NKHANI YOPHUNZIRA 42
NYIMBO NA. 44 Pemphero la Munthu Wovutika
Mungatani Kuti Mapemphero Anu Azikhala Ochokera Pansi pa Mtima?
“Ndaitana ndi mtima wanga wonse. Ndiyankheni inu Yehova.”—Sal. 119:145.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tiona mmene mapemphero a atumiki a Yehova otchulidwa m’Baibulo angatithandizire kuti tizipemphera kuchokera pansi pa mtima.
1-2. (a) N’chiyani chingatilepheretse kuuza Yehova mmene tikumvera? (b) Tikudziwa bwanji kuti Yehova amamvetsera mapemphero athu mokoma mtima?
Kodi nthawi zina mumaona kuti mapemphero anu amakhala obwerezabwereza, osachokera pansi pa mtima komanso achizolowezi? Ngati ndi choncho, si inu nokha. Chifukwa choti timatanganidwa, nthawi zina tikhoza kumangopemphera mwachidule. Kapena tingamavutike kuuza Yehova mmene tikumvera chifukwa timadziona kuti ndife osayenera kulankhula naye.
2 Baibulo limati Yehova amaona kuti chofunika kwambiri si mawu amene tikugwiritsa ntchito popemphera, koma kuti tizipemphera kuchokera pansi pa mtima. Iye amamva “pempho la anthu ofatsa.” (Sal. 10:17) Ndipo amamvetsera mokoma mtima mawu onse amene tikunena chifukwa amatikonda kwambiri.—Sal. 139:1-3.
3. Kodi tikambirana mafunso ati?
3 Tingadzifunse kuti: N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera kwa Yehova momasuka? Kodi tingatani kuti mapemphero athu azikhala ochokera pansi pa mtima? Kodi mapemphero a atumiki a Yehova amene ali m’Baibulo, angatithandize bwanji kuti tizipemphera kuchokera pansi pa mtima? Nanga tingatani ngati tili ndi nkhawa kwambiri moti tikulephera kuuza Yehova mmene tikumvera? Tiyeni tikambirane mayankho a mafunso amenewa.
MUZIPEMPHERA KWA YEHOVA MOLIMBA MTIMA
4. N’chiyani chingatithandize kuti tizipemphera kwa Yehova molimba mtima? (Salimo. 119:145)
4 Tikamvetsa kuti Yehova ndi mnzathu wokhulupirika amene amafuna kuti zinthu zizitiyendera bwino, tingapemphere kwa iye molimba mtima. Chitsanzo ndi amene analemba Salimo 119. Iye ankaona kuti Yehova ndi bwenzi lake lokhulupirika. Iye anakumana ndi mavuto ambiri pamoyo wake. Anthu ena ankamunenera zoipa. (Sal. 119:23, 69, 78) Ankakhumudwanso chifukwa cha zimene ankalakwitsa. (Sal. 119:5) Ngakhale zinali choncho, sankaopa kuuza Yehova mmene ankamvera.—Werengani Salimo 119:145.
5. N’chifukwa chiyani sitiyenera kulola maganizo ofooketsa kutilepheretsa kupemphera kwa Yehova? Perekani chitsanzo.
5 Yehova amafuna kuti ngakhale anthu amene achita machimo aakulu azipemphera kwa iye. (Yes. 55:6, 7) Choncho tisamalole kuti maganizo ofooketsa atilepheretse kupemphera. Mwachitsanzo, woyendetsa ndege amadziwa kuti akhoza kulankhula ndi anthu oyang’anira za kayendedwe ka ndege akafuna thandizo. Ndiye kodi angalephere kupempha thandizo ngati atasochera kapena ngati atalakwitsa zinazake chifukwa cha manyazi? Ayi. Mofanana ndi zimenezi, ifenso nthawi zina tikasochera kapena kuchita tchimo, tingapemphere kwa Yehova molimba mtima.—Sal. 119:25, 176.
TINGATANI KUTI MAPEMPHERO ATHU AZIKHALA OCHOKERA PANSI PA MTIMA?
6-7. Kodi kuganizira za makhalidwe a Yehova kungatithandize bwanji kuti mapemphero athu azikhala ochokera pansi pa mtima? Perekani chitsanzo. (Onaninso mawu a m’munsi)
6 Tikamalankhula ndi Yehova momasuka, kumuuza zimene zili mumtima mwathu komanso mmene tikumvera, mapemphero athu amakhala ochokera pansi pa mtima. Ndiye kodi tingatani kuti tizipemphera mwanjira imeneyi?
7 Muziganizira makhalidwe a Yehova.a Tikamaganizira kwambiri makhaliwe a Yehova, m’pamenenso tingakhale omasuka kumufotokozera mmene tikumvera. (Sal. 145:8, 9, 18) Taganizirani za Mlongo Kristine, amene bambo ake anali ankhanza. Iye ananena kuti: “Sizinali zophweka kuti ndizilankhula ndi Yehova ngati bambo anga. Ndinkaona kuti Yehova sangandikonde chifukwa cha zimene ndinkalakwitsa.” Kodi ndi khalidwe la Yehova liti limene linamuthandiza? Iye anati: “Chikondi chokhulupirika cha Yehova chimandithandiza kuona kuti ndine wotetezeka. Ndimadziwa kuti iye sadzasiya kundithandiza. Ngakhale nditalakwitsa zinazake, iye adzapitiriza kundikonda komanso kundithandiza. Zimenezi zimandithandiza kuti ndizimasuka kumuuza zomwe zandisangalatsa komanso zimene zandikhumudwitsa.”
8-9. Kodi kuganizira kaye zimene tikufuna kunena tisanapemphere kuli ndi ubwino wotani? Perekani chitsanzo.
8 Muziganizira zimene mukufuna kunena. Musanapemphere mwina mungadzifunse mafunso ngati awa: ‘Kodi ndi mavuto ati amene ndikulimbana nawo panopa? Kodi pali amene ndikufunika kumukhululukira? Kodi pali chimene chasintha pamoyo wanga chomwe ndikufuna kuti Yehova andithandize? (2 Maf. 19:15-19) Tingatsatirenso pemphero lachitsanzo la Yesu, n’kumaganizira zomwe tingapemphe Yehova zokhudza dzina lake komanso zimene amafuna.—Mat. 6:9, 10.
9 Mlongo wina dzina lake Aliska atadziwa kuti mwamuna wake ali ndi khansa ya muubongo ndipo sangachire, zinkamuvuta kupemphera. Iye ananena kuti: “Ndinali ndi nkhawa kwambiri moti zinkandivuta kuganizira mawu oti ndinene popemphera.” Ndiye chinamuthandiza n’chiyani? Iye anati: “Ndisanapemphere, ndimaganizira kaye zimene ndikufuna kumuuza Yehova. Zimenezi zimandithandiza kuti ndisamangotchula za ineyo. Zimandithandizanso kuti mtima wanga ukhale m’malo ndiponso kuti maganizo anga akhale okhazikika ndikamapemphera.”
10. N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera kwa nthawi yaitali? (Onaninso chithunzi.)
10 Muzipemphera kwa nthawi Yaitali. N’zoona kuti tikhoza kupereka pemphero lalifupi, koma tikamapemphera kwa nthawi yaitali, timakhala ndi mwayi womuuza Yehova zimene tikuganiza komanso mmene tikumvera.b Mwamuna wa Aliska dzina lake Elijah ananena kuti: “Ndimapemphera maulendo ambiri patsiku ndipo zandithandiza kuti ndikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova chifukwa ndimakhala ndi nthawi yaitali yopemphera. Yehova samaona kuti ndikuchedwa kumaliza pemphero langa. Choncho ndimapemphera kwa nthawi yaitali.” Tayesani izi: Muzipeza nthawi komanso malo abwino komwe mungapempherereko, mwinanso mokweza popanda zosokoneza ndipo mukhale ndi chizolowezi chopereka mapemphero ataliatali.
Muzipeza nthawi komanso malo amene mungapemphere kwa Yehova kwa nthawi yaitali popanda zosokoneza (Onani ndime 10)
MUZIGANIZIRA MAPEMPHERO OCHOKERA PANSI PA MTIMA AMENE ANALEMBEDWA M’BAIBULO
11. Kodi kuganizira mapemphero ochokera pansi pa mtima amene analembedwa m’Baibulo kumatithandza bwanji? (Onaninso bokosi lakuti “Kodi Munakumanapo ndi Zimene Iwo Anakumana Nazo?”)
11 Kuganizira mapemphero a atumiki a Yehova otchulidwa m’Baibulo komanso nyimbo zawo kungatithandize kwambiri. Mukaganizira zimene iwo anauza Yehova kuchokera pansi pa mtima, zingakuthandizeni kuti inunso muzipemphera mwanjira imeneyo. Mapemphero awo angatithandize kupeza mawu abwino amene tinganene m’pemphero. Ndipotu mukhoza kupeza mapemphero ogwirizana ndi zimene zikuchitika pa moyo wanu.
12. Kodi tingadzifunse mafunso ati tikamaganizira mapemphero amene analembedwa m’Baibulo?
12 Mukamaganizira mapemphero amene analembedwa m’Baibulo muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ndi ndani ananena mawuwa, nanga ankakumana ndi zotani? Kodi zimene anafotokozazi ndi zomwenso zikundichitikira? Nanga ndikuphunzirapo chiyani?’ Mungafunike kufufuza mokwanira mayankho a mafunsowa ndipo mungapindule kwambiri. Tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo.
13. Kodi tingaphunzire chiyani pa pemphero la Hana? (1 Sam. 1:10, 11) (Onaninso chithunzi chapachikuto.)
13 Werengani 1 Samueli 1:10, 11. Pamene Hana ankapereka pempheroli ankakumana ndi mavuto awiri akuluakulu. Iye anali wosabereka ndipo mkazi mnzake ankamuvutitsa kwambiri. (1 Sam. 1:4-7) Ngati mwakhala mukulimbana ndi vuto linalake, kodi mungaphunzire chiyani pa pemphero la Hana? Hana anapemphera kwa Yehova kwa nthawi yaitali ndipo anafotokoza zonse zomwe zinkamudetsa nkhawa moti anapepukidwa. (1 Sam. 1:12, 18) Ifenso tingapepukidwe ngati ‘titamutulira Yehova nkhawa zathu’ pomuuza mmene tikumvera chfukwa cha vuto linalake limene tikukumana nalo.—Sal. 55:22.
Pamene ankavutika ndi nkhawa chifukwa cha kusabereka komanso kunyozedwa ndi mkazi mnzake, Hana anauza Yehova nkhawa zake kuchokera pansi pa mtima (Onani ndime 13)
14. (a) Kodi tingaphunzirenso chiyani kwa Hana? (b) Kodi kuganizira mozama Mawu a Mulungu kungatithandize bwanji kuti tipeze zoti tinene m’pemphero? (Onani mawu a m’munsi.)
14 Patapita zaka zochepa Samueli atabadwa, Hana anapita naye kwa Eli yemwe anali mkulu wa ansembe. (1 Sam. 1:24-28) M’pemphero lake lochokera pansi pa mtima, Hana anayamikira Yehova chifukwa amateteza ndi kusamalira atumiki ake okhulupirika.c (1 Sam. 2:1, 8, 9) N’kutheka kuti mavuto ake a kunyumba sanatheretu, komabe Hana ankaganizira kwambiri mmene Yehova anamudalitsira. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tingakwanitse kupirira mavuto amene takhala tikulimbana nawo tikamaganizira mmene Yehova wakhala akutithandizira mpaka pano.
15. Kodi tingaphunzire chiyani pa pemphero la mneneri Yeremiya tikakumana ndi zinthu zopanda chilungamo? (Yeremiya 12:1)
15 Werengani Yeremiya 12:1. Pa nthawi ina, mneneri Yeremiya anakhumudwa ataona kuti anthu oipa zinthu zikuwayendera bwino komanso chifukwa cha zimene Aisiraeli anzake ankamuchitira. (Yer. 20:7, 8) Tingamvetse zimenezi tikaganizira mmene timamvera tikaona anthu oipa zinthu zikuwayendera bwino kapenanso akamatinyoza. Ngakhale kuti Yeremiya anafotokoza mmene ankamvera, sanaimbe Mulungu mlandu wochita zinthu mopanda chilungamo. Ataona chilango chimene Yehova anapereka kwa anthu opandukawo, anayamba kukhulupirira kwambiri Yehova yemwe ndi wachilungamo. (Yer. 32:19) Ifenso tingauze Yehova momasuka mmene tikumvera, n’kumakhulupirira kuti pa nthawi yake yoyenera adzakonza zinthu zonse zopanda chilungamo.
16. Ngati tikuona kuti sitingakwanitse kuchita zinazake, kodi tingaphunzire chiyani kwa Mlevi wina amene anali ku ukapolo? (Salimo 42:1-4) (Onaninso zinthunzi.)
16 Werengani Salimo 42:1-4. Nyimboyi inalembedwa ndi Mlevi wina, amene anali ku ukapolo ndipo sankakwanitsa kukalambira limodzi ndi Aisraeli anzake. Nyimbo yakeyi imasonyeza mmene iye ankamvera. Tingamvetse mmene Mleviyu ankamvera ngati tikulephera kuchoka panyumba kapena tili m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chathu. Tingamasinthesinthe mmene tikumvera, koma mulimonse mmene zilili tizimuuza Yehova. Zimenezi zingatithandize kuti tiyambe kuganiza bwino komanso kuona zinthu moyenera. Mwachitsanzo, Mleviyu anazindikira kuti akhoza kutamandanso Yehova mnjira zina zosiyanasiyana. (Sal. 42:5) Ankaganiziranso mmene Yehova akumuthandizira. (Sal. 42:8) Kupemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima kungatithandize kuti tidziwe mmene tikumvera, tiyambenso kuona zinthu moyenera komanso tipeze mphamvu kuti tipirire mavuto athu.
Mlevi amene analemba Salimo 42 anapemphera kwa Mulungu mochokera pansi pa mtima. Tikamauza Yehova mavuto athu timayamba kuona zinthu moyenera (Onani ndime 16)
17. (a) Kodi tingaphunzire chiyani pa pemphero la mneneri Yona? (Yona 2:1, 2) (b) Kodi mawu ena otchulidwa m’nyimbo za m’buku la Masalimo, angatithandize bwanji tikamakumana ndi mavuto? (Onani mawu a m’munsi)
17 Werengani Yona 2:1, 2. Mneneri Yona anapereka pempheroli ali m’mimba mwa chinsomba chachikulu. Ngakhale kuti pa nthawiyi sanamvere Yehova, iye sankakayikira kuti Yehova amva pemphero lake. Popemphera, Yona anagwiritsa ntchito mawu ambiri amene ali m’nyimbo za m’buku la Masalimo.d N’zosakayikitsa kuti ankazidziwa bwino nyimbo zimenezi. Choncho kuganizira nyimbozi kunamutsimikizira kuti Yehova amuthandiza. Ifenso tikamaloweza mavesi ena a m’Baibulo, tingamawakumbukire ndipo angatithandize tikamapemphera kwa Yehova pamene takumana ndi mavuto.
KUPEMPHERA KUMATITHANDIZA KUTI TIKHALE PA UBWENZI WABWINO NDI YEHOVA
18-19. Ngati nthawi zina zimativuta kufotokoza mmene tikumvera tikamapemphera, kodi lemba la Aroma 8:26, 27 lingatithandize bwanji? Perekani chitsanzo.
18 Werengani Aroma 8:26, 27. Nthawi zina timakhala ndi nkhawa kwambiri moti timalephera kumufotokozera Yehova mmene tikumvera. Koma pa nthawi ngati zimenezi, mzimu woyera wa Mulungu, “umachonderera” mʼmalo mwathu. Kodi umachita bwanji zimenezi? Pogwiritsa ntchito mzimu woyera, Yehova anathandiza anthu amene analemba Baibulo kuti alembe mapemphero ambiri. Tikamalephera kufotokoza bwinobwino mmene tikumvera, Yehova angagwiritse ntchito zimene zinalembedwa m’mapempherowa, ngati kuti ndi mapemphero amene ifeyo timafuna kupereka ndipo amatha kuwayankha.
19 Mfundo imeneyi inathandiza mlongo wina wa ku Russia dzina lake Yelena. Iye anamangidwa chifukwa chopemphera komanso kuwerenga Baibulo. Yelena anali ndi nkhawa kwambiri moti zinkamuvuta kupemphera. Iye anati: “Ndinakumbukira kuti ngati ndili ndi nkhawa kwambiri n’kumalephera kupemphera, Yehova angaone mapemphero a atumiki ake amene analembedwa m’Baibulo . . . ngati mapemphero amene ineyo ndikanapereka. . . Zimenezi zinandithandiza kwambiri pa nthawi yovutayi.”
20. N’chiyani chingakuthandizeni kuti mukwanitse kupemphera mukakhala ndi nkhawa?
20 Tikakhala ndi nkhawa tingayambe kuganizira zinthu zina pamene tikupemphera. Kuti maganizo athu akhazikike, tingawerenge kapena kumvetsera nyimbo zopezeka m’buku la Masalimo. Mofanana ndi mfumu Davide, tingathenso kulemba mmene tikumvera. (Sal. 18, 34, 142; timawu tapamwamba.) N’zoona kuti palibe malamulo amene timayenera kutsatira tikamakonzekera kupemphera. (Sal. 141:2) Muzichita zimene mukuona kuti n’zothandiza kwa inuyo.
21. N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera ndi mtima wonse?
21 N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amamvetsa mmene tikumvera ngakhale tisanamuuze chilichonse. (Sal. 139:4) Koma amasangalala tikamufotokozera mawu osonyeza kuti timamudalira. Choncho musamazengereze kupemphera kwa Atate wanu wakumwamba. Tingathenso kugwiritsa ntchito mawu opezeka m’mapemphero a m’Baibulo. Muzipemphera ndi mtima wanu wonse. Muzimuuza zimene zakusangalatsani komanso zomwe zikukudetsani nkhawa. Popeza Yehova ndi mnzanu wapamtima, iye adzakuthandizani nthawi zonse.
NYIMBO NA. 45 Zimene Ndimaganizira Mozama
a Onani makhalidwe ena a Yehova ochititsa chidwi amene ali m’kabuku kakuti Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu pamutu wakuti “Yehova.”
b Mapemphero amene timapereka pagulu poimira mpingo amafunika azikhala aafupi.
c Popemphera, Hana ananena mawu ena ofanana ndi amene Mose analemba. N’zosakayikitsa kuti ankakhala ndi nthawi yokwanira yoganizira Malemba. (Deut. 4:35; 8:18; 32:4, 39; 1 Sam. 2:2, 6, 7) Patapita zaka zambiri, Mariya, yemwe ndi Mayi wa Yesu, anagwiritsa ntchito mawu otamanda ofanana ndi amene Hana anagwiritsa ntchito.—Luka 1:46-55.
d Mwachitsanzo, yerekezerani Yona 2:3-9 ndi Salimo 69:1; 16:10; 30:3; 142:2, 3; 143:4, 5; 18:6 ndi 3:8, m’ndondomeko imene Yona anawagwiritsira ntchito.