Nkhondo Ndi Yoopsa Kwambiri
Poyerekeza ndi mavuto ena, nkhondo komanso zachiwawa ndi zimene zimachititsa kuti anthu azivutika kwambiri. Asilikali komanso anthu wamba amene anakhudzidwapo ndi nkhondo amadziwa bwino mavuto amene amabwera chifukwa cha nkhondo.
ASILIKALI
“Pa nthawi ya nkhondo kumachitika zinthu zoopsa, umaona anthu akuphedwa komanso kuvulazidwa. Aliyense amakhala mwamantha.”—Gary, wa ku Britain.
“Anandiwomberapo kumsana ndi kunnkhope komanso ndinaonapo anthu ambiri akuphedwa, kuphatikizapo ana ndi akuluakulu omwe. Nkhondo imakuchititsa kukhala wouma mtima.”—Wilmar, wa ku Colombia.
“Ukaona munthu akuwomberedwa, zimene waonazo sumaziiwala. M’maganizomu umangokhalira kumva mmene munthuyo ankalilira komanso mmene ankabuulira. Zimene zinamuchitikirazo umazikumbukirabe mpaka kalekale.”—Zafirah, wa ku United States.
ANTHU WAMBA
“Ndinkaganiza kuti sindidzakhalanso wosangalala mpaka kalekale. Nthawi zonse umakhala mwamantha kuti iweyo kapena anthu am’banja lako akhoza kuphedwa.”—Oleksandra, wa ku Ukraine.
“Tinkaima pamzere woti tilandire chakudya kuyambira 2 koloko m’mawa mpaka 11 koloko usiku, ndipo nthawi zonse tinkaopa kuti tikhoza kuwomberedwa ndi zipolopolo zosochera.”—Daler, wa ku Tajikistan.
“Makolo anga anaphedwa pa nkhondo. Zimenezi zinachititsa kuti ndikhale wamasiye popanda wina aliyense wonditonthoza kapenanso kundisamalira.”—Marie, wa ku Rwanda.
Ngakhale kuti nkhondo inachititsa kuti anthu amene tawatchula pamwambawa akumane ndi zinthu zoopsa, iwo anapeza mtendere. Komanso, sakayikira kuti nkhondo ndi zachiwawa zonse zitha posachedwapa. Magazini ya Nsanja ya Olonda ino ifotokoza mfundo za m’Baibulo zosonyeza mmene nkhondo idzathere.