Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 July tsamba 20-25
  • Kodi ‘Mwaphunzira Chinsinsi’ Chokhala Wokhutira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi ‘Mwaphunzira Chinsinsi’ Chokhala Wokhutira?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • TIZIKHALA OYAMIKIRA
  • PITIRIZANI KUKHALA OGANIZA BWINO KOMANSO ODZICHEPETSA
  • MUZIGANIZIRA ZIMENE YEHOVA WALONJEZA
  • “ONSE AMENE AMAMUOPA SASOWA KANTHU”
  • Tizivomereza Modzichepetsa Kuti Sitikudziwa Zonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Muzikumbukira Yehova Yemwe ndi “Mulungu Wamoyo”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Zosankha Zomwe Zimasonyeza Kuti Timadalira Yehova
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Kodi Mumatha Kuzindikira Choonadi?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 July tsamba 20-25

NKHANI YOPHUNZIRA 31

NYIMBO NA. 111 Tili Ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala

Kodi ‘Mwaphunzira Chinsinsi’ Chokhala Wokhutira?

“Ndaphunzira kukhala wokhutira ndi zimene ndili nazo posatengera mmene zinthu zilili pa moyo wanga.”​—AFIL. 4:11.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tiona mmene kuyamikira, kukhala odzichepetsa komanso kuganizira zimene Yehova walonjeza, kungatithandizire kukhala okhutira.

1. Kodi kukhala okhutira kumatanthauza chiyani, nanga sikumatanthauza chiyani?

KODI mumakhala okhutira ndi zimene muli nazo? Munthu wokhutira amakhala wosangalala komanso amakhala ndi mtendere akamaganizira zinthu zabwino zimene Yehova wamupatsa. Iye samakhumudwa kapena kukwiya chifukwa chakuti alibe zinazake. Komabe kukhala okhutira sikumatanthauza kuti tisamadere nkhawa za moyo wathu. Mwachitsanzo, Mkhristu angachite bwino kumaganizira za mipata yomwe angachitire zambiri potumikira Yehova. (Aroma 12:1; 1 Tim. 3:1) Ngakhale zili choncho, iye sakhumudwa akaona kuti sakupeza msanga mwayi wa utumiki umene amayembekezera.

2. Kodi kusakhutira n’koopsa bwanji?

2 Kusakhutira kungayambitse mavuto aakulu. Anthu amene ndi osakhutira, akhoza kumagwira ntchito kwa nthawi yaitali n’cholinga choti apeze zinthu zomwe ndi zosafunika kwenikweni. N’zomvetsa chisoni kuti Akhristu ena amafika poba ndalama kapena zinthu zina zimene amafuna. Iwo angamadziuze kuti, ‘Ndikufunikira chinthu chimenechi,’ ‘Ndadikira kwa nthawi yaitali,’ kapena ‘Ndidzabwezabe ndalamazi.’ Komatu kuba kwa mtundu uliwonse sikusangalatsa Yehova ndipo kumamunyozetsa. (Miy. 30:9) Anthu ena amakhumudwa chifukwa chakuti sakulandira mwayi winawake wa utumiki, moti amafika pongosiya kutumikira Yehova. (Agal. 6:9) N’chiyani chingachititse mtumiki wa Yehova kufika pochita zimenezi? Vuto lingakhale lakuti munthuyo anasiya kukhala wokhutira.

3. Kodi timapeza mfundo yolimbikitsa iti pa Afilipi 4:11, 12?

3 Tonsefe tikhoza kukhala okhutira. Mtumwi Paulo analemba kuti ‘anaphunzira kukhala wokhutira ndi zimene anali nazo posatengera mmene zinthu zinalili pa moyo wake.’ (Werengani Afilipi 4:11, 12.) Iye analemba mawu amenewa ali m’ndende. Ngakhale zinali choncho, iye ankasangalala. Iye anali ‘ataphunzira chinsinsi’ chokhala wokhutira. Ngati zimativuta kukhala wokhutira, mawu a Paulowa komanso zimene zinamuchitikira, zingatithandize kudziwa kuti ifenso tingakhale okhutira posatengera mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Tisamaganize kuti kukhala okhutira ndi kophweka, m’malomwake timachita kufunika kuphunzira. Tiyeni tione makhalidwe amene angatithandize kuphunzira chinsinsi chokhala okhutira.

TIZIKHALA OYAMIKIRA

4. Kodi mtima woyamikira umatithandiza bwanji kuti tizikhala okhutira? (1 Atesalonika 5:18)

4 Nthawi zambiri munthu woyamikira amakhalanso wokhutira. (Werengani 1 Atesalonika 5:18.) Ngati timayamikira zinthu zofunika zomwe timakhala nazo pa moyo, sitingamadandaule za zinthu zimene timazifuna koma sitingazipeze. Tikamayamikira mwayi wa utumiki umene tili nawo, tikhoza kumasangalala komanso kuchita khama pa utumikiwo, m’malo momangoganizira zolandira utumiki wina watsopano. M’pake kuti Malemba amatilimbikitsa kuti tizithokoza Yehova m’mapemphero athu. Mtima woyamikira umatithandiza kukhala ndi “mtendere wa Mulungu umene anthu sangathe kuumvetsa.”​—Afil. 4:6, 7.

5. Kodi ndi zinthu ziti zimene zikanachititsa Aisiraeli kukhala oyamikira? (Onaninso chithunzi.)

5 Taganizirani zimene zinachitikira Aisiraeli. Nthawi zambiri, iwo ankadandaulira Yehova kuti ankasowa chakudya chimene ankadya ku Iguputo. (Num. 11:4-6) N’zoona kuti moyo wa m’chipululu unali wovuta. Ndiye n’chiyani chikanawathandiza kuti akhale okhutira? Iwo ankafunika kuganizira komanso kuyamikira zimene Yehova anali atawachitira kale. Ali ku Iguputo ankazunzidwa ngati akapolo, ndipo Yehova anagwetsera miliri 10 Aiguputo. Aisiraeliwo atamasulidwa, “anatenga zinthu zambiri za Aiguputo” monga siliva, golide ndi zovala. (Eks. 12:35, 36) Iwo atapanikizika pakati pa asilikali a Farao ndi Nyanja Yofiira, Yehova anagawa nyanjayo modabwitsa. Ndipo pamene ankayenda m’chipululu, tsiku lililonse Yehova ankawapatsa mana. Ndiye kodi vuto lawo linali pati? Aisiraeli sankakhutira, osati chifukwa chakuti analibe chakudya, koma sankayamikira zimene anali nazo.

Aisiraeli ena akudandaulira Mose posakhutira ndi mana, pomwe anzawo chapafupi, akupitiriza kutola manawo ndipo akuwayang’ana anzawowo.

N’chifukwa chiyani Aisiraeli anasiya kukhala okhutira? (Onani ndime 5)


6. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhala ndi mtima woyamikira?

6 Ndiye kodi tingatani kuti tikhale ndi mtima woyamikira? Choyamba, tsiku lililonse tizipeza mpata woganizira zinthu zabwino zimene tili nazo. Mungathe kulemba zinthu ziwiri kapena zitatu zimene mukuyamikira. (Maliro 3:22, 23) Chachiwiri, muzichita zinthu zosonyeza kuti ndinu oyamikira. Muziyesetsa kuyamikira zimene ena akuchitirani. Ndipo kuposa zonse, nthawi zonse muziyamikira Yehova. (Sal. 75:1) Chachitatu, muzikhala ndi anzanu omwe ndi oyamikira. Ngati anzathu ndi oyamikira ifenso tingakhale oyamikira, koma ngati ndi osayamikira, tingatengerenso khalidwe limenelo. (Deut. 1:26-28; 2 Tim. 3:1, 2, 5) Tikamaganizira mipata yoti tiyamikire ena sitingakhumudwe chifukwa chakuti takumana ndi mavuto enaake kapena tilibe zinazake.

7. Kodi n’chiyani chinathandiza Aci kuti akhale ndi mtima woyamikira, nanga zotsatirapo zake zinali zotani?

7 Taganizirani zimene zinachitikira Aci yemwe amakhala ku Indonesia. Iye anati: “Pa nthawi ya mliri wa COVID-19, ndinayamba kumayerekezera mmene zinthu zinalili pa moyo wanga ndi wa Akhristu anzanga. Zimenezi zinachititsa kuti ndiyambe kukhala ndi mtima wosakhutira.” (Agal. 6:4) Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti asinthe maganizo? Aci anati: “Ndinayamba kuganizira madalitso omwe ndinkapeza tsiku lililonse komanso zabwino zimene ndinapeza chifukwa chokhala m’gulu la Yehova. Ndiyeno ndinayamikira Yehova chifukwa cha zimenezo. Pambuyo pake ndinayambiranso kukhala wokhutira.” Ngati inunso simukusangalala chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wanu, zimene Aci anachita zingakuthandizeni kuti muyambirenso kukhala ndi mtima woyamikira.

