza kuti mudziwe amene analemba, amene ankawalembera komanso nthawi yomwe analemba zinthuzo. Kodi zinthu zinali bwanji pa nthawiyo, n’chiyani chinachitika asanalembe zinthuzo, nanga chinachitika n’chiyani pambuyo pake?

Muziganizira zimene mukuphunzirapo pofufuza mayankho a mafunso ngati awa: ‘Kodi anthu otchulidwawo ankamva bwanji? Kodi anasonyeza makhalidwe ati? N’chifukwa chiyani ndiyenera kutsanzira makhalidwewo kapena kuwapewa?’

Muzigwiritsa ntchito zimene mwaphunzirazo mu utumiki kapenanso pochita zinthu ndi ena. Mukamachita zimenezi, mumasonyeza nzeru ya Mulungu, monga mmene Baibulo limanenera kuti: “Aliyense wanzeru aona zinthu zimenezi.”​—Sal. 107:43.

  • Zokuthandizani: Muziona mmene nkhani za pamisonkhano ya mkati mwa mlungu pa gawo lakuti Chuma Chopezeka M’mawu a Mulungu, zimatithandizira kugwiritsa ntchito zimene taphunzira. Nthawi zambiri nkhanizi zimakhala ndi mafunso omwe tingadzifunse, mfundo zomwe tingaganizire komanso zithunzi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena