Mungatani Kuti Muzikhala Mwamtendere Ngakhale Kuti Kuli Nkhondo Komanso Zachiwawa?
Gary yemwe anali msilikali ananena kuti: “Ndisanaphunzire Baibulo sindinkadziwa chifukwa chake padzikoli pakuchitika zinthu monga nkhanza, kupanda chilungamo komanso mavuto ena ochuluka. Koma panopa ndili ndi mtendere wamaganizo. Ndikudziwa kuti Yehova Mulungu adzachititsa kuti dzikoli likhale malo otetezeka.”
Si Gary yekha amene ananena zimenezi. Onani mmene Baibulo lathandizira anthu enanso.
BAIBULO LIMATI: “Inu Yehova ndinu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.”—Salimo 86:5.
KODI MFUNDOYI NDI YOTHANDIZA BWANJI? “Vesili limanditsimikizira kuti Yehova ndi wachifundo. Ndimadziwa kuti ndi wofunitsitsa kundikhululukira pa zimene ndinachita m’mbuyomu pa nthawi imene ndinkamenya nkhondo.”—Wilmar, wa ku Colombia.
BAIBULO LIMATI: “Ndikulenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Ndipo zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso, kapena kuvutitsa maganizo.”—Yesaya 65:17.
KODI MFUNDOYI NDI YOTHANDIZA BWANJI? “Ndimavutika ndi nkhawa chifukwa cha zinthu zoopsa zomwe ndinaona pa nthawi ya nkhondo komanso ndimadwala matenda ovutika maganizo. Koma lembali limandikumbutsa kuti posachedwapa Yehova adzachititsa kuti ndiiwaliretu zinthu zoipa zonsezi. Zinthu zimenezi zidzakhala mbiri yakale. Imeneyitu ndi mphatso yapadera.”—Zafirah, wa ku United States.
BAIBULO LIMATI: “Mʼmasiku a ulamuliro wake, wolungama zinthu zidzamuyendera bwino, ndipo padzakhala mtendere wochuluka kwa nthawi yonse imene mwezi udzakhalepo.”—Salimo 72:7.
KODI MFUNDOYI NDI YOTHANDIZA BWANJI? “Nthawi zambiri ndimaganizira mawu amenewa. Posachedwapa sikudzakhalanso nkhondo komanso zoopsa zonse zimene zimayamba chifukwa cha nkhondo. Anthufe tidzasiyiratu kudera nkhawa za chitetezo chathu kapena cha abale athu.”—Oleksandra, wa ku Ukraine.
BAIBULO LIMATI: “Anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo. . . . Dzukani ndipo mufuule mosangalala, inu anthu okhala mʼfumbi!”—Yesaya 26:19.
KODI MFUNDOYI NDI YOTHANDIZA BWANJI? “Pafupifupi anthu onse am’banja langa anaphedwa pa nthawi imene anthu a mtundu wina ankapha Atutsi. Koma vesi limeneli limanditsimikizira kuti onsewa ndidzawaonanso. Ndikuyembekezera mwachidwi kudzamvanso mawu awo osangalatsa akadzaukitsidwa.”—Marie, wa ku Rwanda.
BAIBULO LIMATI: “Kwatsala kanthawi kochepa, ndipo oipa sadzakhalaponso . . . Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:10, 11.
KODI MFUNDOYI NDI YOTHANDIZA BWANJI? “Ngakhale kuti nkhondo inatha, anthu ochita zinthu zopanda chilungamo komanso oipa akadalipo. Mavesiwa akhala akundithandiza kwambiri. Yehova amaona zonse ndipo amamvetsa mmene zinthu zilili pa moyo wanga. Iye amalonjeza kuti posachedwapa mavuto onsewa adzatha ndipo adzaiwalika.”—Daler, wa ku Tajikistan.
Anthu amene atchulidwa m’magaziniyi ali m’gulu la a Mboni za Yehova mamiliyoni ambirimbiri amene Baibulo lawathandiza kukhala ndi mtendere. Iwo aphunzira kuthana ndi mavuto monga kusankhana mitundu komanso chidani. (Aefeso 4:31, 32) A Mboni za Yehova salowerera nkhani za ndale ndipo amakana kuchita nawo zachiwawa.—Yohane 18:36.
A Mboni za Yehova amathandizana ngati anthu a m’banja limodzi. (Yohane 13:35) Mwachitsanzo, Oleksandra, amene tamutchula kale uja anathawira kudziko lina ndi mchemwali wake chifukwa cha nkhondo. Iye ananena kuti: “Titangowoloka malire a dziko lathu, nthawi yomweyo tinaona a Mboni za Yehova omwe anabwera kudzatilandira. Sitinavutike kuzolowera moyo wa m’dziko lachilendo chifukwa chakuti anatithandiza kwambiri.”
Tikukupemphani kuti mubwere kudzasonkhana nafe kuti mudzaphunzire zimene Baibulo limanena pa nkhani ya mtendere komanso mmene mungagwiritsire ntchito zomwe mudzaphunzirezo. Pitani pa jw.org kuti mupeze Nyumba ya Ufumu yakufupi ndi kwanu kapena mungapemphe kuti muziphunzira Baibulo mochita kukambirana ndi mmodzi wa Mboni za Yehova, pogwiritsa ntchito buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale.