NKHANI YOPHUNZIRA 14
NYIMBO NA. 8 Yehova Ndi Pothawirapo Pathu
“Sankhani . . . Amene Mukufuna Kum’tumikira”
“Koma ine ndi banja langa tizitumikira Yehova.”—YOS. 24:15.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Nkhaniyi itikumbutsa zifukwa zimene zinatichititsa kusankha kutumikira Yehova.
1. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale osangalala? Perekani chifukwa. (Yesaya 48:17, 18)
ATATE wathu wakumwamba amatikonda kwambiri ndipo amafuna kuti tizisangalala panopa komanso m’tsogolo. (Mlal. 3:12, 13) Iye anatilenga m’njira yoti tizitha kusonyeza maluso osiyanasiyana. Koma sanatilenge m’njira yoti tizidzilamulira tokha kapenanso kumasankha tokha kuti ichi n’choyenera kapena cholakwika. (Mlal. 8:9; Yer. 10:23) Iye amadziwa kuti tikhoza kumasangalala kwambiri ngati titamamutumikira komanso kutsatira mfundo zake.—Werengani Yesaya 48:17, 18.
2. Kodi Satana amafuna tizikhulupirira bodza liti, nanga Yehova wayankha bwanji bodza limeneli?
2 Satana amafuna kuti tizikhulupirira kuti tikhoza kukhala osangalala popanda kutsogoleredwa ndi Yehova, kapena kuti anthu akhoza kumadzilamulira bwinobwino. (Gen. 3:4, 5) Yehova anayankha bodza limeneli polola kuti anthu adzilamulire okha kwa kanthawi. Kulikonse tikuona umboni wakuti ulamuliro wa anthu si wabwino. Koma m’Malemba muli zitsanzo za amuna ndi akazi omwe anakhala osangalala chifukwa chotumikira Yehova. Munthu mmodzi amene anasangalala kwambiri ndi Yesu Khristu. Choyamba, tiyeni tione chifukwa chake iye anasankha kutumikira Yehova. Kenako tikambirana chifukwa chake Atate wathu wakumwamba ali woyenera kulambiridwa. Pomaliza tikambirana zifukwa zomwe zimatichititsa kusankha kutumikira Yehova.
N’CHIFUKWA CHIYANI YESU ANASANKHA KUTUMIKIRA YEHOVA?
3. Kodi Satana anauza Yesu kuti achite chiyani, nanga Yesu anayankha bwanji?
3 Yesu ali padziko lapansi anafunika kusankha woti azimutumikira. Atangobatizidwa kumene, Satana anamuuza kuti amupatsa maufumu onse a padziko lapansi ngati atangomulambira kamodzi kokha. Yesu anamuyankha kuti: “Choka Satana! Chifukwa Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’” (Mat. 4:8-10) N’chifukwa chiyani Yesu ananena zimenezi? Tiyeni tione zifukwa zitatu.
4-5. N’chifukwa chiyani Yesu anasankha kutumikira Yehova?
4 Chifukwa chachikulu chomwe chinachititsa Yesu kusankha kuti azitumikira Yehova ndi chikondi. Yesu amakonda kwambiri Atate wake ndipo sangasiye kuwakonda. (Yoh. 14:31) Kuwonjezera pamenepo, Yesu amatumikira Yehova chifukwa amadziwa kuti zimenezo ndi zimene ayenera kuchita. (Yoh. 8:28, 29; Chiv. 4:11) Amadziwanso kuti Yehova ndi amene anatipatsa moyo, ndi wodalirika komanso ndi wowolowa manja. (Sal. 33:4; 36:9; Yak. 1:17) Yehova ankauza Yesu zoona zokhazokha ndipo ndi amene anamupatsa chilichonse chomwe anali nacho. (Yoh. 1:14) Pomwe Satana ndi amene anayambitsa imfa. Iye ndi wabodza ndipo amachita zinthu chifukwa chadyera komanso kudzikonda. (Yoh. 8:44) Chifukwa chodziwa mfundo zonsezi, Yesu sanaganizirepo zosiya kumvera Yehova ngati mmene Satana anachitira.—Afil. 2:5-8.
5 Chifukwa china chimene chinachititsa Yesu kusankha kutumikira Yehova ndi chakuti ankaganizira zimene zingachitike ngati atakhalabe wokhulupirika. (Aheb. 12:2) Iye ankadziwa kuti ngati atakhalabe wokhulupirika adzayeretsa dzina la Atate wake komanso adzathetsa mavuto amene Mdyerekezi anayambitsa.
N’CHIFUKWA CHIYANI YEHOVA ALI WOYENERA KUMULAMBIRA?
6-7. N’chifukwa chiyani anthu ambiri masiku ano amakana kutumikira Yehova, nanga n’chifukwa chiyani iye ndi woyenera kutumikiridwa?
6 Anthu ambiri masiku ano satumikira Yehova chifukwa sadziwa makhalidwe abwino amene ali nawo komanso sazindikira zinthu zonse zimene wawachitira. Umu ndi mmenenso zinalili kwa anthu amene mtumwi Paulo anawalalikira ku Atene.—Mac. 17:19, 20, 30, 34.
7 Paulo anauza anthuwo kuti Mulungu woona “amapatsa anthu onse moyo, mpweya ndi zinthu zonse.” Anawonjezeranso kuti: “Chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” Mulungu ndi woyenera kulambiridwa chifukwa iye ndi Mlengi amene “kuchokera mwa munthu mmodzi anapanga mitundu yonse ya anthu.”—Mac. 17:25, 26, 28.
8. Kodi n’chiyani chomwe Yehova sangachite? Fotokozani.
8 Popeza kuti Yehova ndi Mlengi komanso Mfumu ya chilengedwe chonse, akanatha kukakamiza anthu kuti azimutumikira. Koma Yehova sangachite zimenezo. M’malomwake amatipatsa umboni wakuti iye alipodi ndipo amatikonda kwambiri. Amafuna anthu ambiri akhale anzake mpaka kalekale. (1 Tim. 2:3, 4) Kuti zimenezi zitheke, Yehova watiphunzitsa mmene tingauzire ena za zolinga zake komanso zokhudza zinthu zabwino zomwe adzachitire anthu m’tsogolo. (Mat. 10:11-13; 28:19, 20) Kuti tizimulambira bwino, iye watipatsa mpingo komanso akulu achikondi oti azitithandiza.—Mac. 20:28.
9. Kodi Yehova wasonyeza bwanji chikondi chake?
9 Chikondi cha Yehova chimaonekera bwino tikaganizira mmene amachitira zinthu ndi anthu omwe sakhulupirira kuti iye aliko. Taganizirani mfundo izi: Kuyambira kale, anthu ambiri akhala akusankha kuyendera mfundo zawo zokhudza chabwino ndi choipa. Koma mokoma mtima, Yehova wakhala akuwapatsa zinthu zowathandiza kuti akhale ndi moyo komanso azisangalala. (Mat. 5:44, 45; Mac. 14:16, 17) Amawathandiza kuti azitha kukhala ndi anzawo, kukhala ndi banja komanso kupindula ndi ntchito zawo. (Sal. 127:3; Mlal. 2:24) Zimenezi zimasonyeza kuti Atate wathu wakumwamba amakonda anthu onse. (Eks. 34:6) Tsopano tiyeni tikambirane zifukwa zomwe zimatichititsa kusankha kuti tizitumikira Yehova komanso mmene iye amatidalitsira.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIMASANKHA KUTUMIKIRA YEHOVA?
10. (a) Kodi chifukwa chachikulu chomwe timatumikirira Yehova ndi chiyani? (Mateyu 22:37) (b) Kodi kuleza mtima kwa Yehova kwakuthandizani bwanji? (Salimo 103:13, 14)
10 Mofanana ndi Yesu, timatumikira Yehova chifukwa chakuti timamukonda kwambiri. (Werengani Mateyu 22:37.) Kuphunzira zambiri zokhudza makhalidwe ake kumatichititsa kuti tikhale naye pa ubwenzi. Mwachitsanzo, taganizirani mmene Yehova amasonyezera kuleza mtima. Pa nthawi ina Aisiraeli atalephera kumumvera, iye anawachonderera kuti: “Bwererani nʼkusiya njira zanu zoipa.” (Yer. 18:11) Yehova amakumbukira kuti anthufe si angwiro ndipo ndife fumbi. (Werengani Salimo 103:13, 14.) Tikaganizira mmene Yehova amatisonyezera kuleza mtima komanso makhalidwe ake ena abwino, timafunitsitsa kumutumikira mpaka kalekale.
11. Kodi ndi zifukwa zina ziti zomwe zimatichititsa kusankha kutumikira Atate wathu wakumwamba?
11 Timafunitsitsanso kutumikira Yehova chifukwa timadziwa kuti ndi zimene tiyenera kuchita. (Mat. 4:10) Timadziwanso zimene zingachitike ngati titakhalabe okhulupirika. Tikakhala okhulupirika timathandiza kuti dzina la Yehova liyeretsedwe, timasonyeza kuti Mdyerekezi ndi wabodza komanso timasangalatsa mtima wa Atate wathu. Ndipo tikasankha kutumikira Yehova panopa, timakhala ndi chiyembekezo chodzamutumikira mpaka kalekale.—Yoh. 17:3.
12-13. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Jane ndi Pam?
12 Ngati titayamba kukonda Yehova kuyambira tili aang’ono, chikondicho chikhoza kupitirirabe ngakhale titakalamba. Izi ndi zimene zinachitikira Jane ndi mchemwali wake Pam.a Iwo anayamba kuphunzira Baibulo wina ali ndi zaka 10 wina 11. Makolo awo sankakonda kuphunzira koma ankalola Jane ndi Pam kuti aziphunzira ndi a Mboni. Chomwe ankangofuna n’chakuti kumapeto kwa mlungu azipita kutchalitchi kwawo. Jane anati: “Zimene a Mboni ankandiphunzitsa m’Baibulo zinandithandiza kuti ndisamangotengera anzanga omwe ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kuchita zachiwerewere.”
13 Atsikana onsewa anakhala ofalitsa asanakwanitse zaka 20. Kenako anayamba upainiya uku akusamalira makolo awo okalamba. Jane anafotokoza mmene amamvera akaganizira zimene Yehova wamuchitira. Iye anati: “Ndaphunzira kuti Yehova ndi wokhulupirika ndipo amasamalira anzake. Ndipo mogwirizana ndi lemba la 2 Timoteyo 2:19,‘Yehova amadziwa anthu ake.’” N’zosachita kufunsa kuti Yehova amasamalira anthu amene amamukonda komanso kumutumikira.
14. Kodi zolankhula ndi zochita zathu zimathandiza bwanji kuyeretsa dzina la Yehova? (Onaninso zithunzi.)
14 Timafuna kuthandiza nawo poyeretsa dzina la Mulungu. Tiyerekeze kuti muli ndi mnzanu yemwe ndi wokoma mtima, wopatsa komanso wokhululuka. Ndiyeno tsiku lina mukumva munthu wina akukuuzani kuti mnzanuyo ndi munthu wankhanza komanso wachinyengo. Kodi mungatani? Mukhoza kumuikira kumbuyo mnzanuyo. Mofanana ndi zimenezi, Satana ndi anthu omwe ali kumbali yake amafuna kuipitsa mbiri ya Yehova ponena zabodza zokhudza iye. Choncho timaikira kumbuyo Yehova pouza ena zokhudza iye ndi dzina lake. (Sal. 34:1; Yes. 43:10) Zolankhula komanso zochita zimasonyeza kuti timafuna kutumikira Yehova ndi mtima wathu wonse.
Kodi muthandiza nawo kuikira kumbuyo mbiri ya Yehova? (Onani ndime 14)b
15. Kodi mtumwi Paulo anapindula bwanji chifukwa chosintha zinthu pa moyo wake? (Afilipi 3:7, 8)
15 Timasintha zinthu zina pa moyo n’cholinga choti tizitumikira Yehova movomerezeka komanso ndi mtima wonse. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analolera kusiya udindo wapamwamba umene anali nawo n’cholinga choti akhale wophunzira wa Khristu n’kumatumikira Yehova. (Agal. 1:14) Izi zinathandiza kuti akhale ndi moyo wabwino komanso chiyembekezo chokalamulira ndi Khristu kumwamba. Iye sananong’oneze bondo chifukwa cha zimene anasankha. Ngati ifenso titasankha kutumikira Yehova, sitidzanong’oneza bondo.—Werengani Afilipi 3:7, 8.
16. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Julia? (Onaninso zithunzi.)
16 Tikamaona kuti kutumikira Yehova ndi kofunika kwambiri tidzakhala ndi moyo wabwino panopa komanso m’tsogolo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Julia. Ali wamng’ono komanso asanaphunzire choonadi, Julia ankaimba kwaya kuchipembedzo chawo. Katswiri wina woimba anaona kuti Julia ali ndi luso ndipo anamuphunzitsa kuimba bwino. Pasanapite nthawi yaitali Julia anakhala woimba wotchuka ndipo ankaimba m’maholo akuluakulu. Ali kusukulu ina yophunzitsa kuimba, mnzake wina anayamba kumuuza zokhudza Mulungu ndipo anamufotokozera kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Pasanapite nthawi yaitali, Julia anayamba kuphunzira Baibulo kawiri pa mlungu. Kenako anaganiza zosiya kuphunzira kuimba n’cholinga choti azitumikira Yehova. Koma zimenezi sizinali zophweka. Julia anati: “Anthu ambiri ankandiuza kuti ndikutaya mwayi. Koma ine ndinkafuna kutumikira Yehova ndi moyo wanga wonse.” Kodi Julia amamva bwanji panopa chifukwa cha zimene anasankha zaka 30 zapitazo? Iye anati: “Ndili ndi mtendere wamumtima ndipo ndimakhulupirira kuti Yehova adzandipatsa zonse zimene mtima wanga umafuna posachedwapa.”—Sal. 145:16.
Tikamaona kuti kutumikira Yehova ndi kofunika timakhala ndi moyo wosangalala ngakhale panopa (Onani ndime 16)c
PITIRIZANI KUTUMIKIRA YEHOVA
17. Kodi mfundo yoti mapeto ali pafupi ikukhudza bwanji anthu amene akutumikira Mulungu komanso amene sakumutumikira?
17 Mapeto a dzikoli ali pafupi kwambiri. Mtumwi Paulo analemba kuti: “‘Kwatsala kanthawi kochepa’ ndipo ‘amene akubwerayo afika ndithu, sachedwa.’” (Aheb. 10:37) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Choyamba, nthawi yoti anthu asankhe kutumikira Yehova ndi yochepa. (1 Akor. 7:29) Ndipo ngati tinasankha kale kutumikira Yehova, tikudziwa kuti mavuto amene tingawapirire ndi a “kanthawi kochepa.”
18. Kodi Yesu ndi Yehova amafuna kuti tizichita chiyani?
18 Yesu analimbikitsa anthu kuti akhale otsatira ake ndiponso kuti apitirize kumutsatira. (Mat. 16:24) Choncho ngati takhala tikutumikira Yehova kwa zaka zambiri tiyeni tisagwe ulesi. Tipitirize kukhala ndi moyo mogwirizana ndi zimene tinasankha ndipo tikatero tidzapeza madalitso ngakhale panopa.—Sal. 35:27.
19. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Gene?
19 Anthu ena amaganiza kuti munthu akamatumikira Yehova sasangalala. Ngati ndinu wachinyamata, kodi mumaganiza kuti mudzamanidwa zinthu zina chifukwa chotumikira Yehova? M’bale wina wachinyamata dzina lake Gene anati: “Zinkaoneka ngati anzanga akusangalala ndi zinthu ngati mapate, zibwenzi komanso masewera achiwawa a pa kompyuta pomwe ineyo ndinkangokhalira kumisonkhano ndi mu utumiki.” Kodi maganizo amenewa anamukhudza bwanji Gene? Iye anati: “Ndinayamba moyo wachinyengo ndipo kwa kanthawi ndinkaona kuti ndikusangalala. Koma chisangalalo chake chinali chosakhalitsa. Ndinayamba kuganizira mfundo za choonadi zomwe ndinazinyalanyaza ndipo kenako ndinaganiza zotumikira Yehova ndi mtima wanga wonse. Kuchokera nthawi imeneyo, Yehova wakhala akuyankha mapemphero anga onse.”
20. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?
20 Wolemba masalimo wina anaimbira Yehova kuti: “Wosangalala ndi munthu amene inu mwamusankha nʼkumubweretsa pafupi ndi inu, kuti akhale mʼmabwalo anu.” (Sal. 65:4) Choncho tiyeni tikhale ndi maganizo ngati amene Yoswa anali nawo, akuti: “Koma ine ndi banja langa tizitumikira Yehova.”—Yos. 24:15.
NYIMBO NA. 28 Tikhale pa Ubwenzi Ndi Yehova
a Mayina ena asinthidwa.
b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mayi wina wamva anthu otsutsa akulankhula panja pamalo a msonkhano. Kenako wapita pamene pali kashelefu ndipo akumvetsera uthenga wa choonadi.
c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Chithunzi choyerekezera zimene Julia anachita posankha kutumikira Yehova.