NKHANI YOPHUNZIRA 28
NYIMBO NA. 88 Ndidziwitseni Njira Zanu
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupempha Malangizo?
“Anthu amene amapempha malangizo amakhala ndi nzeru.”—MIY. 13:10.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi, tiona zimene tingachite kuti tizipindula ndi malangizo amene timapatsidwa.
1. Kodi tingatani kuti tizisankha zochita mwanzeru kuti zinthu zitiyendere bwino? (Miyambo 13:10; 15:22)
TONSEFE timafuna kuti tizisankha zochita mwanzeru ndipo timafuna kuti zinthu zizitiyendera bwino. Mawu a Mulungu amatiuza zomwe tingachite kuti zimenezi zitheke.—Werengani Miyambo 13:10; 15:22.
2. Kodi Yehova akutilonjeza chiyani?
2 Tingapeze malangizo komanso nzeru kwa Atate wathu Yehova. Iye amatilonjeza kuti: “Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyangʼanira.” (Sal. 32:8) Yehova samangopereka malangizo n’kusiyira pomwepo. Koma amachita nafe chidwi komanso kutithandiza kudziwa mmene tingagwiritsire ntchito malangizowo.
3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
3 Munkhaniyi, tigwiritsa ntchito Mawu a Mulungu kuti atithandize kupeza mayankho a mafunso 4 awa: (1) Kodi ndiyenera kukhala ndi khalidwe liti kuti malangizo azindithandiza? (2) Kodi ndi ndani angandipatse malangizo abwino? (3) Kodi ndingasonyeze bwanji kuti ndine wokonzeka kulandira malangizo? (4) N’chifukwa chiyani sindiyenera kupempha ena kuti andisankhire zochita?
KODI TIYENERA KUKHALA NDI KHALIDWE LITI?
4. Kodi tiyenera kukhala ndi khalidwe liti kuti tizipindula ndi malangizo?
4 Tiyenera kukhala odzichepetsa kuti tizipindula ndi malangizo. Tizivomerezanso kuti tilibe luso kapenanso kuti tingathe kusankha zinthu zonse mwanzeru patokha. Ndipo ngati si ife odzichepetsa, malangizo alionse omwe tingapeze powerenga Mawu a Mulungu, akhoza kumangolowera khutu ili n’kutulukira khutu linali. (Mika 6:8; 1 Pet. 5:5) Koma ngati ndife odzichepetsa, tikhoza kulandira mosavuta malangizo ochokera m’Baibulo ndipo akhoza kutithandiza.
5. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zikanachititsa Mfumu Davide kukhala wonyada?
5 Tiyeni tione zimene tingaphunzire kwa Mfumu Davide. Iye anachita zinthu zambiri zimene zikanachititsa kuti akhale wonyada. Asanakhale mfumu, iye anali wotchuka chifukwa cha luso lake loimba, mpaka anasankhidwa kuti azikaimbira mfumu. (1 Sam. 16:18, 19) Atasankhidwa kuti akhale mfumu, Yehova anamupatsa mphamvu ya mzimu woyera. (1 Sam. 16:11-13) Iye anatchuka kwambiri atapha adani a Isiraeli kuphatikizapo Goliyati. (1 Sam. 17:37, 50; 18:7) Davide akanakhala wonyada, zimene anachitazi zikanamupangitsa kuganiza kuti safunikanso kupatsidwa malangizo. Koma Davide anali wodzichepetsa.
6. Kodi tikudziwa bwanji kuti Davide ankakonda kulandira malangizo? (Onaninso chithunzi.)
6 Davide atakhala mfumu, anali ndi anzake omwe ankamupatsa malangizo. (1 Mbiri 27:32-34) Zimenezi ndi zosadabwitsa chifukwa kuyambira kale, Davide ankatsatira malangizo. Sikuti iye ankangolandira malangizo kuchokera kwa amuna, koma analandiranso malangizo kuchokera kwa Abigayeli yemwe anali wamkazi. Abigayeli anali mkazi wa Nabala ndipo mwamuna wakeyu anali wopanda ulemu, wosayamika komanso wonyada. Davide anadzichepetsa n’kutsatira malangizo a Abigayeli ndipo anapewa kulakwitsa kwambiri zinthu.—1 Sam. 25:2, 3, 21-25, 32-34.
Modzichepetsa, Davide analandira komanso kugwiritsa ntchito malangizo a Abigayeli. (Onani ndime 6)
7. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Davide? (Mlaliki 4:13) (Onaninso zithunzi.)
7 Tingaphunzire zambiri kuchokera kwa Davide. Mwachitsanzo, tingakhale ndi luso linalake kapena udindo. Koma tisamaganize kuti tikudziwa zonse kapenanso sitikufunikira malangizo. Mofanana ndi Davide, tiyenera kukhala ofunitsitsa kutsatira malangizo posatengera kuti achokera kwa ndani. (Werengani Mlaliki 4:13.) Tikamachita zimenezo, tingapewe mavuto omwe angakhumudwitse ifeyo komanso anthu ena.
Tizikhala ofunitsitsa kumvera malangizo posatengera kuti aperekedwa ndi ndani (Onani ndime 7)c
KODI NDI NDANI ANGATIPATSE MALANGIZO ABWINO?
8. N’chifukwa chiyani Yonatani anali woyenera kupereka malangizo kwa Davide?
8 Tiyeni tikambirane mfundo inanso imene tingaphunzire kwa Davide. Iye anamvera malangizo ochokera kwa anthu amene anali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso omwe ankamvetsa mavuto amene iye ankakumana nawo. Mwachitsanzo, pamene ankafuna kudziwa ngati Mfumu Sauli inkafuna kukhala naye pa mtendere, iye anafunsa malangizo kwa Yonatani yemwe anali mwana wa Sauli. N’chifukwa chiyani Yonatani anatha kupereka malangizo kwa Davide? Chifukwa kuwonjezera pa kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, Yonatani ankamudziwanso bwino Sauli. (1 Sam. 20:9-13) Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani?
9. Kodi tiyenera kupempha malangizo kwa ndani? Fotokozani. (Miyambo 13:20)
9 Tikamafuna malangizo, tizifunsa anthu amene ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso amene akudziwa bwino nkhani imene tikufunika malangizoyo.a (Werengani Miyambo 13:20.) Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti wachinyamata akufuna munthu woyenera kukwatirana naye. Kodi ndani angamupatse malangizo abwino? Mnzake yemwe sali pa banja angathe kumupatsa malangizo othandiza ngati malangizowo akuchokera pa mfundo za m’Baibulo. Koma wachinyamatayo angapeze malangizo abwino komanso othandiza kwambiri ngati atafunsa anthu omwe amamudziwa bwino komanso akhala pa banja kwa zaka zambiri.
10. Kodi tsopano tikambirana chiyani?
10 Takambirana zokhudza anthu amene angatipatse malangizo abwino komanso khalidwe limene tiyenera kukhala nalo. Tsopano tiyeni tikambirane chifukwa chake tiyenera kukhala okonzeka kulandira malangizo komanso chifukwa chake sitiyenera kupempha ena kuti azitisankhira zochita.
KODI NDINGATANI KUTI NDIZIKHALA WOKONZEKA KULANDIRA MALANGIZO?
11-12. (a) Kodi nthawi zina tingachite chiyani? (b) Kodi Mfumu Rehobowamu anachita chiyani pamene ankafunika kusankha zochita pa nkhani yofunika?
11 Nthawi zina munthu angaoneke ngati akufuna kupempha malangizo, pomwe amakhala atasankha kale zochita ndipo akungofuna kudziwa ngati anthu ena akugwirizana ndi maganizo akewo. Munthu woteroyo amakhala kuti sakufuna kulandira malangizo. Iye ayenera kuphunzirapo kanthu pa zimene zinachitikira Mfumu Rehobowamu.
12 Rehobowamu anakhala mfumu ya Isiraeli pambuyo pa Mfumu Solomo. Pamene Rehobowamu anakhala mfumu, Aisiraeli anali ndi zinthu zambiri zabwino. Koma iwo ankaona kuti Solomo ankawagwiritsa ntchito yolemetsa. Choncho anthu anabwera kwa Rehobowamu n’kumuchonderera kuti awapeputsireko mtolo. Rehobowamu anawauza kuti amupatse nthawi yoti aganizire zimene angawayankhe. Iye anayamba bwino chifukwa anafunsa amuna achikulire amene ankathandiza Solomo. (1 Maf. 12:2-7) Koma sanatsatire malangizo amene akuluakuluwo anamupatsa. Chifukwa chiyani? Kodi Rehobowamu anali atasankha kale zimene ankafuna kuchita ndipo ankangofuna anthu oti agwirizane ndi zimene anasankhazo? Ngati ndi choncho, ndiye kuti anasangalala ndi malangizo amene achinyamata anzake anamupatsa. (1 Maf. 12:8-14) Rehobowamu anakawayankha anthuwo mogwirizana ndi malangizo amene achinyamatawo. Zotsatira zake n’zakuti mtunduwo unagawikana ndipo kuchokera nthawi imeneyo, Rehobowamu ankangokumana ndi mavuto.—1 Maf. 12:16-19.
13. Kodi tingadziwe bwanji ngati tili okonzeka kulandira malangizo?
13 Tingaphunzire zambiri pa chitsanzo cha Rehobowamu. Tikapempha ena kuti atipatse malangizo, tizikhala okonzeka kuwalandira. Ndiye kodi tingadziwe bwanji ngati tili okonzeka kulandira malangizo? Tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndimapempha malangizo kenako n’kuwakana mwamsanga chifukwa choti sakugwirizana ndi zimene ndikufuna?’ Tiyeni tione chitsanzo pa nkhaniyi.
14. Tikapatsidwa malangizo, kodi tiyenera kukumbukira chiyani? Perekani chitsanzo. (Onaninso chithunzi.)
14 Tiyerekeze kuti m’bale wina wapeza ntchito ya malipiro abwino. Iye asanakayambe ntchitoyo akupempha malangizo kwa mkulu. Ndiye mkuluyo akukumbutsa m’baleyo mfundo ya m’Baibulo yakuti udindo wake woyamba komanso waukulu ndi kusamalira banja lake mwauzimu. (Aef. 6:4; 1 Tim. 5:8) M’baleyo sakugwirizana ndi zimene mkuluyo wanena choncho akufunsabe abale ena za nkhaniyo mpaka atapeza amene angamuuze zogwirizana ndi maganizo ake. Kodi apa tingati m’baleyo amafunadi malangizo kapena anali atasankha kale zochita? Tizikumbukira kuti mtima wathu ndi wopusitsa kwambiri. (Yer. 17:9) Nthawi zambiri malangizo amene timafunikira ndi amene sitingawakonde.
Kodi tikufunadi malangizo kapena tikungofuna kumva zogwirizana ndi zimene ife tikufuna? (Onani ndime 14)
KODI NDIZIPEMPHA ANTHU ENA KUTI AZINDISANKHIRA ZOCHITA?
15. Kodi sitiyenera kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
15 Tonsefe tili ndi udindo wosankha tokha zochita. (Agal. 6:4, 5) Monga mmene taonera, munthu wanzeru amafufuza malangizo m’Mawu a Mulungu komanso kwa Akhristu olimba mwauzimu asanasankhe zochita. Komabe sitiyenera kupempha ena kuti atisankhire zochita. Ena amafunsa mwachindunji munthu amene amamudalira kuti, “Kodi mukanakhala inuyo mukanatani?” Pomwe ena amangotsanzira zimene ena anachita popanda kuganizira nkhaniyo paokha.
16. Kodi chinachitika n’chiyani ku Korinto pa nkhani ya nyama zimene zinkaperekedwa nsembe kwa mafano, nanga unali udindo wa ndani kusankha kudya kapena kusadya nyamazo? (1 Akor. 8:7; 10:25, 26)
16 Taganizirani zimene zinachitika mumpingo wa ku Korinto pa nkhani ya nyama zimene zinkaperekedwa kwa mafano. Paulo analembera Akhristuwo kuti: “Timadziwa kuti fano si kanthu ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.” (1 Akor. 8:4) Akhristu ena mumpingowo ankaona kuti angathe kudya nyama imene inaperekedwa kwa mafano ndipo pambuyo pake n’kugulitsidwa kumsika. Ena ankaona kuti sangathe kudya nyama ngati imeneyo popanda kuvutitsidwa ndi chikumbumtima chawo. (Werengani 1 Akorinto 8:7; 10:25, 26.) Munthu ankayenera kusankha yekha pa nkhaniyi. Paulo sanalimbikitse kuti Akorinto azisankhira ena zochita kapena kutsanzira zimene ena asankha. Aliyense ankafunika ‘kudzayankha yekha kwa Mulungu.’—Aroma 14:10-12.
17. Kodi chingachitike n’chiyani ngati titamangotengera zimene ena akuchita? Perekani chitsanzo. (Onaninso zithunzi.)
17 Zoterezi zikhoza kuchitikanso masiku ano? Mwachitsanzo, taganizirani nkhani ya tizigawo tamagazi. Mkhristu aliyense ayenera kusankha yekha kulandira kapena kukana tizigawo timeneti.b Mwina zingativute kumvetsa pa nkhani imeneyi. Koma kusankha zochita ndi udindo wa aliyense payekha. (Aroma 14:4) Ngati titangotengera zimene ena asankha, chikumbumtima chathu chikhoza kukhala chofooka. Tingaphunzitse komanso kulimbitsa chikumbumtima chathu tikamachigwiritsa ntchito. (Aheb. 5:14) Ndiye kodi ndi pa nthawi iti pamene tingafunse malangizo kwa Mkhristu wolimba mwauzimu? Tingachite zimenezi pambuyo poti tafufuza patokha koma tikufunabe munthu wina atithandize kumvetsa mfundo za m’Baibulo zogwirizana ndi nkhaniyo.
Tizifufuza kaye patokha tisanapemphe malangizo (Onani ndime 17)
PITIRIZANI KUPEMPHA MALANGIZO
18. Kodi Yehova watichitira chiyani?
18 Yehova wasonyeza kuti amatikhulupirira kwambiri potilola kuti tizisankha tokha zochita. Iye anatipatsa Mawu ake Baibulo kuti lizitithandiza. Komanso watipatsa anzathu anzeru omwe angatithandize kuti tiziganizira mfundo za m’Baibulo. Apatu iye wakwaniritsa udindo wake monga Atate wathu. (Miy. 3:21-23) Ndiye kodi tingatani kuti tizisonyeza kuti timayamikira?
19. Kodi tingatani kuti tipitirize kusangalatsa Yehova?
19 Taganizirani izi: Makolo amasangalala kuona ana awo akukula n’kukhala anzeru, oganiza bwino komanso kukhala atumiki a Yehova okhulupirika. Mofanana ndi zimenezi, Yehova amasangalala akationa tikupitiriza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi iye, kupempha malangizo ake komanso kusankha zinthu zomwe zingachititse kuti iye alemekezedwe.
NYIMBO NA. 127 Mtundu wa Munthu Amene Ndiyenera Kukhala
a Nthawi zina Akhristu angafunse malangizo kwa anthu amene salambira Yehova pa nkhani zokhudza chuma, thandizo lachipatala kapenanso nkhani zina.
b Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, onani phunziro 39 mfundo 5 komanso gawo lakuti “Onani Zinanso” m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale.
c MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mkulu akupereka malangizo kwa mkulu mnzake okhudza mmene analankhulira pamsonkhano wa akulu.