NKHANI YOPHUNZIRA 32
NYIMBO NA. 38 Adzakulimbitsa
Kodi Yehova Amatithandiza Bwanji Kupirira?
“Mulungu yemwe amasonyeza kukoma mtima konse kwakukulu . . . adzakupatsani mphamvu, adzakuthandizani kuti mukhalebe okhulupirika komanso adzakulimbitsani.”—1 PET. 5:10.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi, tiona zinthu zimene Yehova watipatsa kuti tizipirira komanso tiona zomwe tingachite kuti zinthu zimenezi zizitithandiza.
1. N’chifukwa chiyani tiyenera kupirira, nanga ndi ndani angatithandize? (1 Petulo 5:10)
M’MASIKU otsiriza ano, anthu a Yehova akupirira mavuto osiyanasiyana. Ena akudwala matenda aakulu, ena ali ndi chisoni chifukwa choti munthu yemwe amamukonda anamwalira, pomwe enanso amatsutsidwa ndi achibale awo kapena boma. (Mat. 10:18, 36, 37) Ndiye kaya inuyo mukukumana ndi mavuto otani, musamakayikire kuti Yehova adzakuthandizani kupirira.—Werengani 1 Petulo 5:10.
2. Monga Akhristu, kodi n’chiyani chimatithandiza kupirira?
2 Kupirira kumatanthauza kukhalabe okhulupirika kwa Yehova, n’kumamutumikirabe mosangalala ngakhale tikukumana ndi mavuto, kuzunzidwa kapenanso mayesero. Akhristufe sitingathe kupirira patokha. M’malomwake, Yehova ndi amene amatipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa.” (2 Akor. 4:7) Munkhaniyi tikambirana zinthu 4 zimene Yehova watipatsa potithandiza kuti tizipirira komanso mmene zingatithandizire.
PEMPHERO
3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti pemphero ndi chinthu chodabwitsa?
3 Pemphero ndi chinthu chodabwitsa chomwe Yehova watipatsa potithandiza kuti tizipirira. Iye wachititsa kuti tizitha kulankhula naye ngakhale kuti ndife ochimwa. (Aheb. 4:16) Tangoganizani, tingathe kupemphera kwa Yehova pa nthawi iliyonse komanso pa nkhani iliyonse. Iye akhoza kutimva m’chilankhulo chilichonse komanso kulikonse, ngakhale pamene tili kwatokha kapena m’ndende. (Yona 2:1, 2; Mac. 16:25, 26) Pamene tili ndi nkhawa ndipo sitikudziwa mmene tingafotokozere zimene tikufuna, Yehova amadziwa zomwe tikufuna kulankhula. (Aroma 8:26, 27) Kunena zoona, pemphero ndi njira yodabwitsa yolankhulirana ndi Yehova.
4. N’chifukwa chiyani mapemphero athu opempha Yehova kuti atithandize kupirira amakhala ogwirizana ndi chifuniro chake?
4 Yehova amatitsimikizira m’Mawu ake kuti “chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi zimene amafuna, amatimvera.” (1 Yoh. 5:14) Ndiye kodi tingapemphe Yehova kuti atithandize kupirira? Inde, kuchita zimenezi n’kogwirizana ndi chifuniro chake. Tikutero chifukwa tikamapirira mayesero, timamuthandiza Yehova kuyankha Satana Mdyerekezi yemwe amamutonza. (Miy. 27:11) Kuwonjezera pamenepo, Baibulo limati Yehova ndi wofunitsitsa kuti “aonetse mphamvu zake kwa anthu odzipereka ndi mtima wonse kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Choncho sitimakayikira kuti Yehova ali ndi mphamvu komanso amafunitsitsa kutithandiza kuti tizipirira.—Yes. 30:18; 41:10; Luka 11:13.
5. Kodi pemphero lingatithandize bwanji kupeza mtendere wamumtima? (Yesaya 26:3)
5 Baibulo limanena kuti mukamapemphera mochokera pansi pa mtima, “mtendere wa Mulungu umene anthu sangathe kuumvetsa, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.” (Afil. 4:7) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Anthu amene satumikira Yehova, nawonso amakumana ndi mavuto ndipo amayesa njira zosiyanasiyana zomwe zingawathandize kupeza mtendere wamumtima. Mwachitsanzo, anthu ena amayesa kudzichititsa kuti asaganizire chilichonse kuphatikizapo zinthu zimene zikuwadetsa nkhawa. Komatu kuchita zimenezi n’kowopsa chifukwa kusiya kuganizira chilichonse kungachititse kuti ziwanda zipezerepo mwayi. (Yerekezerani ndi Mateyu 12:43-45.) Kuwonjezera pamenepo, mtendere umene Yehova amatipatsa tikapempha, umaposa mtendere uliwonse womwe anthu angapeze m’njira zosiyanasiyana. Tikamapemphera kwa Yehova timasonyeza kuti timamudalira kwambiri ndipo iye amatipatsa “mtendere wosatha.” (Werengani Yesaya 26:3.) Njira imodzi yomwe Yehova amatipatsira mtendere ndi kutithandiza kukumbukira malemba otonthoza omwe tinawerenga m’Baibulo. Malemba amenewo amatithandiza kukhazikitsa mtima pansi chifukwa timadziwa kuti Yehova amatisamalira ndipo amafuna kuti zinthu zizitiyendera bwino.—Sal. 62:1, 2.
6. Kodi tingatani kuti pemphero lizitithandiza kwambiri? (Onaninso chithunzi.)
6 Zimene mungachite. Mukamapirira mayesero enaake, ‘muzimutulira Yehova nkhawa zanu’ ndipo muzimupempha kuti akupatseni mtendere. (Sal. 55:22) Muzipemphanso nzeru zomwe zingakuthandizeni kulimbana ndi mayeserowo. (Miy. 2:10, 11) Mukamapemphera kuti akuthandizeni kupirira, musamaiwalenso kumuthokoza. (Afil. 4:6) Muzikhala tcheru kuti muziona njira zimene Yehova akukuthandizirani kupirira ndipo muzimuthokoza chifukwa cha zimenezo. Mayesero amene mukukumana nawo, asamakulepheretseni kuona madalitso amene Yehova wakupatsani kale.—Sal. 16:5, 6.
Mukamapemphera mumakhala mukulankhula ndi Yehova, ndipo mukamawerenga Baibulo iye amakhala akulankhula nanu (Onani ndime 6)b
MAWU A MULUNGU
7. Kodi kuphunzira Baibulo kungatithandize bwanji kuti tizipirira?
7 Yehova anatipatsa Mawu ake kuti azitithandiza kupirira. M’Baibulo muli mavesi ambiri omwe amatitsimikizira kuti Yehova amatithandiza. Chitsanzo ndi lemba la Mateyu 6:8, limene limati: “Atate wanu amadziwa zimene mukufunikira musanamupemphe nʼkomwe.” Yesu ndi amene analankhula mawuwa ndipo iye amamudziwa bwino Yehova kuposa wina aliyense. Choncho sitiyenera kukayikira kuti Yehova amatiganizira tikamakumana ndi mavuto. M’Baibulo mulinso malemba ena ambiri omwe angatithandize kuti tipitirize kupirira.—Sal. 94:19.
8. (a) Kodi ndi mfundo imodzi iti ya m’Baibulo yomwe ingatithandize kupirira? (b) N’chiyani chingatithandize kukumbukira mfundo za m’Baibulo pamene tikuzifunikira?
8 Mfundo za m’Baibulo zimatithandiza kupirira tikakumana ndi mavuto. Koposa zonse, mfundozi zimatipatsa malangizo othandiza omwe amatithandiza kuti tizisankha zochita mwanzeru. (Miy. 2:6, 7) Mwachitsanzo, Baibulo limatilimbikitsa kuti tisamadere nkhawa kwambiri zinthu zimene zichitike m’tsogolo, m’malomwake tsiku lililonse tizidalira Yehova. (Mat. 6:34) Tikamawerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku komanso kuwaganizira mozama, zingakhale zosavuta kukumbukira mfundo zimene zingatithandize pa nthawi imene tikuzifunikira.
9. Kodi nkhani za m’Baibulo zimatithandiza bwanji kuti tizikhulupirira kuti Yehova atithandiza kupirira?
9 M’Baibulo mulinso nkhani za anthu ngati ife tomwe, amene anadalira Yehova ndipo iye anawathandiza. (Aheb. 11:32-34; Yak. 5:17) Kuganizira nkhani ngati zimenezi kumatithandiza kuti tizikhulupirira kuti Yehova ndi “pothawira pathu komanso mphamvu yathu, thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya mavuto.” (Sal. 46:1) Tikamaona mmene atumiki okhulupirika akale anasonyezera chikhulupiriro, zimatilimbikitsa kuti tizitsanzira chikhulupiriro chawo ndi kupirira kwawo.—Yak. 5:10, 11.
10. Kodi mungatani kuti Mawu a Mulungu azikuthandizani kwambiri?
10 Zimene mungachite. Muziwerenga Baibulo tsiku lililonse ndipo muzisunga malemba amene mukuona kuti angakuthandizeni. Anthu ambiri amaona kuti kuwerenga lemba latsiku m’mawa, kumawathandiza kuti aziganizira zinthu zolimbikitsa tsiku lonse. Mlongo wina dzina lake Mariea anaona kuti zimenezi zinamuthandiza pa nthawi imene makolo ake onse awiri anapezeka ndi khansa. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kupirira pamene ankawasamalira m’masiku omaliza a moyo wawo? Iye anati, “M’mawa uliwonse ndinkawerenga lemba latsiku komanso kuliganizira. Zimenezi zinandithandiza kuti ndiziganizira zokhudza Yehova komanso mfundo za m’Malemba m’malo momangoganizira mavuto omwe ndinkakumana nawo.”—Sal. 61:2.
AKHRISTU ANZATHU
11. Kodi kudziwa kuti abale ndi alongo athu akukumananso ndi mavuto kumatilimbikitsa bwanji?
11 Yehova anatipatsa abale ndi alongo padziko lonse kuti azitithandiza kupirira. Timalimbikitsidwa “podziwa kuti abale ndi alongo [athu] padziko lonse akukumananso ndi mavuto.” (1 Pet. 5:9) Zimenezi zikutanthauza kuti kaya tikukumana ndi zotani, enanso akukumana ndi mavuto ngati omwewo ndipo akupirira. Choncho ifenso tingathe kupirira.—Mac. 14:22.
12. Kodi Akhristu anzathu angatithandize bwanji, nanga ifeyo tingawathandize bwanji? (2 Akorinto 1:3, 4)
12 Abale ndi alongo athu akhoza kutilimbikitsa tikakumana ndi mavuto. Izi ndi zimene zinachitikiranso mtumwi Paulo. Nthawi zambiri iye ankayamikira anthu omwe ankamuthandiza pa nthawi yomwe anali pa ukaidi wosachoka panyumba, moti ankawatchula mayina. Iwo ankamulimbikitsa, kumutonthoza komanso kumupatsa zinthu zimene ankafunikira. (Afil. 2:25, 29, 30; Akol. 4:10, 11) Zoterezi zikhoza kuchitikanso masiku ano. Abale ndi alongo athu amatithandiza kupirira tikakumana ndi mavuto ndipo nawonso akakumana ndi mavuto nafenso timawathandiza.—Werengani 2 Akorinto 1:3, 4.
13. Kodi n’chiyani chinathandiza Maya kuti apirire?
13 Abale ndi alongo a ku Russia analimbikitsa mlongo wina dzina lake Maya. Mu 2020, apolisi anakachita chipikisheni m’nyumba yake ndipo pambuyo pake anaimbidwa mlandu chifukwa chouza ena zimene amakhulupirira. Maya anati: “Pa nthawi imene ndinkada nkhawa kwambiri abale ndi alongo ankandiimbira foni, komanso kundilembera mameseji ndi makalata onditsimikizira kuti amandikonda. M’mbuyo monsemu ndinkadziwa kuti abale ndi alongo amandikonda ndipo ali ngati anthu a m’banja langa. Koma kuchokera mu 2020, m’pamene ndinatsimikizira kwambiri za mfundo imeneyi.”
14. Kodi tingatani kuti tizipindula ndi zimene Akhristu anzathu amachita potithandiza? (Onaninso chithunzi.)
14 Zimene mungachite. Mukamakumana ndi mavuto muzikhala pafupi ndi abale ndi alongo anu. Musamazengereze kupempha akulu kuti akuthandizeni. Iwo ali ngati “malo obisalirapo mphepo” komanso “malo obisalirapo mvula yamkuntho.” (Yes. 32:2) Muzikumbukira kuti Akhristu anzanu akukumananso ndi mavuto. Mukamakomera mtima abale ndi alongo anu omwe akuvutika mumakhala osangalala ndipo zimakuthandizani kuti muzipirira mavuto anu.—Mac. 20:35.
Muzilola kuti abale ndi alongo anu akulimbikitseni (Onani ndime 14)c
CHIYEMBEKEZO
15. Kodi chiyembekezo chinathandiza bwanji Yesu, nanga chikuthandiza bwanji atumiki a Yehova okhulupirika? (Aheberi 12:2)
15 Yehova watipatsa chiyembekezo chotsimikizika chomwe chimatithandiza kupirira. (Aroma 15:13) Taganizirani mmene chiyembekezo chinathandizira Yesu kupirira pa tsiku lovuta kwambiri pa moyo wake. (Werengani Aheberi 12:2.) Yesu ankadziwa kuti kukhulupirika kwake kudzachititsa kuti dzina la Yehova liyeretsedwe. Ankayembekezeranso kubwerera kwa Atate wake komanso m’kupita kwa nthawi, kudzalamulira ndi abale ake odzozedwa mu Ufumu wakumwamba. Mofanana ndi zimenezi, chiyembekezo chathu chodzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano chimatithandiza kupirira mavuto amene tingakumane nawo m’dziko la Satanali.
16. Kodi chiyembekezo chinathandiza bwanji mlongo wina kupirira, nanga tikuphunzira chiyani pa zimene iye ananena?
16 Taganizirani mmene chiyembekezo cha Ufumu chinathandizira mlongo wina wa ku Russia dzina lake Anna, yemwe mwamuna wake anatsekeredwa m’ndende poyembekezera kuimbidwa mlandu. Zimenezi zitachitika Anna anati: “Kupemphera komanso kuganizira za chiyembekezo chathu cha m’tsogolo kumandithandiza kuti ndisafooke. Ndikudziwa kuti mavutowa adzatha. Yehova adzagonjetsa adani ake ndipo adzatipatsa mphoto.”
17. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira chiyembekezo chimene Yehova watipatsa? (Onaninso chithunzi.)
17 Zimene mungachite. Muzipeza nthawi yoganizira zinthu zosangalatsa zimene Yehova watilonjeza m’tsogolo. Muziyerekezera mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano komanso madalitso amene mudzapeze. Mukamachita zimenezi, mavuto amene mukukumana nawo angaoneke “akanthawi ndiponso aang’ono.” (2 Akor. 4:17) Muziyesetsanso kuuza ena zimene mumakhulupirira. Anthu m’dzikoli akukumana ndi mavuto ndipo sakudziwa zimene Mulungu walonjeza m’tsogolomu, choncho muziganizira mmene zingakhalire zovuta kwa iwo kupirira mavuto amenewa. Kukambirana nawo mfundo zochepa kungawathandize kukhala ndi chidwi chofuna kudziwa zambiri zokhudza Ufumu wa Yehova ndi malonjezo ake.
Muzipeza nthawi yoganizira zinthu zabwino zimene Yehova walonjeza m’tsogolo (Onani ndime 17)d
18. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira zimene Yehova watilonjeza?
18 Pambuyo popirira mokhulupirika mavuto ambiri omwe anakumana nawo, Yobu anauza Yehova kuti: “Tsopano ndadziwa kuti inu mumatha kuchita zinthu zonse, ndiponso kuti palibe chilichonse chimene mukufuna kuchita chimene simungakwanitse.” (Yobu 42:2) Yobu anaphunzira kuti palibe chimene chingalepheretse Yehova kukwaniritsa cholinga chake. Mfundo imeneyi ingatilimbikitsenso ifeyo kuti tizipirira. Tiyerekeze kuti pali mayi wina yemwe wakhumudwa chifukwa chakuti madokotala ambiri akulephera kumuchiritsa. Koma kenako akukumana ndi dokotala wina yemwe ndi waluso komanso wodalirika ndipo akumufotokozera mavuto ake komanso mmene angamuthandizire pa mavuto akewo. Mayiyo akuyamba kusangalala ngakhale kuti pangatenge nthawi kuti achire. Iye angathe kupirira chifukwa tsopano ali ndi chiyembekezo chakuti adzachira. Mofanana ndi zimenezi, kukhulupirira zimene tikuyembekezera m’Paradaiso kumatithandiza kupirira.
19. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tizipirira?
19 Munkhaniyi taona kuti Yehova amatithandiza kupirira pogwiritsa ntchito Mawu ake, pemphero, Akhristu anzathu komanso chiyembekezo. Tikamalola kuti zinthu zimenezi zitithandize, Yehova angatithandize kupirira vuto lililonse limene tingakumane nalo mpaka pamene adzathetse mavuto onse m’dzikoli.—Afil. 4:13.
NYIMBO NA. 33 Umutulire Yehova Nkhawa Zako
a Mayina ena munkhaniyi asinthidwa.
b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale wachikulire wakhala akupirira kwa zaka zambiri ndipo akukhalabe wokhulupirika kwa Yehova.
c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale wachikulire wakhala akupirira kwa zaka zambiri ndipo akukhalabe wokhulupirika kwa Yehova.
d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale wachikulire wakhala akupirira kwa zaka zambiri ndipo akukhalabe wokhulupirika kwa Yehova.