Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 August tsamba 8-13
  • Musamakayikire Kuti Yehova Amakukondani

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Musamakayikire Kuti Yehova Amakukondani
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • TISAMAKAYIKIRE KUTI YEHOVA AMATIKONDA
  • N’CHIYANI CHINGATITHANDIZE KUTI TISAMAKAYIKIRE KUTI YEHOVA AMATIKONDA?
  • YESU AMATITHANDIZA KUTI TISAMAKAYIKIRE KUTI YEHOVA AMATIKONDA
  • MUZILIMBITSA CHIKHULUPIRIRO CHANU
  • Yehova Amakukondani Kwambiri
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Kodi Dipo Limatiphunzitsa Chiyani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Chikondi cha Mulungu Chidzakhalapo Mpaka Kalekale
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Tizivomereza Modzichepetsa Kuti Sitikudziwa Zonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 August tsamba 8-13

NKHANI YOPHUNZIRA 33

NYIMBO NA. 4 “Yehova Ndi M’busa Wanga”

Musamakayikire Kuti Yehova Amakukondani

“Ndakukokera kwa ine ndi chikondi chokhulupirika.”​—YER. 31:3.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tiona chifukwa chake sitiyenera kukayikira kuti Yehova amatikonda komanso zimene tingachite kuti tizikhulupirira kwambiri zimenezi.

1. N’chifukwa chiyani munadzipereka kwa Yehova? (Onaninso chithunzi.)

KODI mukukumbukira nthawi imene munadzipereka kwa Yehova? Munasankha kuchita zimenezi chifukwa chakuti munafika pomudziwa bwino komanso kumukonda. Munamulonjeza kuti mudzaika zimene amafuna pamalo oyamba komanso mudzapitiriza kumukonda ndi mtima wanu wonse, moyo wanu, maganizo ndi mphamvu zanu zonse. (Maliko 12:30) Kuyambira nthawi imeneyo chikondi chanu pa Yehova chakhala chikukulirakulira. Ndiye kodi mungayankhe bwanji munthu wina atakufunsani kuti, “Kodi mumakondadi Yehova?” Mosakayikira mungamuyankhe kuti, “Ndimamukonda kuposa munthu wina aliyense kapena chinthu china chilichonse.”

Chithunzi: Mlongo akuganizira nthawi imene anadzipereka komanso kubatizidwa. 1. Wakhala panja ndipo akupempera. 2. Iye akubatizidwa mumtsinje.

Kodi mumakumbukira mmene munkakondera Yehova pa nthawi imene munadzipereka kwa iye komanso kubatizidwa? (Onani ndime 1)


2-3. Kodi Yehova amafuna kuti tisamakayikire za chiyani, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi? (Yeremiya 31:3)

2 Koma kodi mungayankhe bwanji munthu wina atakufunsani kuti, “Kodi mukuganiza kuti Yehova amakukondani?” Kodi mwina mungakayikire kuyankha chifukwa chodziona kuti ndinu wosayenera kuti Yehova azikukondani? Mlongo wina amene sanasonyezedwe chikondi ali mwana ananena kuti: “Ndimadziwa kuti ndimakonda Yehova ndipo sindimakayikira zimenezi. Chimene nthawi zambiri ndimakayikira n’chakuti, Kodi Yehova amandikonda ineyo?” Ndiye kodi n’chiyani chimene chingakuthandizeni kuti musamakayikire kuti Yehova amakukondani?

3 Yehova amafuna kuti musamakayikire kuti amakukondani. (Werengani Yeremiya 31:3.) N’zoona kuti Yehova ndi amene anakukokerani kwa iye. Ndipo pamene munadzipereka kwa iye n’kubatizidwa, iye anakupatsani chinthu chamtengo wapatali chomwe ndi chikondi chake chokhulupirika. Chikondi chimenechi n’chachikulu kwambiri moti iye sangakusiyeni, ndipo ndi chimene chimamuchititsa kuti aziona atumiki ake okhulupirika kuphatikizapo inuyo ngati “chuma chapadera.” (Mal. 3:17) Yehova amafuna kuti muzimva ngati mtumwi Paulo yemwe sankakayikira kuti Yehova amamukonda. Paulo analemba kuti: “Ndatsimikiza mtima kuti imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera, mphamvu, msinkhu, kuzama kapena cholengedwa chilichonse, sizidzatha kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu.” (Aroma 8:38, 39) Munkhaniyi tikambirana chifukwa chake sitiyenera kukayikira kuti Yehova amatikonda komanso zimene zingatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri zimenezi.

TISAMAKAYIKIRE KUTI YEHOVA AMATIKONDA

4. Kodi Satana amafuna tizikhulupirira bodza liti, nanga tingamutsutse bwanji?

4 Kusakayikira kuti Yehova amatikonda kungatithandize kulimbana ndi chimodzi mwa “zochita zachinyengo” za Satana. (Aef. 6:11) Satana adzachita chilichonse chomwe angathe kuti atilepheretse kutumikira Yehova. Chimodzi mwa zochita zachinyengo za Satana ndi kuchititsa anthu kuti azikhulupirira bodza lakuti Yehova satikonda. Tisaiwale kuti Satana amakonda kupezerapo mwayi pa zofooka zathu. Nthawi zambiri iye amatiukira akaona kuti tafooka chifukwa cha mavuto amene tikukumana nawo panopa, zimene tinalakwitsa m’mbuyo, kapenanso pamene tikukayikira zam’tsogolo. (Miy. 24:10) Satana ali ngati mkango umene umapezerera nyama imene ikuoneka kuti ndi yosatetezeka. Choncho amapezerapo mwayi tikafooka kuti atichititse kusiya kutumikira Yehova. Koma tikamakhulupirira kwambiri kuti Yehova amatikonda, tingakhale okonzeka bwino ‘kulimbana’ ndi Satana ndi zochita zake zachinyengo.​—1 Pet. 5:8, 9; Yak. 4:7.

5. Kodi kusakayikira kuti Yehova amatikonda n’kofunika bwanji?

5 Kukhulupirira kuti Yehova amatikonda kumatithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba. N’chifukwa chiyani tikutero? Yehova anatilenga m’njira yoti tizikonda ena komanso tizifuna kuti ena azitikonda. Ena akatisonyeza chikondi ifenso timafuna kuwakonda. Choncho tikamaona kuti Yehova amatikonda, m’pamenenso timafunitsitsa kumukonda. (1 Yoh. 4:19) Ndipo tikayamba kumukonda kwambiri, nayenso amatikonda kwambiri. Baibulo limatiuza kuti: “Yandikirani Mulungu ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yak. 4:8) Ndiye kodi tingatani kuti tizikhulupirira kwambiri kuti Yehova amatikonda?

N’CHIYANI CHINGATITHANDIZE KUTI TISAMAKAYIKIRE KUTI YEHOVA AMATIKONDA?

6. Kodi tiyenera kupempherera chiyani kuti tisamakayikire zoti Yehova amatikonda?

6 Muzipemphera nthawi zonse ndipo muzitchula zenizeni zimene mukufuna. (Luka 18:1; Aroma 12:12) Muzipempha Yehova kambirimbiri tsiku lililonse kuti azikuthandizani kuti muzidziona ngati mmene iye amakuonerani. Kunena zoona, mtima wodziimba mlandu ungachititse kuti zikhale zovuta kuti munthu aziona kuti Yehova amamukonda. Koma tisamaiwale kuti Yehova ndi wamkulu kuposa mitima yathu. (1 Yoh. 3:19, 20) Iye amakudziwani bwino kuposa mmene inuyo mumadzidziwira ndipo amaona makhalidwe abwino amene muli nawo omwe inuyo simungathe kuwaona. (1 Sam. 16:7; 2 Mbiri 6:30) Choncho musamazengereze ‘kumukhuthulira’ zonse zamumtima mwanu, pomufotokozera mmene mukumvera komanso kumupempha kuti akuthandizeni kuti muzikhulupirira kuti iye amakukondani. (Sal. 62:8) Kenako muzichita zinthu mogwirizana ndi mapemphero anu pogwiritsa ntchito mfundo zotsatirazi.

7-8. Kodi buku la Masalimo limatitsimikizira bwanji kuti Yehova amatikonda?

7 Muzikhulupirira zimene Yehova amanena. Pogwiritsa ntchito mzimu woyera, Yehova anathandiza olemba Baibulo kuti afotokoze zoona zokhudza mmene iyeyo alili. Taganizirani mmene Davide anafotokozera bwino mfundo yosonyeza kuti Yehova amatikonda. Iye anati: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Iye amapulumutsa anthu amene akhumudwa.” (Sal. 34:18, mawu a m’munsi.) Nthawi zambiri mukakhumudwa mungamadzione kuti muli nokhanokha. Koma Yehova akulonjeza kuti pa nthawi ngati imeneyi m’pamene amakhala nanu pafupi kwambiri, chifukwa amadziwa kuti ndi pamene mukufunikira kwambiri thandizo lake. Musalimo lina, Davide analemba kuti: “Sungani misozi yanga mʼthumba lanu lachikopa.” (Sal. 56:8) Yehova amaona tikakhumudwa ndipo zimamukhudza akaona tikuvutika. Tingati Yehova amasunga misozi yanu ndipo amaiona kuti ndi yamtengo wapatali ngati mmene munthu wapaulendo ankaonera madzi amene ankaika m’thumba lake lachikopa. Pa Salimo 139:3 timawerenga kuti: “[Yehova] mumadziwa chilichonse chimene ndikuchita.” Yehova amaona chilichonse chimene mukuchita koma amaganizira kwambiri zabwino zimene mumachita. (Aheb. 6:10) Chifukwa chiyani? Chifukwa amayamikira kwambiri zonse zimene mumayesetsa kuchita kuti mumusangalatse.a

8 Pogwiritsa ntchito malemba olimbikitsa ngati amenewa, zili ngati Yehova akutiuza kuti: “Ndikufuna udziwe kuti ndimakukonda kwambiri.” Koma monga mmene taonera kumayambiriro kwa nkhaniyi, Satana amafuna kuti tizikhulupirira bodza lakuti Yehova satikonda. Choncho ngati nthawi zina mumakayikira kuti Yehova amakukondani muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndiyenera kukhulupirira ndani, “tate wake wa bodza” kapena “Mulungu wa choonadi”?’​—Yoh. 8:44; Sal. 31:5.

9. Kodi Yehova amawatsimikizira chiyani anthu omwe amamukonda? (Ekisodo 20:5, 6)

9 Muziganizira mmene Yehova amamvera ena akamamusonyeza chikondi. Mwachitsanzo taganizirani zimene Yehova anauza Mose ndi Aisiraeli. (Werengani Ekisodo 20:5, 6.) Yehova analonjeza kuti adzapitiriza kusonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu amene amamukonda. Mawu amenewa akusonyeza kuti Mulungu wathu yemwe ndi wokhulupirika, amakonda anthu omwe amamukonda. (Neh. 1:5) Ndiye nthawi ina mukamakayikira kuti Yehova amakukondani muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndimakonda Yehova?’ Ndiyeno muziganizira mfundo iyi: Ngati mumamukonda ndipo mukuyesetsa kuchita zomusangalatsa, musamakayikire kuti iyenso amakukondani kwambiri. (Dan. 9:4; 1 Akor. 8:3) Izi zikutanthauza kuti ngati mumakonda Yehova, palibe chifuwa chokayikirira kuti iye amakukondani. Muzikhulupirira ndi mtima wonse kuti iye amakukondani ndipo sadzakusiyani.

10-11. Kodi Yehova amafuna tiziliona bwanji dipo? (Agalatiya 2:20)

10 Muziganizira za dipo. Dipo ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova anapereka kwa anthu. (Yoh. 3:16) Koma kodi mphatso imeneyi anakupatsani inuyo panokha? Inde. Taganizirani zimene zinachitikira mtumwi Paulo. Kumbukirani kuti anachita machimo akuluakulu asanakhale Mkhristu ndipo ankalakwitsabe zinthu zina. (Aroma 7:24, 25; 1 Tim. 1:12-14) Koma iye ankaona kuti dipo ndi mphatso imene Yehova anapereka kwa iyeyo payekha. (Werengani Agalatiya 2:20.) Ndiyeno kumbukirani kuti Yehova ndi amene anauzira Paulo kuti alembe zimenezi. Ndipotu zonse zimene zinalembedwa m’Baibulo zinalembedwa kuti zitilangize. (Aroma 15:4) Mawu a Paulowa akusonyeza kuti Yehova amafuna kuti inuyo muziona dipo ngati mphatso imene anakupatsani inuyo panokha. Mukamaona dipo m’njira imeneyi, mumakhulupirira kwambiri kuti Mulungu amakukondani.

11 Timathokoza kwambiri Yehova kuti anatumiza Yesu padzikoli kuti adzatifere. Koma chifukwa china chimene Yesu anabwerera, ndi kudzauza anthu choonadi chokhudza Mulungu. (Yoh. 18:37) Mwachitsanzo, Yesu anaphunzitsa kuti Yehova amakonda kwambiri ana ake.

YESU AMATITHANDIZA KUTI TISAMAKAYIKIRE KUTI YEHOVA AMATIKONDA

12. N’chifukwa chiyani sitingakayikire zimene Yesu anafotokoza zokhudza Yehova?

12 Yesu ali padziko lapansi, ankaphunzitsa anthu makhalidwe a Yehova. (Luka 10:22) Sitikayikira zinthu zonse zokhudza Yehova zimene iye anaphunzitsa. Paja Yesu anakhala ndi Yehova kumwamba kwa zaka zosawerengeka asanabwere padziko lapansi. (Akol. 1:15) Iye anaona yekha ndipo ankadziwa mmene Yehova amakondera ana ake okhulupirika. Ndiye kodi Yesu amathandiza bwanji ena kuti azikhulupirira kuti Yehova amawakonda?

13. Kodi Yesu amafuna tizimuona bwanji Yehova?

13 Yesu amafuna kuti tiziona Yehova ngati mmene iyeyo amamuonera. M’mabuku a Uthenga Wabwino, Yesu anatchula Yehova kuti “Atate” maulendo oposa 160. Ndipo akamalankhula ndi otsatira ake, ankakonda kugwiritsa ntchito mawu akuti “Atate wanu” kapena “Atate wanu wakumwamba.” (Mat. 5:16; 6:26) Yesu asanabwere padzikoli, atumiki okhulupirika a Yehova ankagwiritsa ntchito mawu ngati, ‘Wamphamvuyonse,’ ‘Wam’mwambamwamba’ kapena akuti ‘Mlengi Wamkulu’ ponena za Yehova. Koma nthawi zambiri Yesu ankagwiritsa ntchito mawu akuti ‘Atate,’ pofuna kusonyeza kuti Yehova amakonda kwambiri atumiki ake ngati mmene bambo wachikondi amakondera ana ake. Tiyeni tikambirane maulendo awiri pamene Yesu anagwiritsa ntchito mawu akuti “Atate.”

14. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti aliyense wa ife ndi wamtengo wapatali kwa Atate wathu wakumwamba? (Mateyu 10:29-31) (Onaninso chithunzi.)

14 Tiyambe ndi kukambirana mawu a Yesu a pa Mateyu 10:29-31. (Werengani.) Mpheta ndi mbalame zazing’ono zomwe sizingalambire kapena kukonda Yehova. Komatu Atate wathu amaona kuti mbalame imeneyi ndi yamtengo wapatali ndipo amadziwa ikagwa pansi. Ndiye ngati Yehova amaona kuti mbalame zimenezi ndi zamtengo wapatali, kuli bwanji atumiki ake okhulupirika omwe amamulambira chifukwa chomukonda? Yesu ananenanso kuti Yehova amadziwa kuchuluka kwa tsitsi lomwe lili m’mutu mwathu. Ndiye ngati Yehova amadziwa tinthu ting’onoting’ono tokhudza ifeyo, tisamakayikire kuti amatikonda. Apa n’zoonekeratu kuti Yesu amafuna kuti tizikhulupirira kuti Atate wathu amationa kuti ndife amtengo wapatali.

Yesu akuloza mpheta yomwe ikutera. Ophunzira ake akumumvetsera mwatcheru.

Yehova amaona kuti mpheta imodzi ndi yamtengo wapatali ndipo amadziwa ikagwa pansi. Ndiye kuli bwanji inuyo amene mumamukonda komanso kumutumikira mokhulupirika? (Onani ndime 14)


15. Kodi mawu a Yesu a pa Yohane 6:44, amatiuza zotani zokhudza Atate wathu wakumwamba?

15 Tiyeni tione nthawi inanso pamene Yesu anagwiritsa ntchito mawu akuti “Atate.” (Werengani Yohane 6:44.) Atate wanu wakumwamba ndi amene anakukokani kapena kukuthandizani kuti mudziwe choonadi. N’chifukwa chiyani anakukokani? Chifukwa anaona makhalidwe abwino mumtima mwanu. (Mac. 13:48) Pamene Yesu ankanena mawu omwe ali pa Yohane 6:44, ayenera kuti ankafotokoza zomwe Yeremiya analemba zimene zili mulemba lotsogolera nkhaniyi. Palemba limeneli, Yehova anauza anthu ake kuti: “Ndakukokera kwa ine ndi chikondi chokhulupirika, [kapena kuti ndikupitiriza kukusonyeza chikondi chokhulupirika].” (Yer. 31:3; mawu a m’munsi; yerekezerani ndi Hoseya 11:4.) Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani? Atate wanu wakumwamba akupitirizabe kuona zabwino mwa inu zimene inuyo simuziona.

16. (a) Kodi tingati Yesu akutiuza kuti chiyani, nanga n’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kwambiri kuti Yehova ndi Atate wathu wachikondi? (Onani bokosi lakuti “Atate Amene Tonsefe Timafunikira.”)

16 Pofotokoza kuti Yehova ndi Atate wathu, zili ngati Yesu akunena kuti: “Sikuti Yehova ndi Atate wa ine ndekha koma inunso ndi Atate wanu. Ndipo ndikukutsimikizirani kuti amakukondani inuyo panokha.” Choncho ngati nthawi zina mumakayikira kuti Yehova amakukondani, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndi nzeru kukayikira Mwana wa Mulungu, yemwe amadziwa bwino Atate komanso amalankhula zoona nthawi zonse?’​—1 Pet. 2:22.

“Atate Amene Tonsefe Timafunikira”

Mawu amenewa amapezeka m’mawu oyamba a buku la Yandikirani kwa Yehova. Pofotokoza cholinga cha bukuli mawu oyambawo amati: “Tiona kuti Yehova ndi . . . Atate amene tonsefe timafunikira. Popeza iye ndi wamphamvu, wachilungamo, wanzeru komanso wachikondi, sasiya ana ake okhulupirika.”

Pofotokoza mmene bukuli linamuthandizira, mlongo wina yemwe analeredwa ndi bambo wankhanza ananena kuti: “Bukuli linandithandiza kuti ndisamachite mantha ndikamva mawu akuti ‘bambo.’ Panopa ndimadziwa zimene bambo wabwino amachita. Ndimakhulupirira kuti Yehova amandikonda ndipo inenso ndimamukonda monga Bambo anga.” Pambuyo powerenga bukuli munthu winanso ananena kuti: “Kunena zoona, Yehova ndi Bambo wabwino kwambiri kuposa aliyense.”

Kuti muzikhulupirira kuti Yehova ndi Bambo amene inuyo mumafunikira, yesetsani kuti muwerenge bukuli kapena kuliwerenganso ngati munaliwerenga kale.

MUZILIMBITSA CHIKHULUPIRIRO CHANU

17. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tisamakayikire zoti Yehova amatikonda?

17 Tiyenera kupitiriza kulimbitsa chikhulupiriro chathu kuti tisamakayikire kuti Yehova amatikonda. Monga mmene taonera munkhaniyi, Satana yemwe ndi mdani wathu wochenjera apitirizabe kuyesetsa kuti atisiyitse kutumikira Yehova. Pofuna kufooketsa chikhulupiriro chathu, Satana apitiriza kutichititsa kukayikira zoti Mulungu amatikonda. Koma tisalole kuti Satana apambane.​—Yobu 27:5.

18. Kodi tingatani kuti tisamakayikire zoti Yehova amatikonda?

18 Kuti musamakayikire zoti Yehova amakukondani, pitirizani kumupempha kuti akuthandizeni kuti muzidziona ngati mmene iye amakuonerani. Muziganizira zimene olemba Baibulo anafotokoza zokhudza chikondi chake. Muziganizira mmene amamvera anthu ena akamamusonyeza chikondi, paja nayenso amawasonyeza chikondi. Muziganiziranso zifukwa zimene zimakuchititsani kuti muziona kuti dipo ndi mphatso imene anakupatsani inuyo panokha. Muzikhulupiriranso mawu a Yesu akuti Yehova ndi Atate wanu. Ndiyeno munthu wina akadzakufunsani kuti, “Kodi Yehova amakukondani?” mudzayankha molimba mtima kuti, “Inde amandikonda, ndipo tsiku lililonse ndimayesetsa kuti ndizimusonyeza kuti ndimamukonda.”

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Yehova amatikonda?

  • N’chiyani chimene chingatithandize kuti tisamakayikire kuti Yehova amatikonda?

  • Kodi Yesu amatithandiza bwanji kuti tisamakayikire kuti Yehova amatikonda?

NYIMBO NA. 154 Chikondi Sichitha

a Kuti mupeze malemba ena omwe amatitsimikizira kuti Yehova amatikonda, onani kamutu kakuti “Kudzikayikira” m’buku lakuti Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena