NKHANI YOPHUNZIRA 29
NYIMBO NA. 87 Bwerani Mudzalimbikitsidwe
Zimene Tingachite Kuti Tizipereka Malangizo Abwino
“Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyangʼanira.”—SAL. 32:8.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi, tiona zimene tingachite kuti tizipereka malangizo othandiza.
1. Kodi ndi ndani amene ayenera kupereka malangizo? Fotokozani.
KODI mumasangalala kupereka malangizo kwa ena? Ena siziwavuta kuchita zimenezi, pomwe ena amazengereza ndipo samva bwino akamapereka malangizo. Kaya zinthu zili bwanji, nthawi ndi nthawi tonsefe timafunika kupereka malangizo. Chifukwa chiyani? Chifukwa Yesu ananena kuti otsatira ake adzadziwika ngati amakondana. (Yoh. 13:35) Ndipo njira imodzi imene tingasonyezere kuti timakonda abale ndi alongo athu, ndi kuwapatsa malangizo ngati pakufunika kutero. Mawu a Mulungu amanena kuti ‘mnzako wabwino ndi amene amakupatsa malangizo mosapita m’mbali.’—Miy. 27:9.
2. Kodi akulu ayenera kukhala okonzeka kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani? (Onaninso bokosi lakuti “Kupereka Malangizo Pamisonkhano ya Mkati Mwa Mlungu.”)
2 Makamaka akulu, ayenera kudziwa mmene angaperekere malangizo othandiza. Yehova ndi Yesu anapereka udindo kwa amuna amenewa, woweta nkhosa mumpingo. (1 Pet. 5:2, 3) Njira imodzi imene akulu amachitira zimenezo, ndi kupereka malangizo ochokera m’Baibulo pokamba nkhani. Iwo amaperekanso malangizo kwa munthu aliyense payekha, ngakhale amene wasochera. Ndiye kodi akulu komanso ena tonsefe, tingatani kuti tizipereka malangizo abwino?
3. (a) Kodi tingatani kuti tikhale mlangizi wabwino? (Yesaya 9:6; onaninso bokosi lakuti “Muzitsanzira Yesu Mukamapereka Malangizo.”) (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
3 Tingaphunzire zambiri pa nkhani yokhala mlangizi wabwino, potengera zitsanzo za anthu otchulidwa m’Baibulo, makamaka Yesu. Dzina lina limene Yesu anapatsidwa ndi lakuti “Mlangizi Wodabwitsa.” (Werengani Yesaya 9:6.) Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite ngati tapemphedwa kuti tipereke malangizo komanso zimene tingachite ngati tikufunika kupereka malangizo tisanapemphedwe. Tikambirananso ubwino wopereka malangizo pa nthawi yoyenera komanso m’njira yoyenera.
WINA AKATIPEMPHA MALANGIZO
4-5. Ngati munthu wina watipempha malangizo, kodi ndi funso liti limene choyamba tiyenera kudzifunsa? Perekani chitsanzo.
4 Kodi tizitani wina akatipempha malangizo? Nthawi zambiri timasangalala ndipo tingafune kupereka malangizowo nthawi yomweyo. Koma choyamba tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndine woyenera kupereka malangizo pa nkhani imeneyi?’ Nthawi zina njira yabwino imakhala kuthandiza munthuyo kupeza munthu wina amene angamupatse malangizo oyenera pa nkhaniyo.
5 Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mnzanu ali ndi matenda aakulu. Ndiye akukuuzani kuti wayamba kufufuza mitundu ya mankhwala amene angalandire, kenako akukufunsani kuti mankhwala abwino ndi ati. Ngakhale kuti pali mankhwala ena amene mungakonde, inu si dokotala ndipo simunaphunzitsidwe kuthandiza odwala. Njira yabwino yomuthandizira mnzanuyo ndi kumufufuzira munthu amene angamuthandize.
6. N’chifukwa chiyani ndi bwino kuyamba tadikira tisanapereke malangizo?
6 Ngakhale titaona kuti ndife oyenera kupereka malangizo pa nkhani inayake, ndi bwino kudikira pang’ono tisanamuyankhe munthu amene watipempha malangizo. Tikutero chifukwa chakuti lemba la Miyambo 15:28 limanena kuti “mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe.” Nanga bwanji ngati tikuona kuti tikudziwa yankho lake? Tikufunikabe kudikira pang’ono kuti tifufuze, kupemphera komanso kuiganizira bwino nkhaniyo. Tikatero tidzatsimikizira kuti yankho lathu likugwirizana ndi maganizo a Yehova. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mneneri Natani.
7. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha mneneri Natani?
7 Polankhula ndi mneneri Natani, Mfumu Davide inanena kuti inkafuna kumangira Yehova kachisi. Mwamsanga Natani anamuuza kuti akhoza kumanga kachisiyo. Komatu choyamba Natani ankafunika kufunsa kwa Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Yehova sankafuna kuti Davide amange kachisiyo. (1 Mbiri 17:1-4) Monga mmene taonera pa nkhani imeneyi, tikapemphedwa malangizo, ndi nzeru kumaganizira kaye ‘tisanalankhule.’—Yak. 1:19.
8. Kodi chifukwa chinanso chotichititsa kukhala osamala tikamapereka malangizo ndi chiti?
8 Tiyeninso tione chifukwa china chotichititsa kukhala osamala tikamapereka malangizo. Ngati zinazake zoipa zitachitika chifukwa cha malangizo amene tapereka, ifenso tingakhale ndi mlandu. Choncho n’zofunika kwambiri kuti tizikhala osamala tisanapereke malangizo.
KUPEREKA MALANGIZO PA NTHAWI IMENE SITINAPEMPHEDWE
9. Kodi akulu ayenera kutsimikizira chiyani asanapereke malangizo? (Agalatiya 6:1)
9 Nthawi ndi nthawi, akulu amafunika kupereka malangizo kwa abale ndi alongo omwe ayamba kulowera “njira yolakwika.” (Werengani Agalatiya 6:1.) Nthawi zina munthu angamasankhe zinthu molakwika, zomwe pambuyo pake zingachititse kuti achite tchimo lalikulu. Cholinga cha akulu ndi kuthandiza munthu kupitirizabe kuyenda panjira ya ku moyo wosatha. (Yak. 5:19, 20) Koma kuti malangizo awo akhale othandiza, choyamba iwo amafunika kutsimikizira ngati munthuyo wayambadi kulowera njira yolakwika. Yehova amalola kuti aliyense azisankha zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima chake. (Aroma 14:1-4) Koma kodi akulu angatani ngati m’baleyo wayambadi kulowera njira yolakwika ndipo akufunika kum’patsa malangizo?
10-12. Kodi akulu angachite chiyani akamapereka malangizo kwa munthu yemwe sanachite kupempha? Perekani chitsanzo. (Onaninso zithunzi.)
10 Sizimakhala zophweka kuti akulu apereke malangizo kwa munthu yemwe sanachite kupempha. N’chifukwa chiyani tikutero? Mtumwi Paulo ananena kuti munthu akhoza kuyamba kulowera njira yolakwika mwiniwakeyo asakudziwa. Choncho akuluwo choyamba amafunika kukonzekeretsa munthuyo kuti alandire malangizowo.
11 Kupereka malangizo pamene sitinapemphedwe kuli ngati kudzala mbewu panthaka yolimba. Mlimi asanadzale mbewu amalima kaye nthakayo. Zimenezi zimathandiza kuti nthakayo ikhale yofewa, yotheka kudzalapo mbewu. Kenako amathirira mbewuyo kuti ikule. Mofanana ndi zimenezi, pali zina zimene mkulu ayenera kuchita akamapereka malangizo asanapemphedwe, n’cholinga choti munthuyo awalandire. Mwachitsanzo, mkuluyo angasankhe nthawi yabwino yoti alankhule ndi munthuyo, n’kumutsimikizira kuti amamufunira zabwino komanso amamukonda kenako n’kumuuza kuti pali zina zimene akufuna kuti akambirane. Mlangizi akamadziwika kuti ndi wachikondi komanso wokoma mtima, zimakhala zosavuta kuti ena alandire malangizo ake.
12 Pokambiranapo, tingati mkuluyo angapitirize kufewetsa nthaka pomukumbutsa kuti aliyense amalakwitsa zinthu ndipo amafunika malangizo nthawi ndi nthawi. (Aroma 3:23) Mkuluyo angamusonyeze m’baleyo modekha komanso mwaulemu, malemba omuthandiza kuona kuti wayamba kulowera njira yolakwika. M’baleyo akazindikira kulakwa kwake, tingati mkuluyo “angadzale mbewu” pomufotokozera momveka bwino zimene ayenera kuchita kuti akonzenso zinthu. Pomaliza, mkuluyo “angathirire” mbewu poyamikira m’baleyo mochokera pansi pamtima komanso kupemphera naye.—Yak. 5:15.
Pamafunika chikondi komanso luso kuti munthu apereke malangizo asanapemphedwe (Onani ndime 10-12)
13. Kodi akulu angatsimikize bwanji kuti munthu wamvetsa malangizo amene akumupatsa?
13 Nthawi zina zingachitike kuti wopereka malangizo akulankhula zinthu zina ndipo amene akupatsidwa malangizoyo akumva zina. Ndiye kodi akulu angatani kuti zimenezi zisamachitike? Iwo angathandize munthuyo kumvetsa zimene akukambirana naye pomufunsa mafunso mwanzeru komanso mwaulemu. (Mlal. 12:11) Mayankho amene angapereke, angathandize mkuluyo kudziwa kuti munthuyo wamvetsa malangizo omwe wamupatsa.
KUPEREKA MALANGIZO PA NTHAWI YOYENERA KOMANSO M’NJIRA YOYENERA
14. N’chifukwa chiyani sitiyenera kupereka malangizo titakwiya? Fotokozani.
14 Tonsefe si angwiro, choncho nthawi zina tingalankhule kapena kuchita zinthu zimene zingakhumudwitse ena. (Akol. 3:13) Mawu a Mulungu amavomereza kuti nthawi zina tingakwiyitsane. (Aef. 4:26) Komabe, tiziyesetsa kuti tisamapereke malangizo titakwiya. Tikutero chifukwa chakuti “munthu amene wakwiya sachita zinthu mogwirizana ndi chilungamo cha Mulungu.” (Yak. 1:20) Tikamapereka malangizo titakwiya, zingangochititsa kuti zinthu ziipe kwambiri. Zimenezi sizikutanthauza kuti sitiyenera kufotokozera maganizo athu munthu amene watikwiyitsa kapenanso mmene tikumvera. Komabe tingachite bwino kudikira kaye mpaka mtima wathu utakhala m’malo kuti tilankhulane bwino. Tiyeni tione chitsanzo cha Elihu yemwe anapereka malangizo abwino kwa Yobu.
15. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Elihu? (Onaninso chithunzi.)
15 Kwa masiku angapo, Elihu ankangomvetsera pamene Yobu ankadziikira kumbuyo poyankha anzake atatu omwe ankamuimba mlandu. Iye ankamumvera chisoni Yobu. Koma Elihu anakwiya chifukwa Yobu analankhula zinthu zina zomwe sizinali zoona zokhudza Yehova, komanso ankangoganizira kwambiri za iye yekha. Ngakhale zinali choncho, Elihu anadikira mpaka nthawi yake yolankhula itakwana ndipo anapereka malangizo kwa Yobu modekha komanso mwaulemu. (Yobu 32:2; 33:1-7) Chitsanzo cha Elihu chikutiphunzitsa mfundo yofunika yakuti, malangizo ayenera kuperekedwa pa nthawi yoyenera ndiponso m’njira yoyenera, mwaulemu komanso mwachikondi.—Mlal. 3:1, 7.
Ngakhale kuti poyamba anakwiya kwambiri, Elihu anapereka malangizo modekha komanso mwaulemu (Onani ndime 15)
PITIRIZANI KUPEREKA KOMANSO KULANDIRA MALANGIZO
16. Kodi tikuphunzira chiyani pa Salimo 32:8?
16 Lemba lotsogolera nkhaniyi likuti ‘Yehova amapereka malangizo komanso kutiyang’anira.’ (Werengani Salimo 32:8.) Zimenezi zikusonyeza kuti iye amapitirizabe kutithandiza. Sikuti amangotipatsa malangizo, koma amatithandizanso kuti tiziwatsatira. Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife. Tikakhala ndi mwayi wopereka malangizo kwa ena, tizitsanzira Yehova popitiriza kuwalimbikitsa komanso kuwathandiza kuti asankhe zinthu mwanzeru.
17. Kodi akulu omwe amapereka malangizo ochokera m’Baibulo akuyerekezeredwa ndi chiyani? Fotokozani. (Yesaya 32:1, 2)
17 Panopa kuposa kale, tiyenera kukhala okonzeka kupereka ndi kulandira malangizo. (2 Tim. 3:1) Akulu amene amapereka malangizo ochokera m’Baibulo ali ngati “mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi.” (Werengani Yesaya 32:1, 2.) Anzathu omwe amadziwa zomwe tikufuna koma n’kutiuza zimene tikufunikira kumva amatipatsa mphatso yamtengo wapatali ngati “maapozi agolide m’mbale zasiliva.” (Miy. 25:11) Tonsefe tiyeni tipitirize kuphunzira zimene tingachite kuti tizipereka komanso kulandira malangizo abwino.
NYIMBO NA. 109 Tizikondana Kwambiri Kuchokera Mumtima