NKHANI YOPHUNZIRA 16
NYIMBO NA. 87 Bwerani Mudzalimbikitsidwe
Kugwirizana ndi Abale ndi Alongo Athu Kumatithandiza
“Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana!”—SAL. 133:1.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi, tiona zimene tingachite kuti tizigwirizana ndi abale ndi alongo athu komanso madalitso omwe timapeza tikamachita zimenezo.
1-2. Kodi Yehova amakhudzidwa ndi chiyani, nanga amafuna kuti tizitani?
YEHOVA amakhudzidwa ndi mmene timachitira zinthu ndi anthu anzathu. Yesu ananena kuti tiyenera kukonda anzathu ngati mmene timadzikondera tokha. (Mat. 22:37-39) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kumakomera mtima ngakhale anthu amene si Akhristu anzathu. Tikamatero timatsanzira Yehova Mulungu yemwe “amawalitsira dzuwa lake anthu abwino ndi oipa omwe, ndipo amagwetsera mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.”—Mat. 5:45.
2 Ngakhale kuti Yehova amakonda anthu onse, iye amakonda kwambiri anthu amene amamumvera. (Yoh. 14:21) Ndipo amafuna kuti tizimutsanzira. Iye amafuna kuti ‘tizikondana kwambiri’ ndi abale ndi alongo athu komanso kuti tiziwasonyeza “chikondi chenicheni.” (1 Pet. 4:8; Aroma 12:10) Chikondi chimene chikufotokozedwa pa lembali, chikufanana ndi chimene timasonyeza m’bale wathu amene timagwirizana naye kapena mnzathu wapamtima.
3. Kodi tizikumbukira chiyani pa nkhani ya chikondi?
3 Chikondi chili ngati maluwa amene amafunika kuwasamalira bwino kuti akule. Mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti: “Pitirizani kukonda abale.” (Aheb. 13:1) Yehova amafuna kuti tipitirize kusonyeza anzathu chikondi. Munkhaniyi, tikambirana chifukwa chake tiyenera kukonda Akhristu anzathu komanso mmene tingapitirizire kuchita zimenezo.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUMAKONDA ANZATHU?
4. Mogwirizana ndi Salimo 133:1, kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira mgwirizano wathu? (Onaninso zithunzi.)
4 Werengani Salimo 133:1. Wolemba masalimo ananena kuti kugwirizana ndi anthu omwe amakonda Yehova ndi ‘kwabwino komanso kosangalatsa’ ndipo zimenezi ndi zoona. Munthu akamaona mtengo waukulu komanso wokongola tsiku lililonse, akhoza kusiya kuuganizira. Zimenezi zikhoza kuchitikanso ndi mgwirizano umene Akhristufe tili nawo. Timaona abale ndi alongo athu pafupipafupi mwinanso kangapo pa mlungu. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timawayamikira? Tikamaona kuti abale ndi alongo ndi ofunika mumpingo komanso kwa ifeyo, tikhoza kuyamba kumawayamikira kwambiri.
Sitiona mopepuka mgwirizano wathu ndi Akhristu anzathu (Onani ndime 4)
5. Kodi anthu ena amakhudzidwa bwanji akaona tikukondana?
5 Anthu ena akafika koyamba pamisonkhano amachita chidwi ndi mmene timakonderana. Zimenezi zimawachititsa kutsimikizira kuti apeza choonadi. Yesu anati: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Chaithra, yemwe anali ku yunivesite ndipo ankaphunzira ndi a Mboni za Yehova. Iye anavomera atalandira kapepala komuitanira kumsonkhano wachigawo. Atapezekapo tsiku loyamba, anauza mlongo amene ankamuphunzitsa Baibulo kuti: “Makolo anga sanandihagepo. Koma pa msonkhanowu, tsiku limodzi lokha anandihanga anthu 52. Ndinamva kuti Yehova akundisonyeza chikondi kudzera m’banja limeneli ndipo nanenso ndikufuna kukhala m’banja limeneli.” Chaithra anapitiriza kuphunzira ndipo anabatizidwa mu 2024. Anthu atsopano akaona ntchito zathu zabwino komanso mmene timakonderana, amayamba kufuna kutumikira Yehova.—Mat. 5:16.
6. Kodi kugwirizana ndi abale ndi alongo athu kumatiteteza bwanji?
6 Kugwirizana ndi abale ndi alongo athu kumatiteteza. Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Pitirizani kulimbikitsana tsiku ndi tsiku . . . kuti chinyengo champhamvu cha uchimo chisaumitse mtima wa aliyense wa inu.” (Aheb. 3:13) Tikakhumudwa n’kuyamba kusochera pa njira yachilungamo, Yehova akhoza kugwiritsa ntchito Mkhristu wina kuti atithandize. (Sal. 73:2, 17, 23) Ndipo tikalimbikitsidwa zinthu zimayambanso kuyenda bwino.
7. Kodi chikondi chimathandiza bwanji kuti tikhale ogwirizana? (Akolose 3:13, 14)
7 Timapeza madalitso ambiri chifukwa chakuti tili m’gulu limene anthu ake amayesetsa kuti azisonyezana chikondi. (1 Yoh. 4:11) Mwachitsanzo, chikondi chimatilimbikitsa kuti ‘tizilolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse’ ndipo zimenezi zimathandiza kuti tizigwirizana. (Werengani Akolose 3:13, 14; Aef. 4:2-6) Choncho tikakhala pa misonkhano timamva bwino kuposa mmene tingamvere titakhala m’gulu lina lililonse padziko lapansi.
TIZISONYEZANA ULEMU
8. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kuti tikhale ogwirizana?
8 Mgwirizano wathu wa padziko lonse ndi wodabwitsa. Yehova amatithandiza kuti tizigwirizana ngakhale kuti si ife angwiro. (1 Akor. 12:25) Baibulo limanena kuti ‘Mulungu amatiphunzitsa kuti tizikondana.’ (1 Ates. 4:9) Zimenezi zikutanthauza kuti kudzera m’Malemba, Yehova amatiuza zimene tiyenera kuchita kuti tizigwirizana. Tikamaphunzira ndi kutsatira malangizo a Mulungu, timakhala tikuphunzitsidwa ndi Mulungu. (Aheb. 4:12; Yak. 1:25) Izi ndi zimene a Mboni za Yehova amayesetsa kuchita.
9. Kodi tikuphunzira chiyani pa Aroma 12:9-13 pa nkhani yosonyezana ulemu?
9 Kodi ndi mfundo ziti za m’Mawu a Mulungu zomwe zimatithandiza kuti tizigwirizana? Taganizirani zimene Paulo ananena pa Aroma 12:9-13. (Werengani.) Mawu amene tikufuna kukambirana ndi akuti “pa nkhani yosonyezana ulemu, muziyamba ndi inuyo.” Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani? Tiyenera kuyamba ndi ifeyo kuwasonyeza anthu ena “chikondi chenicheni” pochita zinthu monga kuwakhululukira, kuwalandira bwino kunyumba kwathu komanso kuwapatsa zinthu. (Aef. 4:32) Sitiyenera kudikira kuti m’bale kapena mlongo ayambe kutisonyeza chikondi. Tiyenera kuyamba ndi ifeyo kuchita zimenezo. M’pomveka kuti Yesu ananena kuti: “Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.”—Mac. 20:35.
10. Kodi tingachite bwanji khama ‘pa nkhani yosonyeza ulemu’? (Onaninso chithunzi.)
10 Chochititsa chidwi ndi chakuti atangonena kuti pa nkhani yosonyezana ulemu tiziyamba ndi ifeyo, Paulo anatilimbikitsanso kuti tikhale “akhama osati aulesi.” Munthu wakhama amalimbikira ntchito ndipo amaigwira ndi mtima wonse. Lemba la Miyambo 3:27, 28 limatilimbikitsa kuti: “Usalephere kuchitira zabwino anthu amene uyenera kuwachitira zabwinozo ngati ungathe kuwathandiza.” Choncho tikaona munthu wina ali pa mavuto timayesetsa kumuthandiza. Sitichita zinthu mozengereza kapena kuganiza kuti munthu wina athandiza.—1 Yoh. 3:17, 18.
Tiziyesetsa kuthandiza abale ndi alongo athu omwe ali pamavuto (Onani ndime 10)
11. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizigwirizana ndi anzathu?
11 Njira ina imene tingasonyezere kuti timalemekeza anzathu ndi kuwakhululukira mwamsanga akatilakwira. Lemba la Aefeso 4:26 limati: “Dzuwa lisalowe mudakali okwiya.” N’chifukwa chiyani vesili limanena zimenezi? Vesi 27 limati, ‘kuti tisamupatse mpata Mdyerekezi.’ M’Mawu ake, Yehova amatiuza mobwerezabwereza kuti tizikhululukirana. Lemba la Akolose 3:13 limatilimbikitsa ‘kupitiriza kukhululukirana ndi mtima wonse.’ Kukhululukira anthu amene atilakwira kumathandiza kwambiri kuti tizigwirizana. Tikamachita zimenezi zimathandiza kuti ‘tisunge umodzi umene timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyera pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chimene chimatigwirizanitsa.’ (Aef. 4:3) Mwachidule tingati kukhululuka kumatithandiza kuti tizigwirizana komanso tizikhala mwamtendere.
12. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kuti tizikhululukira anzathu?
12 N’zoona kuti nthawi zina tingamavutike kukhululukira anthu amene atilakwira. Koma tikhoza kukwanitsa mothandizidwa ndi mzimu woyera. Pambuyo potilimbikitsa kukhala ndi “chikondi chenicheni” komanso “akhama,” Malemba amatilimbikitsanso kuti: “Yakani ndi mzimu.” Munthu amene akuyaka, amakhala wakhama kwambiri mothandizidwa ndi mzimu woyera. Choncho mzimu woyera ungatithandize kuti tizisonyezana chikondi chenicheni komanso tizikhululukirana ndi mtima wonse. N’chifukwa chake timapempha Yehova kuti azitithandiza.—Luka 11:13.
“PAKATI PANU PASAKHALE KUGAWANIKA”
13. Kodi n’chiyani chingachititse kuti tisamagwirizane?
13 Mumpingo mumakhala anthu osiyana mitundu komanso chikhalidwe. (1 Tim. 2:3, 4) Ngati sitingasamale, kusiyana kumeneku kungachititse kuti tizisiyana maganizo pa nkhani monga kuvala, kudzikongoletsa, mankhwala komanso zosangalatsa. (Aroma 14:4; 1 Akor. 1:10) Popeza Mulungu amatiphunzitsa kuti tizikondana, tiyenera kukhala osamala kuti tisamaone kuti maganizo athu ndi abwino kuposa ena.—Afil. 2:3.
14. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
14 Tingathandizenso kuti mumpingo mukhale mgwirizano poyesetsa kukhala olimbikitsa nthawi zonse. (1 Ates. 5:11) Posachedwapa anthu ambiri amene anachotsedwa kapena amene anasiya kusonkhana abwerera mumpingo. Tiyenera kuwalandira mosangalala. (2 Akor. 2:8) Chitsanzo ndi zimene zinachitikira mlongo wina amene anabwerera ku Nyumba ya Ufumu patapita zaka 10. Iye anati: “Aliyense ankandimwetulira komanso kundipatsa moni.” (Mac. 3:19) Kodi mlongoyu anamva bwanji? Iye anati, “Zinandithandiza kudziwa kuti Yehova akundithandiza kuti ndiyambirenso kukhala wosangalala.” Tikamakhala olimbikitsa kwa onse, Khristu akhoza kutigwiritsa ntchito potsitsimula anthu amene ‘akugwira ntchito yotopetsa ndi olemedwa.’—Mat. 11:28, 29.
15. Kodi ndi njira ina iti yomwe tingalimbikitsire mgwirizano? (Onaninso chithunzi.)
15 Zolankhula zathu zikhoza kuthandizanso kuti tizigwirizana. Lemba la Yobu 12:11 limanena kuti: “Kodi si paja khutu limasiyanitsa mawu ngati mmene lilime limasiyanitsira kakomedwe ka chakudya?” Munthu wodziwa kuphika amalawa kaye chakudya chake asanachipereke kwa anthu ena. Ifenso tiyenera kuganizira kaye zimene tikufuna kulankhula tisanazilankhule. (Sal. 141:3) Tizionetsetsa kuti zimene tikufuna kulankhula zizikhala zolimbikitsa, zotsitsimula komanso ‘zothandiza anthu amene akumvetsera.’—Aef. 4:29.
Tiziganiza kaye tisanalankhule (Onani ndime 15)
16. Kodi ndi ndani makamaka amene ayenera kuyesetsa kukhala olimbikitsa?
16 Amuna omwe ali pabanja komanso makolo ayenera kuyesetsa kuti zolankhula zawo zizikhala zolimbikitsa. (Akol. 3:19, 21; Tito 2:4) Akulu, omwenso ndi abusa a nkhosa za Yehova, ayeneranso kukhala olimbikitsa. (Yes. 32:1, 2; Agal. 6:1) Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.”—Miy. 15:23.
“TIZISONYEZANA CHIKONDI CHENICHENI M’ZOCHITA ZATHU”
17. Kodi tingatsimikizire bwanji kuti tili ndi chikondi chenicheni kwa abale ndi alongo athu?
17 Mtumwi Yohane anatilimbikitsa kuti “tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tisizonyezana chikondi chenicheni m’zochita zathu.” (1 Yoh. 3:18) Tiyenera kumakonda abale ndi alongo athu kuchokera pansi pa mtima. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tikamacheza kwambiri ndi abale ndi alongo m’pamene timayamba kukondana komanso kugwirizana kwambiri. Choncho tizipeza mipata yocheza ndi abale ndi alongo pamisonkhano komanso mu utumiki. Tiziyenderanso anthu ena. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti ‘Mulungu akutiphunzitsa kuti tizikondana.’ (1 Ates. 4:9) Tidzaonanso kuti “ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana.”—Sal. 133:1.
NYIMBO NA. 90 Tizilimbikitsana