PITIRIZANI KUKHALA OGANIZA BWINO KOMANSO ODZICHEPETSA

8. Kodi n’chiyani chomwe chinachitikira Baruki?

8 Pa nthawi ina, mlembi wa Yeremiya dzina lake Baruki sankakhutira ndi mmene zinthu zinalili pa moyo wake. Iye anali ndi ntchito yovuta yothandiza mneneri Yeremiya pamene ankapereka uthenga wamphamvu kwa Aisiraeli omwe anali osayamika. Kwa kanthawi, Baruki anasiya kuganiza bwino. M’malo moganizira kwambiri zimene Yehova ankafuna kuti iye achite, anayamba kuganizira kwambiri zofuna zake. Kudzera mwa Yeremiya, Yehova anauza Baruki kuti: “Iwe ukufunafuna zinthu zazikulu. Leka kufunafuna zinthu zimenezo.” (Yer. 45:3-5) Apa zinali ngati akumuuza kuti, “Uzikhutira ndi mmene zinthu zilili pa moyo wako panopa.” Baruki anatsatira malangizowa ndipo anapitiriza kutumikira Yehova mosangalala.

9. Mogwirizana ndi 1 Akorinto 4:6, 7, kodi kudzichepetsa kumatithandiza kuzindikira chiyani? (Onaninso zithunzi.)

9 Nthawi zina Mkhristu angamaone kuti amayenera kupatsidwa mwayi winawake wa utumiki. Iye akhoza kukhala waluso, wakhama kapenanso wodziwa zambiri. Koma ena angapatsidwe utumiki umene iye amalakalaka. Ndiye kodi n’chiyani chingamuthandize kuti asakhumudwe? Iye angachite bwino kuganizira zimene mtumwi Paulo analemba pa 1 Akorinto 4:6, 7. (Werengani.) Utumiki uliwonse umene tingapatsidwe komanso luso lililonse lomwe tingakhale nalo zimachokera kwa Yehova. Yehova sanatipatse mphatso zimenezi chifukwa chakuti ndife apadera kuposa ena. M’malomwake amatipatsa mphatsozi chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu.​—Aroma 12:3, 6; Aef. 2:8, 9.

Zithunzi: Abale ndi alongo omwe ali ndi mwayi wochita utumiki wosiyanasiyana. 1.M’bale akuona mmene mapaipi alili pamalo olambirira. 2. Mlongo akufunsidwa mafunso pamsonkhano wadera wa chilankhulo chamanja. 3. M’bale akukamba nkhani pamsonkhano wampingo.

Yehova anatipatsa mphatso iliyonse yomwe tili nayo chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu (Onani ndime 9)a


10. Kodi tingatani kuti tikhale odzichepetsa?

10 Tingakhale odzichepetsa tikamaganizira kwambiri chitsanzo chimene Yesu anatipatsa. Taganizirani zimene zinachitika pa usiku umene iye anasambitsa mapazi a ophunzira ake. Mtumwi Yohane analemba kuti: ‘Yesu ankadziwa kuti [1] Atate anapereka zinthu zonse mʼmanja mwake komanso [2] kuti anabwera kuchokera kwa Mulungu ndiponso [3] kuti ankapita kwa Mulungu. Choncho . . . anayamba kusambitsa mapazi a ophunzirawo.’ (Yoh. 13:3-5) Yesu akanatha kumaona kuti atumwi akewo ndi amene ankafunika kumusambitsa mapazi. Koma iye ali padzikoli sanaganizepo zoti ankafunika kukhala moyo wapamwamba kapena wawofuwofu. (Luka 9:58) Yesu anali wodzichepetsa komanso wokhutira ndipo anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri.​—Yoh. 13:15.

11. Kodi kudzichepetsa kwathandiza bwanji Dennis kuti azikhala wokhutira?

11 Dennis yemwe kwawo ndi ku Netherlands, wakhala akuyesetsa kutsanzira Yesu pokhala wodzichepetsa, koma si nthawi zonse pomwe zinali zophweka. Iye anati: “Nthawi zina ndimaona kuti ndimakhumudwa kapenanso kuyamba kusonyeza mtima wosakhutira, mwachitsanzo, munthu wina akapatsidwa utumiki womwe ndimaufuna. Zoterezi zikachitika ndimaphunzira nkhani zokhudza kudzichepetsa. Ndinasonkhanitsa mu JW Library® malemba ena okhudza kudzichepetsa n’cholinga choti ndiziwapeza mwamsanga n’kumawawerenga mobwerezabwereza. Mu foni yanga ndinachitanso dawunilodi nkhani zokhudza kudzichepetsa zomwe ndimazimvetsera pafupipafupi. Ndaphunzira kuti ntchito iliyonse imene timagwira, cholinga chake n’chakuti tipereke ulemerero kwa Yehova osati ifeyo. Aliyense wa ife amangochita kambali kochepa pothandiza kuti Yehova akwaniritse cholinga chake.” Mukaona kuti simukukhalanso wokhutira chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wanu, yesetsani kuti muyambe kukhala wodzichepetsa. Zimenezi zidzakuthandizani kuti mukhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova komanso mukhale wokhutira.​—Yak. 4:6, 8.

MUZIGANIZIRA ZIMENE YEHOVA WALONJEZA

12. Kodi ndi zinthu ziti zimene Yehova walonjeza zomwe zingatithandize kuti tizikhala wokhutira? (Yesaya 65:21-25)

12 Kuganizira zimene tikuyembekezera m’tsogolomu kumatithandiza kukhala okhutira. Mawu a Yehova omwe mneneri Yesaya analemba, amavomereza kuti masiku ano moyo ndi wovuta ndipo amatitsimikizira kuti Yehova adzathetsa mavuto onsewa. (Werengani Yesaya 65:21-25.) Tizidzakhala m’nyumba zabwino komanso zotetezeka. Tizidzagwira ntchito yabwino komanso tizidzadya chakudya chokoma ndi chopatsa thanzi. Sitidzaopa kuti zoipa zinazake zitichitikira ifeyo kapena ana athu. (Yes. 32:17, 18; Ezek. 34:25) Sitimakayikira ngakhale pang’ono kuti zimenezi zidzachitikadi.

13. Kodi ndi pa nthawi iti makamaka, pamene tingafunike kuganizira za zimene Yehova walonjeza?

13 Kuposa kale, panopa tiyenera kumaganizira kwambiri zimene Yehova watilonjeza. Tikutero chifukwa tikukhala “m’masiku otsiriza” ndipo tikhoza kukumana ndi zinthu zovuta kwambiri. (2 Tim. 3:1) Tsiku lililonse Yehova amatithandiza kupirira potipatsa malangizo, mphamvu komanso thandizo lililonse limene tingafunikire. (Sal. 145:14) Kuwonjezera pamenepo, zimene Yehova watilonjeza zimatithandiza kupirira mavuto amene timakumana nawo pa moyo wathu. N’kutheka kuti panopa mumavutika kupeza zinthu zofunika pabanja lanu. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti muzingovutika mpaka kalekale? Ayi. Yehova akulonjeza kuti adzakupatsani zinthu zambirimbiri zimene mumafunikira m’Paradaiso. (Sal. 9:18; 72:12-14) Mwina mukudwala matenda aakulu, mukuvutika maganizo kapenanso mukuvutika chifukwa cha ukalamba. Kodi umu ndi mmene moyo wanu ukuyenera kukhalira mpaka kalekale popanda chiyembekezo chilichonse? Ayi. Matenda komanso imfa zidzatha m’dziko latsopano. (Chiv. 21:3, 4) Chiyembekezo chimenechi chimatithandiza kuti tizikhala okhutira ndipo sitimakhumudwa kapena kukwiya chifukwa cha mmene zinthu zilili panopa. Tingathe kukhalabe okhutira ngakhale titakumana ndi zopanda chilungamo, kudwala matenda aakulu, kuferedwa kapenanso kukumana ndi mayesero alionse. Tikutero chifukwa kaya zinthu zili bwanji panopa, “mavuto amene tikukumana nawo ndi akanthawi” ndipo adzatheratu m’dziko latsopano lomwe layandikira kwambiri.​—2 Akor. 4:17, 18.

14. Kodi n’chiyani chomwe chingatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri zimene Yehova walonjeza?

14 Popeza kuti zimene Yehova watilonjeza zimatithandiza kuti tikhale okhutira, kodi tingatani kuti chiyembekezo chathu chikhale cholimba? Mofanana ndi munthu yemwe amavala magalasi kuti aone bwino zinthu zimene zili patali, ifenso tiyenera kuchita zinthu zina kuti tilimbitse chiyembekezo chathu n’cholinga choti tiziona bwino zinthu zimene zikubwera m’tsogolo m’Paradaiso. Mwachitsanzo, tikamadera nkhawa nkhani zokhudza ndalama, tiziganizira mmene moyo udzakhalire pa nthawi imene ndalama, ngongole kapena kusiyana pa nkhani zachuma kudzakhale kutatha. Tikakhumudwa chifukwa chakuti sitinapatsidwe utumiki winawake, tiziganizira mmene nkhawa zimenezi zidzakhalire zosafunika pambuyo poti takhala angwiro n’kumatumikira Yehova kwa zaka zambiri. (1 Tim. 6:19) N’zoona kuti panopa timadera nkhawa za zinthu zambiri, zomwe zimachititsa kuti zizitivuta kuganizira za malonjezo a m’tsogolo. Koma nthawi ikamapita tingayambe kuona kuti n’zosavuta kumaganizira za zinthu zimene Yehova watilonjeza.

15. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Christa ananena?

15 Taganizirani mmene chiyembekezo chinathandizira Christa, amene ndi mkazi wa Dennis tamutchula kale uja. Iye anati: “Ndili ndi matenda omwe amachititsa kuti minofu yanga izifooka moti ndimagwiritsa ntchito njinga ya olumala komanso nthawi zambiri ndimakhala ndili chigonere. Tsiku lililonse ndimakhala ndikumva ululu waukulu. Posachedwapa dokotala wanga anandiuza kuti ndisayembekezere kuti zinthu zikhala bwino. Koma mwamsanga ndinaganiza kuti, ‘Dokotalayu sakuona zam’tsogolo ngati mmene ineyo ndimaonera.’ Ine ndili ndi chiyembekezo chomwe chimandipatsa mtendere wa mumtima. Panopa ndiyenera kupirira koma ndidzasangalala kwambiri m’dziko latsopano.”

“ONSE AMENE AMAMUOPA SASOWA KANTHU”

16. N’chifukwa chiyani Mfumu Davide analemba kuti amene amaopa Yehova “sasowa kanthu”?

16 Mtumiki wa Yehova amene ndi wokhutira amakumanabe ndi mavuto. Taganizirani za Mfumu Davide. Iye anaferedwapo ana atatu, ananeneredwa zinthu zabodza, anzake ena anamusiya komanso kwa zaka zambiri ankasakidwa kuti aphedwe. Ngakhale kuti anakumana ndi mavuto onsewa, ponena za Yehova, Davide anati: “Onse amene amamuopa sasowa kanthu.” (Sal. 34:9, 10) N’chifukwa chiyani ananena zimenezi? Chifukwa iye ankadziwa kuti monga anthu a Yehova, sitimayembekezera kuti sitizikumana ndi mavuto, koma timakhala otsimikiza kuti iye atipatsa zimene tikufunikira. (Sal. 145:16) Komanso timamudalira kuti atithandiza kupirira mayesero athu onse. Choncho tingathe kukhala okhutira.

17. N’chifukwa chiyani mukufunitsitsa kudziwa chinsinsi chokhala okhutira?

17 Yehova amafuna kuti muzikhala okhutira. (Sal. 131:1, 2) Choncho muyenera kuyesetsa kuti mudziwe chinsinsi chokhala okhutira. Mukamachita khama kuti mukhale ndi mtima woyamikira, kukhala oganiza bwino ndi odzichepetsa komanso kumakhulupirira kwambiri zimene Yehova walonjeza, mudzatha kunena kuti: “Inde, ndikukhutira.”​—Sal. 16:5, 6.

KODI MFUNDO ZOTSATIRAZI ZINGAKUTHANDIZENI BWANJI KUKHALA OKHUTIRA?

  • Kuyamikira

  • Kukhala oganiza bwino komanso kudzichepetsa

  • Kuganizira zimene Yehova walonjeza

NYIMBO NA. 118 “Tiwonjezereni Chikhulupiriro”

a MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akukonza zinthu pamalo olambirira, mlongo yemwe anaphunzira chilankhulo chamanja akufunsidwa mafunso pamsonkhano wadera, ndipo m’bale akukamba nkhani ya onse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena