NKHANI YOPHUNZIRA 26
NYIMBO NA. 123 Tizigonjera Mulungu Mokhulupirika
Tizivomereza Modzichepetsa Kuti Sitikudziwa Zonse
“Wamphamvuyonse sitingathe kumumvetsa.”—YOBU 37:23.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Nkhaniyi itithandiza kudziwa mmene kuvomereza kuti sitikudziwa zonse kungatithandizire kupirira mavuto amene timakumana nawo. Itithandizanso kuti tiziganizira zimene tikudziwa komanso tizidalira Yehova.
1. Kodi Yehova anatilenga ndi luso lotha kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
YEHOVA anatilenga ndi luso loti tizitha kuganiza, kuphunzira, kumvetsa komanso kugwiritsa ntchito zimene taphunzira. N’chifukwa chiyani anatilenga m’njira imeneyi? Iye amafuna kuti ‘timudziwe’ bwino komanso tizigwiritsa ntchito luso lathu la kuganiza pomutumikira.—Miy. 2:1-5; Aroma 12:1.
2. (a) Kodi tiyenera kudziwa chiyani zokhudza anthufe? (Yobu 37:23, 24) (Onaninso chithunzi.) (b) Kodi kuvomereza modzichepetsa kuti sitidziwa zonse kumatithandiza bwanji?
2 Ngakhale kuti tinalengedwa ndi luso lotha kuphunzira, pali zinthu zina zimene sitimazidziwa. (Werengani Yobu 37:23, 24.) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yobu. Pa nthawi ina iye anafunsidwa mafunso angapo omwe anasonyeza kuti panali zambiri zomwe sankazidziwa. Zimenezi zinamuthandiza kukhala wodzichepetsa komanso kusintha mmene ankaganizira. (Yobu 42:3-6) Ifenso tingapindule kwambiri tikamavomereza modzichepetsa kuti sitikudziwa zonse. Kudzichepetsa kumeneku kungatithandize kuti tizikhulupirira kuti Yehova adzatithandiza kudziwa zimene tikufunikadi kudziwa n’cholinga choti tizitha kusankha zinthu mwanzeru.—Miy. 2:6.
Kuvomereza kuti sitikudziwa zonse kungatithandize ngati mmene kunathandizira Yobu (Onani ndime 2)
3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
3 Munkhaniyi, tikambirana zinthu zina zimene sitikudziwa komanso mavuto amene angakhalepo chifukwa cha zimenezo. Tionanso chifukwa chake ndi bwino kuti pali zina zomwe sitizidziwa. Kukambirana zimenezi kutithandiza kuti tizikhulupirira kuti Yehova, “amene amadziwa chilichonse,” amatiuza zimene timafunikiradi kudziwa.—Yobu 37:16.
SITIKUDZIWA TSIKU LIMENE MAPETO ADZAFIKE
4. Mogwirizana ndi Mateyu 24:36, kodi sitikudziwa chiyani?
4 Werengani Mateyu 24:36. Sitikudziwa tsiku limene mapeto adzafike. Ngakhale pamene Yesu anali padzikoli, sankadziwa za “tsiku limenelo ndi ola lake.”a Pambuyo pake anauza atumwi ake kuti Yehova, yemwe ndi Wosunga Nthawi Wamkulu, amasankha nthawi yochitira zinthu “mu ulamuliro wake,” kapena kuti mogwirizana ndi mmene akufunira. (Mac. 1:6, 7) Yehova anaika nthawi imene adzawononge dzikoli koma ifeyo sitingadziwe nthawi yeniyeni yomwe adzachitire zimenezi.
5. Kodi kusadziwa nthawi yomwe mapeto adzafike kumatikhudza bwanji?
5 Mogwirizana ndi zimene Yesu ananena, sitimadziwa kuti tiyembekezera kwa nthawi yaitali bwanji kuti mapeto afike. Izi zingachititse kuti titaye mtima kapena tifooke, makamaka ngati takhala tikuyembekezera tsiku la Yehova kwa nthawi yaitali. Kapenanso zingamativute kupirira achibale ndi anzathu akamatinyoza chifukwa chakuti mapeto sanafikebe. (2 Pet. 3:3, 4) N’kutheka kuti tingamaganize kuti tikanakhala kuti tikudziwa tsiku lenileni lomwe mapeto adzafike, zikanatithandiza kuti tisataye mtima komanso tizipirira mosavuta.
6. N’chifukwa chiyani ndi bwino kuti sitimadziwa tsiku limene mapeto adzafike?
6 Posatiululira tsiku lomwe mapeto adzafike, Yehova anatipatsa mwayi wosonyeza kuti timamutumikira chifukwa chomukonda komanso kumukhulupirira. Timafuna kutumikira Yehova mpaka kalekale osati kungolekezera pamene mapeto adzafike. M’malo momangoganizira nthawi imene “tsiku la Yehova” lidzafike, tingachite bwino kumaganizira zabwino zomwe zidzachitike pambuyo pa tsikulo. Tikamachita zimenezo, tidzapitiriza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu n’kumayesetsa kuchita zomusangalatsa.—2 Pet. 3:11, 12.
7. Kodi n’chiyani chomwe tikudziwa?
7 Tingachite bwino kumaganizira zomwe tikudziwa, monga zoti masiku otsiriza anayamba mu 1914. Sikuti maulosi a m’Baibulo amene Yehova amafotokoza amangotchula chakachi, koma amafotokozanso mmene zinthu zakhala zikuchitikira kuyambira nthawi imeneyo. Zimenezi zimatithandiza kuti tisamakayikire kuti “tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi.” (Zef. 1:14) Timadziwanso za ntchito imene Yehova amafuna kuti tigwire, yomwe ndi kuuza anthu ambiri mmene tingathere zokhudza “uthenga wabwino uwu wa Ufumu.” (Mat. 24:14) Uthengawu ukulalikidwa m’mayiko pafupifupi 240 komanso m’zilankhulo zoposa 1,000. Sitikufunika kudziwa “tsiku limenelo ndi ola” kuti tizigwira ntchito yofunikayi mwakhama.
SITIDZIWA MMENE YEHOVA ANGACHITIRE ZINTHU
8. Kodi mawu akuti “ntchito ya Mulungu woona” amatanthauza chiyani? (Mlaliki 11:5)
8 Anthufe sitidziwa “ntchito ya Mulungu woona.” (Werengani Mlaliki 11:5.) Mawuwa akunena za zinthu zimene Yehova amazichititsa kapenanso zimene amalola kuti zichitike pofuna kukwaniritsa cholinga chake. Sitingadziwe zifukwa zonse zomwe zachititsa kuti Yehova alole kuti zinazake zichitike kapenanso zimene akufuna kuchita kuti atithandize. (Sal. 37:5) Ntchito ya Mulungu woona ndi yozama kwambiri ndipo sitingathe kuimvetsa. Zili ngati mmene zimakhalira zovuta kudziwa mmene mwana amakulira m’mimba mwa mayi ake, ndipo mpaka pano asayansi sakuzimvetsabe.
9. Kodi kusadziwa zimene Yehova angachite potithandiza kungakhale ndi mavuto ati?
9 Kusadziwa kuti Yehova achita chiyani potithandiza kungachititse kuti tizizengereza posankha zinthu zina. Mwina tingamazengereze kudzimana zinthu zina kuti tizichita zambiri pa utumiki wathu, monga kukhala ndi moyo wosafuna zambiri kapenanso kusamukira kumene kukufunika olalikira Ufumu ambiri. Mwina tingamakayikire ngati Mulungu akusangalala nafe tikamaona kuti sitikukwaniritsa zolinga zathu zauzimu. Tingamakayikirenso ngati sitikuona zotsatira za khama lathu mu utumiki kapenanso tikamakumana ndi mavuto pa ntchito inayake ya gulu yomwe tikugwira.
10. Kodi timakhala ndi makhalidwe ofunika ati chifukwa chosadziwa mmene Yehova atithandizire?
10 Kusadziwa mmene Yehova atithandizire kungachititse kuti tikhale ndi makhalidwe ofunika monga kudzichepetsa. Khalidweli limatithandiza kudziwa kuti maganizo komanso njira za Yehova ndi zapamwamba kuposa zathu. (Yes. 55:8, 9) Limatithandizanso kuti tizimukhulupirira kwambiri komanso kumudalira kuti atithandiza. Zinthu zikatiyendera bwino mu utumiki kapena pa ntchito ya gulu lathu imene tikugwira, timapereka ulemerero kwa Yehova. (Sal. 127:1; 1 Akor. 3:7) Kaya zinthu sizinayende bwino ngati mmene timaganizira, tizikumbukira kuti Yehova akudziwa zonse. (Yes. 26:12) Tizichita mbali yathu n’kumakhulupirira kuti Yehova achita mbali yake. Sitimakayikira kuti iye azitipatsa malangizo amene timafunikira, ngakhale kuti sangachite zimenezo modabwitsa ngati mmene ankachitira kale.—Mac. 16:6-10.
11. Kodi ndi zinthu zofunika ziti zomwe tikudziwa?
11 Timadziwa kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi, wachilungamo komanso wanzeru. Timadziwanso kuti amayamikira zimene timachita pomutumikira komanso zimene timachitira Akhristu anzathu. Timadziwanso kuti nthawi zonse Yehova amadalitsa anthu amene ndi okhulupirika kwa iye.—Aheb. 11:6.
SITIMADZIWA ZIMENE ZICHITIKE MAWA
12. Mogwirizana ndi Yakobo 4:13, 14, kodi sitimadziwa chiyani?
12 Werengani Yakobo 4:13, 14. Mfundo yoona ndi yakuti sitimadziwa zimene zitichitikire mawa. M’dziko loipali tingathe kukumana ndi “nthawi yatsoka komanso zinthu zosayembekezereka.” (Mlal. 9:11) Choncho sitimadziwa ngati zimene takonza zithekedi kapenanso ngati tidzakhale ndi moyo kuti tichite komanso kumalizitsa zomwe takonzazo.
13. Kodi nthawi zina timamva bwanji chifukwa cha zimene zichitike m’tsogolo?
13 Zingakhale zovuta kupirira chifukwa chosadziwa bwinobwino zimene zichitike m’tsogolo. Mwina tingamadere nkhawa kwambiri zimene zichitike ndipo izi zingachititse kuti tisamasangalale. Moyo wathu ungasinthe mosayembekezereka kapenanso zinthu zoipa zingatichitikire mwadzidzidzi ndipo tingafooke. Komanso ngati zimene timayembekezera sizinachitike tingakhumudwe.—Miy. 13:12.
14. Kodi tiyenera kudziwa chiyani kuti tipeze chimwemwe chenicheni? (Onaninso zithunzi.)
14 Kaya tikumane ndi zotani pa moyo wathu, tikamapirira timasonyeza kuti timatumikira Yehova chifukwa chakuti timamukonda. Nkhani za m’Baibulo zimasonyeza kuti sitiyenera kuyembekezera kuti Yehova azititeteza pa mavuto athu onse komanso kuti sanakonzeretu zimene zimachitika pa moyo wathu. Iye amadziwa kuti chimwemwe chathu sichimadalira pa kudziwa zimene zitichitikire m’tsogolo. M’malomwake, timakhala osangalala tikamalola kuti azititsogolera komanso kumumvera. (Yer. 10:23) Tikamamudalira pamene tikusankha zochita, zimakhala ngati tikunena kuti: “Yehova akalola, tikhala ndi moyo ndipo tichita zakutizakuti.”—Yak. 4:15.
Timakhala otetezeka tikamamvera Yehova komanso kulola kuti azititsogolera (Onani ndime 14-15)b
15. Kodi tikudziwa zotani zomwe zichitike m’tsogolo?
15 Ngakhale kuti sitidziwa zimene zichitike tsiku lililonse, timadziwa kuti Yehova anatilonjeza kuti tidzakhala ndi moyo wosatha, kaya kumwamba kapena padzikoli. Timadziwa kuti iye sanganame ndipo palibe chimene chingalepheretse kuti akwaniritse malonjezo ake onse. (Tito 1:2) Iye yekha ndi amene ‘amaneneratu zimene zidzachitike, ndipo kale kwambiri ananeneratu zinthu zimene zidzachitike mʼtsogolo.’ Zinthu zonse zimene ananeneratu kuti zidzachitika m’mbuyomu zinachitikadi ndipo zonse zimene amanena kuti zidzachitika m’tsogolomu zidzachitikanso. (Yes. 46:10) Timadziwa kuti palibe chimene chingalepheretse Yehova kutikonda. (Aroma 8:35-39) Iye adzatitonthoza komanso kutipatsa nzeru ndi mphamvu kuti tithe kupirira zonse zimene tingakumane nazo. Sitimakayikira kuti iye adzatithandiza komanso kutidalitsa.—Yer. 17:7, 8.
SITINGAMVETSE BWINO MMENE YEHOVA AMATIDZIWIRA
16. Monga mmene lemba la Salimo 139:1-6 lasonyezera, kodi Yehova amadziwa chiyani zokhudza ifeyo zomwe sitingamvetse?
16 Werengani Salimo 139:1-6. Mlengi wathu amadziwa mmene anatipangira ndipo amadziwa zimene zimachititsa kuti tizioneka mmene tililimu, komanso tiziganiza kapena kuchita zinthu m’njira inayake. Nthawi zonse iye amachita nafe chidwi. Amadziwa zomwe tikulankhula komanso zimene zili mumtima mwathu, zomwe tikuchita ndiponso chifukwa chake tikuchita zinthuzo. Monga mmene Mfumu Davide ananenera, nthawi zonse Yehova amakhala nafe ndipo ndi wokonzeka kutithandiza. N’zolimbikitsa kudziwa kuti Mlengi wathu wamphamvu, yemwe ndi Ambuye Wamkulu m’chilengedwe chonse, amachita nafe chidwi chonchi. Davide anati: “Zinthu zimenezi ndi zodabwitsa kwambiri kwa ine. Ndi zapamwamba kwambiri moti sindingathe kuzifikira.”—Sal. 139:6, mawu a m’munsi.
17. N’chifukwa chiyani nthawi zina zingativute kuvomereza kuti Yehova amatidziwa bwino?
17 Mwina chifukwa cha chikhalidwe chathu, zimene zinkachitika m’banja lathu kapenanso zimene tinkakhulupirira tisanaphunzire Baibulo, zingativute kuona Yehova ngati Atate wachikondi yemwe amachita nafe chidwi. Kapenanso chifukwa chakuti tinalakwitsapo kwambiri zinthu m’mbuyomu, tingamaone kuti Yehova sangafune kutidziwa kapenanso kukhala nafe pa ubwenzi. Umu ndi mmenenso nthawi zina Davide ankamvera. (Sal. 38:18, 21) Mwinanso munthu yemwe amayesetsa kuti azitsatira mfundo zolungama za Yehova angamadzifunse kuti, ‘Ngati Mulungu amandimvetsa, n’chifukwa chiyani amayembekezera kuti ndisiya kuchita zinthu zina zomwe n’zovuta kwa ine kusiya?’
18. Kodi timapindula bwanji chifukwa chovomereza kuti Yehova amatidziwa bwino kuposa mmene timadzidziwira? (Onaninso zithunzi.)
18 Tingadziphunzitse kuti tizivomereza kuti Yehova amatidziwa bwino kuposa mmene timadzidziwira, komanso amaona zabwino mwa ife zimene eniakefe sitingazione. Ngakhale kuti amaona zimene timalakwitsa, iye amamvetsa chifukwa chake tachita zinazake komanso mmene tikumvera. (Aroma 7:15) Kuzindikira kuti Yehova amatikonda komanso amadziwa zimene tingachite bwino, kungatipatse mphamvu zomwe timafunikira kuti tizimutumikira mokhulupirika ndiponso mosangalala.
Yehova amatithandiza kuti tizipirira mavuto osiyanasiyana omwe timakumana nawo. Iye amachita zimenezi potithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri malonjezo a zinthu zosangalatsa zomwe tikuyembekezera m’dziko latsopano (Onani ndime 18-19)c
19. Kodi ndi zinthu ziti zomwe tikudziwa zomwe sitimakayikira zokhudza Yehova?
19 Timadziwa kuti Yehova ndi chikondi. Sitikayikira ngakhale pang’ono mfundo imeneyi. (1 Yoh. 4:8) Timadziwa kuti mfundo zake zolungama zimasonyeza kuti iye amatikonda komanso amatifunira zabwino. Tikudziwa kuti Yehova amafuna kuti tidzapeze moyo wosatha. Kuti zimenezi zidzatheke iye anapereka dipo. Mphatso ya dipo imatitsimikizira kuti tingathe kumutumikira m’njira imene amafuna ngakhale kuti ndife ochimwa. (Aroma 7:24, 25) Komanso timadziwa kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.” (1 Yoh. 3:19, 20) Yehova amadziwa zonse zokhudza ifeyo ndipo sakayikira kuti tingakwanitse kuchita zimene iye amafuna.
20. N’chiyani chingatithandize kuti tisamadere nkhawa kwambiri zimene sitikudziwa?
20 Yehova amatiuza chilichonse chimene timafunika kudziwa. Tikamavomereza modzichepetsa mfundo imeneyi, sitidera nkhawa zimene sitikuzidziwa. M’malomwake, timaganizira za zinthu zimene ndi zofunika kwambiri. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timadalira kwambiri Yehova, “amene amadziwa chilichonse.” (Yobu 36:4) Panopa sitimatha kumvetsa zinthu zambiri, koma tikuyembekezera nthawi imene tidzatha kuphunzira zinthu zatsopano zokhudza Mulungu wathu wamkulu mpaka kalekale.—Mlal. 3:11.
NYIMBO NA. 104 Mzimu Woyera Ndi Mphatso Yochokera Kwa Mulungu
a Yesu adzatsogolera pa nkhondo yowononga dziko loipa la Satanali. Choncho n’zomveka kunena kuti tsopano akudziwa tsiku la nkhondo ya Aramagedo komanso nthawi imene adzamalize ‘kugonjetsa adani ake.’—Chiv. 6:2; 19:11-16.
b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Bambo ndi mwana wake akulongedza zinthu zomwe banja lawo lingadzafunikire patachitika ngozi.
c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale amene akuoneka kuti wakumana ndi mavuto aakulu akuganizira mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano.