Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 October tsamba 12-17
  • Chikondi cha Mulungu Chidzakhalapo Mpaka Kalekale

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikondi cha Mulungu Chidzakhalapo Mpaka Kalekale
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • CHIKONDI CHA YEHOVA NDI IMODZI MWA MFUNDO ZOYAMBIRIRA ZA M’BAIBULO
  • MUZIGANIZIRA MOZAMA MMENE YEHOVA ‘AMAKUKONDERANI’
  • MUZIZINDIKIRA ZIMENE ZIMAKUPANGITSANI KUKAYIKIRA
  • MUZISANKHA KUKHALABE WOKHULUPIRIKA
  • Yehova Amakukondani Kwambiri
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Musamakayikire Kuti Yehova Amakukondani
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Kodi Tingatani Kuti Tisiye Kukayikira?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Kodi Timapindula Bwanji ndi Chikondi Chokhulupirika cha Yehova?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 October tsamba 12-17

NKHANI YOPHUNZIRA 41

NYIMBO NA. 108 Chikondi Chokhulupirika cha Mulungu

Chikondi cha Mulungu Chidzakhalapo Mpaka Kalekale

“Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino. Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”—SAL. 136:1.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona mmene kudziwa zimene Baibulo limanena pa nkhani ya chikondi cha Yehova kungatithandizire tikakumana ndi mavuto.

1-2. Kodi Akhristu ambiri amakumana ndi vuto liti?

TAYEREKEZERANI kuti mwakwera boti ndipo mwakumana ndi mafunde amphamvu. Botilo likungopita kulikonse kumene mafundewo akulikankhira ndipo lingaime pokhapokha ngati wina ataika nangula. Nangulayo angathandize kuti botilo lisamangotengeka ndi mafunde koma kuti likhazikike.

2 Ngati mukukumana ndi vuto lalikulu, mukhoza kumva ngati muli m’boti limeneli. Mungamasinthesinthe mmene mukumvera. Tsiku lina mukhoza kumamva kuti Yehova amakukondani ndipo akukuthandizani. Tsiku lotsatira mukhoza kumakayikira ngati Yehova akuona zimene zikukuchitikirani. (Sal. 10:1; 13:1) Mnzanu angakuuzeni mawu olimbikitsa ndipo mungamveko bwino kwa kanthawi. (Miy. 17:17; 25:11) Koma kenako mukhoza kuyambanso kukayikira n’kumaganiza kuti Yehova amakuonani kuti ndinu wachabechabe. Kodi nangula wanu wophiphiritsa angakuthandizeni bwanji pa nthawi ya mavutoyi? Kodi mungatani kuti mupitirizebe kukhulupirira kuti Yehova amakukondani ndipo akukuthandizani?

3. Kodi mawu akuti “chikondi chokhulupirika” a pa Salimo 31:7; 136:​1, amatanthauza chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi amene amasonyeza kwambiri chikondichi? (Onani chithunzi.)

3 Kukumbukira chikondi chokhulupirika cha Yehova kungatithandize kukhalabe olimba tikamakumana ndi mavuto. (Werengani Salimo 31:7; 136:1.) Mawu akuti “chikondi chokhulupirika” amafotokoza za chikondi champhamvu chimene munthu amasonyeza munthu wina ndipo amapitirizabe kuchisonyeza zivute zitani. Yehova amasonyeza kwambiri chikondi chokhulupirika kuposa aliyense. Ndipotu Baibulo limanena kuti, iye ndi “wachikondi chokhulupirika chochuluka.” (Eks. 34:​6, 7) Limanenanso kuti Yehova ‘amasonyeza chikondi chokhulupirika chochuluka kwa onse amene amaitana pa iye.’ (Sal. 86:5) Kodi malembawa akufuna kutiuza chiyani? Yehova sasiya atumiki ake okhulupirika. Kukumbukira kuti Yehova ndi wokhulupirika kungakuthandizeni kuti mupirire mukamakumana ndi mavuto aakulu.—Sal. 23:4.

Nangula amumangirira ku boti n’cholinga choti botilo lisatengeke ndi mafunde.

Mofanana ndi nangula amene amathandiza kuti boti likhazikike, ifenso tikamakhulupirira kwambiri kuti Yehova amatikonda, tidzakhala olimba tikamakumana ndi mavuto (Onani ndime 3)


CHIKONDI CHA YEHOVA NDI IMODZI MWA MFUNDO ZOYAMBIRIRA ZA M’BAIBULO

4. Perekani zitsanzo za mfundo zoyambirira za m’Baibulo, ndipo fotokozani chifukwa chake timazikhulupirira kwambiri.

4 Tingakhalenso olimba tikakumana ndi mavuto, tikamakumbukira kuti mfundo yoti Yehova amatikonda ndi imodzi mwa mfundo zoyambirira za m’Baibulo. Kodi mumaganizira chiyani mukamva mawu akuti “mfundo zoyambirira za m’Baibulo”? Mwina mumaganizira mfundo za choonadi zimene mwaziphunzira m’Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, munaphunzira kuti dzina la Mulungu ndi Yehova, Yesu ndi Mwana wa Mulungu wobadwa yekha, akufa sadziwa chilichonse komanso kuti dzikoli lidzakhala Paradaiso ndipo anthu adzakhalamo mpaka kalekale. (Sal. 83:18; Mlal. 9:5; Yoh. 3:16; Chiv. 21:​3, 4) Mutayamba kukhulupirira mfundozi, simunalole kuti aliyense akusiyitseni kuzikhulupirira, chifukwa munazindikira kuti ndi zochokera m’Baibulo. Tiyeni tione mmene mfundo yakuti chikondi cha Yehova ndi imodzi mwa mfundo zoyambirira za m’Baibulo, ingatithandizire kuchotsa maganizo akuti Yehova samaona kapena kudera nkhawa mavuto amene tikukumana nawo.

5. Kodi n’chiyani chimathandiza munthu kukana ziphunzitso zabodza?

5 Mutayamba kuphunzira Baibulo, n’chiyani chinakuthandizani kuti musiye kukhulupirira ziphunzitso zabodza? Mwina munkayerekezera zimene munaphunzira kuchipembedzo chanu ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Mwachitsanzo, mwina poyamba munkakhulupirira kuti Yesu ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Ndiye pamene munkaphunzira Baibulo munkadzifunsa kuti, ‘Koma zimene ndinaphunzitsidwa zija n’zoonadi?’ Mutaphunzira zimene Baibulo limanena, munazindikira kuti Yesu si Mulungu Wamphamvuyonse. Ndiyeno munayamba kukhulupirira mfundo ya m’Baibulo yakuti, Yesu ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse” komanso “Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.” (Akol. 1:15; Yoh. 3:18) N’zoona kuti ziphunzitso zabodza ‘zimazikika molimba’ ndipo zingakhale zovuta kusiya kuzikhulupirira. (2 Akor. 10:​4, 5) Koma mutaphunzira choonadi, munakwanitsa kuzisiya ndipo simunayambirenso kuzikhulupirira.—Afil. 3:13.

6. N’chifukwa chiyani sitikayikira kuti “chikondi chokhulupirika” cha Yehova chidzakhalapo mpaka kalekale?

6 Mungachitenso chimodzimodzi pa nkhani ya zimene Baibulo limaphunzitsa zoti Yehova amatikonda. Mukakumana ndi mavuto, n’kuyamba kukayikira ngati Yehova amakukondani, muzidzifunsa kuti, ‘Koma ndikuganiza bwino?’ Ndiye muziyerekezera zimene mukukayikirazo, zoti Yehova amakukondani, ndi zimene zili pa Salimo 136:1 lomwe ndi lemba limene likutsogolera nkhaniyi. N’chifukwa chiyani Yehova amafotokoza kuti chikondi chake ndi “chokhulupirika?” N’chifukwa chiyani mawu akuti “chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale” abwerezedwa maulendo 26 m’chaputalachi? Monga taonera, mfundo yoti Yehova amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu ake, ndi imodzi mwa mfundo zoyambirira za m’Baibulo zimene tiyenera kuzivomereza ngati mmene tinavomerezera mfundo zina zoyambirira za m’Baibulo. Maganizo akuti Yehova amakuonani kuti ndinu achabechabe komanso osayenera kukondedwa, ndi abodza. Muzikana bodza limeneli ngati mmene mungakanire mwamphamvu kukhulupirira ziphunzitso zabodza.

7. Tchulani malemba amene amatitsimikizira kuti Yehova amatikonda.

7 M’Baibulo muli maumboni ambiri amene amatitsimikizira kuti Yehova amatikonda. Mwachitsanzo, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.” (Mat. 10:31) Yehova anauza anthu ake kuti: ‘Ndikulimbitsani, ndithu ndikuthandizani, ndikugwirani mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.’ (Yes. 41:10) Mavesiwatu akunena zinthu motsimikiza. Yesu sakunena kuti ‘Mukhozatu kukhala ofunika kwambiri’ ndipo Yehova sakunena kuti ‘Ndikhozatu kukuthandindizani.’ M’malomwake akunena kuti, “Ndinu ofunika kwambiri” komanso ‘Ndithu ndikuthandizani.’ Choncho mukakumana ndi mavuto n’kumakayikira ngati Yehova amakukondani, malemba ngati amenewa angakuthandizeni kumva kuti amakukondani komanso kukutsimikizirani kuti amakukondanidi. Malembawatu akufotokoza mfundo zenizeni. Tikamapemphera kwa Yehova n’kumaganizira mozama malembawa, tinganene mawu a pa 1 Yohane 4:16 akuti: “Ife tikudziwa komanso tikukhulupirira kuti Mulungu amatikonda.”a

8. Kodi mungatani ngati nthawi zina mumakayikira zoti Yehova amakukondani?

8 Kodi mungatani ngati nthawi zina mumakayikirabe ngati Yehova amakukondani? Muziyerekezera mmene mukumvera ndi zimene mukudziwa zokhudza Yehova. Anthufe timasinthasintha mmene timamvera. Koma mfundo yakuti Yehova amatikonda, simasintha. Ngati timakayikira zoti Yehova amatikonda, ndiye kuti tikunyalanyaza khalidwe lalikulu la Yehova lomwe ndi chikondi.—1 Yoh. 4:8.

MUZIGANIZIRA MOZAMA MMENE YEHOVA ‘AMAKUKONDERANI’

9-10. Kodi Yesu ankanena za chiyani pamene ananena kuti “Atatewo amakukondani” pa Yohane 16:​26, 27? (Onaninso chithunzi.)

9 Tingaphunzire zambiri zokhudza chikondi cha Yehova tikaganizira zimene Yesu anauza otsatira ake kuti, “Atatewo amakukondani.” (Werengani Yohane 16:​26, 27.) Yesu sanauze ophunzira ake mawuwa pongofuna kuwasangalatsa. Ndipotu nkhani yonse m’chaputalachi imasonyeza kuti Yesu sankanena za mmene ophunzira ake akumvera, koma ankanena za pemphero.

10 Yesu anali atangouza ophunzira ake kuti azipemphera kudzera m’dzina lake, osati kwa iye. (Yoh. 16:​23, 24) Zinali zofunika kwambiri kuti ophunzirawo adziwe zimenezi. Yesu ataukitsidwa, n’kutheka kuti ophunzira ake akanafuna kuti azipemphera kwa iye. Pajatu iwo ankaona kuti Yesu ndi mnzawo. Popeza ankadziwa kuti Yesu amawakonda, mwina ankaganiza kuti azimvetsera mapemphero awo n’kupempha Yehova kuti awathandize. Komabe Yesu anawauza kuti asakhale ndi maganizo amenewa. Chifukwa chiyani? Chifukwa anawauza kuti: “Atatewo amakukondani.” Imeneyi ndi mbali ya mfundo zoyambirira za m’Baibulo yokhudza pemphero. Kodi mfundoyi ikukukhudzani bwanji? Inunso mutaphunzira Baibulo munadziwa Yesu ndipo munayamba kumukonda. (Yoh. 14:21) Mofanana ndi ophunzirawo, nanunso mungapemphere ndi chikhulupiriro podziwa kuti “Atatewo amakukondani.” Ndipo nthawi iliyonse imene mukupemphera kwa Yehova, mumasonyeza kuti mumakhulupirira mawu amenewa.—1 Yoh. 5:14.

Zithunzi: M’bale wakhala pampando ndipo akupemphera ndi mtima wonse zokhudza zinthu zitatu zofunika kwambiri pamoyo wake. 1. Mkazi wake wagona pabedi ndipo m’baleyo akumubweretsera chakudya. 2. M’baleyo akuphunzira Baibulo ndi mwana wake wamkazi. 3. M’bale akuwerengetsera mmene ndalama zikuyendera.

Mungapemphere kwa Yehova ndi chikhulupiriro, podziwa kuti “Atatewo amakukondani” (Onani ndime 9 ndi 10)b


MUZIZINDIKIRA ZIMENE ZIMAKUPANGITSANI KUKAYIKIRA

11. N’chifukwa chiyani Satana amasangalala tikamakayikira zoti Yehova amatikonda?

11 Kodi ndi ndani amene amapangitsa kuti tizikayikira zoti Yehova amatikonda? Mwina munganene kuti ndi Satana ndipotu zimenezi zikhoza kukhala zoona. Mdyerekezi akufunitsitsa ‘kutimeza’ ndipo angasangalale atadziwa kuti tikukayikira zoti Yehova amatikonda. (1 Pet. 5:8) Chifukwa chakuti Yehova amatikonda, anatipatsa mphatso ya dipo. Koma Satana amafuna kuti tizidziona kuti ndife osayenera kulandira mphatsoyi. (Aheb. 2:9) Ndiye kodi ndi ndani amene amasangalala tikamakayikira kuti Yehova amatikonda. Ndi Satana. Nanga ndi ndani amene angasangalale ngati titafooka n’kusiya kutumikira Yehova? Ndi Satana yemweyo. Satana amafuna tiziganiza kuti Yehova satikonda. Koma si zoona. Satanayo ndi amene sakondedwa ndi Yehova. Ndipotu imodzi mwa njira zake “zachinyengo” ndi yoti amatipangitsa kuti tizimva kuti ifeyo ndi amene Yehova satikonda ndipo sasangalala nafe. (Aef. 6:11) Tikazindikira zimene mdani wathuyu akufuna kuchita, tikhoza kuyesetsa kuti ‘timutsutse.’—Yak. 4:7.

12-13. Kodi uchimo womwe tinabadwa nawo umatichititsa bwanji kuti tizikayikira zoti Yehova amatikonda?

12 Chinanso chimene chimatipangitsa kukayikira zoti Yehova amatikonda, ndi uchimo umene timabadwa nawo. (Sal. 51:5; Aroma 5:12) Uchimo unasokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Unawononganso maganizo, mtima ndi thupi lathu.

13 Uchimo unasokoneza mmene timamvera ndipo umapangitsa kuti tizidziimba mlandu, tizikhala ndi nkhawa, tizimva kuti ndife osatetezeka komanso tizichita manyazi. Mmenemu ndi mmene timamvera tikachita tchimo. Tingamamvenso choncho chifukwa nthawi zonse timakumbukira kuti tinabadwa ochimwa, zomwe ndi zosiyana kwambiri ndi zimene Yehova ankafuna. (Aroma 8:​20, 21) Mofanana ndi galimoto yomwe yaphwa tayala ndipo singathamange mmene ikanathamangira ikanakhala kuti ili bwinobwino, ifenso popeza si ife angwiro, sitingachite zinthu bwinobwino ngati mmene tikanachitira tikanakhala angwiro. Choncho n’zosadabwitsa kuti nthawi zina timalimbana ndi maganizo oona ngati Yehova satikonda. Zimenezi zikachitika, tizikumbukira kuti Yehova ndi ‘Mulungu wamkulu komanso wochititsa mantha. Ndipo amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu amene amamukonda ndi kusunga malamulo ake.’—Neh. 1:5.

14. Kodi kuganizira za dipo kungatithandize bwanji kusiya kukayikira zoti Yehova amatikonda? (Aroma 5:8) (Onaninso bokosi lakuti, “Samalani Ndi ‘Chinyengo Champhamvu cha Uchimo.’”)

14 N’zoona kuti nthawi zina tingamadzione kuti si ife oyenera kukondedwa ndi Yehova. Ndipotu kunena zoona anthufe sitinali oyenera kukondedwa ndi Yehova. N’chifukwa chake chikondi chake chili chapadera kwambiri. Iye sanayambe kutikonda chifukwa choti tinachita zinazake. Koma popeza Yehova amatikonda, anapereka dipo kuti machimo athu azikhululukidwa. (1 Yoh. 4:10) Muzikumbukiranso kuti Yesu anabwera kudzapulumutsa anthu ochimwa osati angwiro. (Werengani Aroma 5:8.) Palibe amene angachite zinthu popanda kulakwitsa ndipo Yehova satiyembekezera kuti tizichita zinthu mwangwiro. Tikamvetsa kuti uchimo umapangitsa kuti tizikayikira zoti Yehova amatikonda, zingatithandize kuti tiziyesetsa kulimbana ndi maganizo amenewa.—Aroma 7:​24, 25.

Samalani Ndi “Chinyengo Champhamvu cha Uchimo”

Baibulo limanena za “chinyengo champhamvu cha uchimo.” (Aheb. 3:13) Uchimo umachititsa kuti tizikopeka n’kuchita zinthu zolakwika komanso kuti nthawi zonse tizikayikira zoti Yehova amatikonda. Zoonadi uchimo uli ndi “chinyengo cha mphamvu.”

Tikhoza kumaganiza kuti n’zosatheka kuti tipusitsidwe. Mwachitsanzo, tingamaganize kuti anthu achinyengo sangatipusitse n’kutibera ndalama. Koma ngati sitingasamale ndi zochita zawo zachinyengozo, akhoza kutibera.

Mofanana ndi zimenezi, tiyenera kusamala kuti uchimo umene tili nawo usatipusitse n’kuyamba kukayikira zoti Yehova amatikonda. Uchimo umatipangitsa kuti tizingoganizira zofooka zathu, zimene timalephera kuchita bwino komanso zimene timalakwitsa. Komatu chimenechi ndi “chinyengo champhamvu cha uchimo” ndipo tifunika kusamala.

MUZISANKHA KUKHALABE WOKHULUPIRIKA

15-16. Kodi sitingakayikire chiyani ngati titakhalabe okhulupirika kwa Yehova, nanga n’chifukwa chiyani? (2 Samueli 22:26)

15 Yehova amafuna tizichita zinthu mwanzeru pokhalabe “okhulupirika kwa iye.” (Deut. 30:​19, 20) Tikachita zimenezi, sitingakayikire kuti Yehova adzakhalabe wokhulupirika kwa ife. (Werengani 2 Samueli 22:26.) Tikapitiriza kukhala okhulupirika kwa Yehova, sitingakayikire kuti iye adzatithandiza kupirira mavuto alionse amene tingakumane nawo.

16 Monga taonera, tili ndi zifukwa zambiri zotithandiza kukhalabe olimba tikamakumana ndi mavuto. Timadziwa kuti Yehova amatikonda ndipo apitiriza kutithandiza. Zimenezi n’zomwe Baibulo limaphunzitsa. Tikamakayikira zoti Yehova amatikonda, tizikumbukira zimene tikudziwa zokhudza chikondi chake m’malo moganizira mmene tikumvera pa nthawiyo. Tiyeni tipitirize kukhulupirira zimene Baibulo limanena zoti chikondi chokhulupirika cha Yehova chidzakhalapo mpaka kalekale.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi kukumbukira kuti Yehova amatikonda ndi imodzi mwa mfundo zoyambirira za m’Baibulo kungatithandize bwanji?

  • Kodi uchimo womwe tinabadwa nawo umatipangitsa bwanji kukayikira zoti Yehova amatikonda?

  • Kodi tingatani kuti tisiye kukayikira zoti Yehova amatikonda?

NYIMBO NA. 159 M’patseni Yehova Ulemerero

a Malemba ena ndi Deuteronomo 31:​8, Salimo 94:14 ndi Yesaya 49:15.

b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akupemphera kwa Yehova kuti amuthandize kusamalira mkazi wake amene akudwala, kuti azigwiritsira ntchito ndalama zake mwanzeru komanso kuti aphunzitse mwana wake wamkazi kuti azikonda Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena