NKHANI YOPHUNZIRA 15
NYIMBO NA. 30 Atate Wanga, Mulungu Wanga Ndiponso Bwenzi Langa
“Kuyandikira kwa Mulungu Ndi Chinthu Chabwino” kwa Ife
“Koma kwa ine, kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.—SAL. 73:28.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti Yehova akhale mnzathu komanso mmene kuchita zimenezi kumatithandizira.
1-2. (a) Kodi timafunika kuchita chiyani kuti munthu wina akhale mnzathu? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
KODI inuyo muli ndi mnzanu wapamtima? Kodi munayamba bwanji kugwirizana naye? N’kutheka kuti munkacheza naye, kudziwa mavuto amene wakumana nawo, kudziwa zimene amakonda komanso zimene amadana nazo. Mwina munaona kuti ali ndi makhalidwe abwino omwe mumafuna kutsanzira ndipo izi zinachititsa kuti muzimukonda kwambiri.
2 Kuti munthu akhale mnzathu pamafunika nthawi komanso khama. Ndi mmene zililinso ndi ubwenzi wathu ndi Yehova. Munkhaniyi, tikambirana zimene tingachite kuti Yehova akhale mnzathu komanso mmene kuchita zimenezi kumatithandizira. Choyamba, tiyeni tikambirane chifukwa chake tiyenera kuyesetsa kuti Yehova akhale mnzathu wapamtima.
3. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira ubwino wokhala pa ubwenzi ndi Yehova? Perekani chitsanzo.
3 Mosakayikira, mungavomereze kuti kukhala mnzake wa Yehova ndi kwabwino. Koma kuganizira ubwino wokhala mnzake wa Yehova kungatilimbikitse kuti tipitirize kulimbitsa ubwenziwu. (Sal. 63:6-8) Mwachitsanzo, tikhoza kudziwa kuti kudya zakudya zopatsa thanzi, kuchita masewera olimbitsa thupi, kupuma mokwanira komanso kumwa madzi ambiri n’kofunika. Koma anthu ambiri saganizira zinthu zimenezi ndipo sasamalira thanzi lawo. Koma munthu akamaganizira ubwino wochita zinthu zimenezi m’pamene amazichita kwambiri. Mofanana ndi zimenezi, timadziwa kuti kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova n’kwabwino. Koma kuganizira ubwinowo n’kumene kungatilimbikitse kuti tiziyesetsa kulimbitsa ubwenziwu.—Sal. 119:27-30.
4. Kodi mawu a pa Salimo 73:28, akusonyeza kuti wolemba salimoli ankamva bwanji?
4 Werengani Salimo 73:28. Amene analemba Salimo 73 anali Mlevi amene anasankhidwa kuti azikaimba nyimbo pakachisi wa Yehova. Iye ayenera kuti anali atatumikira Yehova kwa nthawi yaitali. Koma pa nthawi ina anafunika kudzikumbutsa komanso kukumbutsa anthu ena kuti “kuyandikira kwa Mulungu” ndi kwabwino kwa iyeyo komanso kwa anthuwo. Kodi ubwino wake ndi wotani?
“KUYANDIKIRA KWA MULUNGU” KUMACHITITSA KUTI TIZISANGALALA
5. (a) N’chifukwa chiyani timasangalala tikakhala pa ubwenzi ndi Yehova? (b) Mogwirizana ndi Miyambo 2:6-16, kodi nzeru za Yehova zingatithandize bwanji, nanga zingatiteteze bwanji?
5 Tikakhala pa ubwenzi ndi Yehova timakhala osangalala kwambiri. (Sal. 65:4) N’chifukwa chiyani zili choncho? Choyamba, zinthu zimatiyendera bwino chifukwa chotsatira malangizo anzeru opezeka m’Mawu ake. Malangizo amenewa amatiteteza kuti tisachite zoipa komanso tisalakwitse kwambiri zinthu. (Werengani Miyambo 2:6-16.) Mpake kuti Baibulo limanena kuti: “Wosangalala ndi munthu amene amapeza nzeru, ndiponso munthu amene amaphunzira zinthu zimene zingamuthandize kukhala wozindikira.”—Miy. 3:13.
6. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti wolemba masalimoyu akhumudwe?
6 N’zoona kuti nthawi zina anzake a Yehova angakhumudwe. Pa nthawi ina amene analemba Salimo 73 anakhumudwa chifukwa choganizira zinthu zolakwika. Iye anakhumudwa chifukwa ankaona kuti anthu oipa omwe sankaopa Mulungu kapena kutsatira mfundo zake zinthu zinkawayendera bwino. Ankaona molakwika kuti anthu achiwawa komanso odzikuza ankakhala olemera, athanzi komanso sakumana ndi mavuto. (Sal. 73:3-7, 12) Iye anasokonezeka maganizo moti pa nthawi ina anayamba kukayikira ngati kutumikira Yehova kunali kwabwino. Chifukwa chokhumudwa iye anati: “Ndithudi, ndayeretsa mtima wanga pachabe, ndipo ndasamba m’manja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wosalakwa.”—Sal. 73:13.
7. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisiye kukhumudwa? (Onaninso chithunzi .)
7 Ngakhale kuti wolemba salimoyu anakhumudwa kwambiri, anachita zinthu zomwe zinamuthandiza kusintha maganizo. Iye anakalowa “m’malo opatulika aulemerero a Mulungu” ndipo Yehova anamuthandiza. (Sal. 73:17-19) Yehova, yemwe ndi mnzathu wapamtima amadziwa tikakhumudwa. Chomwe chimangofunika ndi kupemphera kwa iye komanso kutsatira malangizo amene amatipatsa kudzera m’Mawu ake komanso mumpingo. Tikatero tidzapeza mphamvu kuti tipirire mavuto athu. Ngakhale nkhawa zitatichulukira, Yehova akhoza kutithonthoza n’kutithandiza kukhala osangalala.—Sal. 94:19.a
Mlevi amene analemba Salimo 73, waima “mʼmalo opatulika aulemerero a Mulungu” (Onani ndime 7)
“KUYANDIKIRA KWA MULUNGU” KUMATITHANDIZA KUKHALA NDI MOYO WABWINO KOMANSO CHIYEMBEKEZO
8. Kodi kukhala pa ubwenzi ndi Yehova kumatithandizanso m’njira ziti?
8 Kuyandikira Mulungu kumatithandizanso m’njira zina zofunika. Choyamba, timakhala ndi moyo wabwino. Chachiwiri, timakhala ndi chiyembekezo champhamvu. (Yer. 29:11) Tiyeni tikambirane mfundo ziwirizi bwinobwino.
9. Kodi kukhala pa ubwenzi ndi Yehova kumatithandiza bwanji kuti tikhale ndi moyo wabwino?
9 Tikakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova timakhala ndi moyo wabwino. Anthu ambiri masiku ano omwe sakhulupirira kuti kuli Mulungu, sadziwa chifukwa chake tili ndi moyo, ndipo amaganiza kuti pakapita nthawi anthu onse adzafa. Koma ifeyo taphunzira m’Mawu a Mulungu ndipo timakhulupirira kuti Mulungu “alikodi ndipo amapereka mphoto kwa anthu amene amamufunafuna ndi mtima wonse.” (Aheb. 11:6) Yehova anatilenga kuti tizimutumikira choncho ngakhale masiku ano timakhala osangalala tikamamutumikira.—Deut. 10:12, 13.
10. Mogwirizana ndi Salimo 37:29, kodi anthu amene amadalira Yehova ali ndi chiyembekezo chotani?
10 Anthu ambiri amaona kuti moyo ndi wokhawu womangopita kuntchito, kukhala ndi banja komanso kusunga ndalama zoti adzagwiritse ntchito akadzakalamba. Za Mulungu saganizirako n’komwe. Koma ifeyo timadziwa kuti Yehova amasamalira atumiki ake. (Sal. 25:3-5; 1 Tim. 6:17) Timakhulupirira Mulungu ndipo timadziwa kuti adzakwaniritsa zimene watilonjeza. Tili ndi chiyembekezo chakuti m’tsogolomu tizidzamulambira mpaka kalekale m’Paradaiso.—Werengani Salimo 37:29.
11. Kodi chimachitika n’chiyani tikakhala pa ubwenzi ndi Yehova, nanga iyeyo amamva bwanji?
11 Kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu n’kothandizanso m’njira zina. Mwachitsanzo, Yehova amatilonjeza kuti azitikhululukira tikalapa. (Yes. 1:18) Choncho sitimangokhalira kudziimba mlandu pa zinthu zimene tinalakwitsa kalekale. (Sal. 32:1-5) Ndipo timakhala osangalala tikadziwa kuti tikusangalatsa Yehova. (Miy. 23:15) Kunena zoona, pali madalitso ambiri amene timapeza chifukwa chokhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Koma kodi tingalimbitse bwanji ubwenziwu?
KODI TINGAPITIRIZE BWANJI “KUYANDIKIRA KWA MULUNGU”?
12. Kodi ndi zinthu ziti zimene inuyo mwachita kuti mukhale pa ubwenzi ndi Yehova?
12 Ngati ndinu Mkhristu wobatizidwa, ndiye kuti muli kale pa ubwenzi ndi Yehova. Mwaphunzira mfundo zambiri zoona zokhudza Yehova Mulungu ndi Khristu Yesu, munalapa machimo anu, mumakhulupirira kwambiri Mulungu ndipo mumayesetsa kuchita zimene iye amafuna. Koma kuti tikhalebe mnzake wa Mulungu tiyenera kupitiriza kuchita zimenezi.—Akol. 2:6.
13. Kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene zingatithandize kuti tipitirizebe kukhala pa ubwenzi ndi Yehova?
13 Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhalebe pa ubwenzi ndi Yehova? (1) Tiyenera kupitiriza kuwerenga ndi kuphunzira Mawu a Mulungu. Tikamaphunzira, cholinga chathu chisamangokhala kudziwa mfundo zoyambirira zokhudza Mulungu. Koma tizifufuza zimene Mulungu akufuna kuti tichite, n’kumatsatira mfundo zimene timapeza m’Mawu ake. (Aef. 5:15-17) (2) Tiyenera kuganizira umboni wakuti iye amatikonda kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu. (3) Tiyenera kupitiriza kudana ndi zinthu zimene Yehova amadana nazo komanso kupewa kugwirizana ndi anthu amene amachita zimenezo.—Sal. 1:1; 101:3.
14. Mogwirizana ndi 1 Akorinto 10:31, kodi tingatani kuti tizisangalatsa Yehova tsiku lililonse? (Onaninso zithunzi.)
14 Werengani 1 Akorinto 10:31. Tiyenera kupitiriza kuchita zinthu zimene zimasangalatsa Yehova. Pali zambiri zimene tiyenera kuchita osati kumangolalikira kapena kupezeka pamisonkhano. Zochita zathu tsiku lililonse ziyenera kusangalatsa Yehova. Mwachitsanzo, Yehova amasangalala tikakhala oona mtima pa zinthu zonse komanso kupatsa ena zinthu zathu. (2 Akor. 8:21; 9:7) Iye amasangalalanso tikamasamalira thanzi lathu. Mwachitsanzo, tiyenera kukhala osamala ndi zimene timadya kapena kumwa n’kumachita zinthu zimene zingathandize kuti tikhale athanzi. Yehova amatikonda kwambiri akamaona kuti tikuyesetsa kuchita zinthu zomusangalatsa ngakhale pa zinthu zooneka ngati zazing’ono.—Luka 16:10.
Yehova amasangalala tikamayendetsa galimoto mosamala, kuchita masewera olimbitsa thupi, kudya chakudya chopatsa thanzi komanso kukhala opatsa (Onani ndime 14)
15. Kodi Yehova amafuna kuti tizichita bwanji zinthu ndi anthu ena?
15 Yehova amakomera mtima anthu olungama ndi osalungama omwe. (Mat. 5:45) Iye amafuna kuti ifenso tizichita zinthu moganizira ena. Mwachitsanzo, Mkhristu ayenera kuyesetsa kuti ‘asamanenere zoipa munthu aliyense, ndiponso asamakonde kukangana, koma azikhala wofatsa kwa anthu onse.’ (Tito 3:2) Choncho sitinyoza anthu ena chifukwa chakuti sakhulupirira Yehova. (2 Tim. 2:23-25) Timakhala pa ubwenzi ndi Yehova tikamayesetsa kukhala okoma mtima komanso oganizira anzathu.
TIKHOZA KUKHALA PA UBWENZI NDI YEHOVA NGAKHALE TITALAKWITSA ZINTHU ZINA
16. Kodi wolemba Salimo 73 anayamba kumva bwanji patapita nthawi?
16 Kodi mungatani ngati mutayamba kudziona kuti si inu woyenera kukondedwa ndi Yehova? Monga tanenera kale, munthu yemwe analemba Salimo 73 analinso ndi maganizo amenewa. Iye ananena modandaula kuti: “Mapazi anga anangotsala pang’ono kusochera, mapazi anga anangotsala pang’ono kuterereka.” (Sal. 73:2) Iye ananena kuti mtima ‘unkamupweteka,’ ‘anali wopanda nzeru,’ komanso anali “ngati nyama yosaganiza” pamaso pa Yehova. (Sal. 73:21, 22) Koma kodi anafika poganiza kuti Yehova sangamukondenso chifukwa cha zimene analakwitsa?
17. (a) Kodi wolemba masalimo anachita chiyani pa nthawi imene anakhumudwa kwambiri? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo chake? (Onaninso zithunzi.)
17 Koma sipanapite nthawi yaitali kuti wolemba salimoyu azindikire kuti Yehova sanamutaye. Zikuoneka kuti atakhumudwa kwambiri anazindikira kuti ankafunika kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova. Paja iye ananena kuti: “Koma tsopano ine ndili ndi inu [Yehova] nthawi zonse. Mwandigwira dzanja langa lamanja. Mumanditsogolera ndi malangizo anu ndipo pambuyo pake mudzandipatsa ulemerero.” (Sal. 73:23, 24) Ifenso tikakhumudwa tizipempha Yehova kuti atipatse mphamvu. (Sal. 73:26; 94:18) Ngakhale phazi lathu litaterereka kwa kanthawi, tisamakayikire kuti Yehova ndi thanthwe lathu ndipo ndi “wokonzeka kukhululuka.” (Sal. 86:5) Pa nthawi imene takhumudwa kwambiri m’pamene tiyenera kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu.—Sal. 103:13, 14.
Tikaona kuti chikhulupiriro chathu chayamba kuchepa, tizilimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova pochita zinthu zambiri zokhudza kulambira (Onani ndime 17)
TIDZAPITIRIZA “KUYANDIKIRA KWA MULUNGU” MPAKA KALEKALE
18. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kuyandikira Yehova kulibe malire?
18 Palibe malire pa nkhani ya kuyandikira Mulungu komanso kumudziwa bwino. Baibulo limanena kuti njira za Yehova komanso nzeru zake “ndi zovuta kuzimvetsa.”—Aroma 11:33.
19. Kodi mawu a m’buku la Masalimo amatitsimikizira za chiyani?
19 Lemba la Salimo 79:13, limati: “Ife anthu anu komanso nkhosa zimene mukuweta tidzakuyamikani mpaka kalekale. Ndipo tidzalengeza kuti inu ndi woyenera kutamandidwa ku mibadwomibadwo.” Ifenso tikapitiriza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu tidzalandira madalitso mpaka kalekale ndipo tidzanena kuti: “Mulungu ndi thanthwe la mtima wanga ndiponso cholowa changa mpaka kalekale.”—Sal. 73:26.
NYIMBO NA. 32 Khalani Kumbali ya Yehova
a Anthu ena amene amakhumudwa kapena kuda nkhawa kwa nthawi yaitali angafunike thandizo lakuchipatala. Kuti mudziwe zambiri onani Nsanja ya Olonda, Na. 1 2023.