Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 October tsamba 24-29
  • Muzikumbukira Kupempherera Anthu Ena

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzikumbukira Kupempherera Anthu Ena
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUPEMPHERERA ENA?
  • TIZIPEMPHERERA ENA
  • ZIMENE TINGANENE POPEMPHERERA MUNTHU ALIYENSE PAYEKHA
  • TIZIONA MOYENERA MAPEMPHERO ATHU
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kuti Mulungu Akhale Mnzanu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Mungatani Kuti Mapemphero Anu Azikhala Ochokera Pansi pa Mtima?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • ‘Pemphereranani’
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 October tsamba 24-29

NKHANI YOPHUNZIRA 43

NYIMBO NA. 41 Imvani Pemphero Langa

Muzikumbukira Kupempherera Anthu Ena

“Ndi kupemphererana . . . Pemphero lopembedzera la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.”—YAK. 5:16.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona kufunika kopempherera ena komanso mmene tingachitire zimenezi.

1. Kodi timadziwa bwanji kuti mapemphero athu ndi ofunika kwa Yehova?

PEMPHERO ndi mphatso yapadera. Taganizirani mfundo iyi: Yehova anapereka ntchito zina kwa angelo. (Sal. 91:11) Anaperekanso maudindo ofunika kwambiri kwa Mwana wake. (Mat. 28:18) Koma kodi anapereka udindo womvetsera mapemphero kwa aliyense? Ayi. Yehova anasankha kuti udindowu ukhale wake wokha basi. Yehova, yemwe ndi “Wakumva pemphero,” amamvetsera yekha mapemphero athu.—Sal. 65:2.

2. Kodi mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yopempherera ena?

2 Tingapemphere kwa Yehova n’kumuuza nkhawa zathu. Komabe tizipemphereranso anthu ena. Zimenezi n’zimene mtumwi Paulo anachita. Mwachitsanzo, analembera mpingo wa ku Efeso kuti: “Ndikupitirizabe kukupemphererani.” (Aef. 1:16) Paulo ankapemphereranso anthu osiyanasiyana. Mwachitsanzo, iye anauza Timoteyo kuti: “Ndikuthokoza Mulungu . . . ndipo sindiiwala kukutchula mʼmapemphero anga opembedzera, usana ndi usiku.” (2 Tim. 1:3) Paulo anali ndi mavuto ake amene ankafunika kuwapempherera. (2 Akor. 11:23; 12:​7, 8) Ngakhale zinali choncho, ankapezabe nthawi yopempherera ena.

3. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatipangitse kuti tiiwale kupempherera ena?

3 Nthawi zina tikhoza kuiwala kupempherera ena. Chifukwa chiyani? Mlongo wina dzina lake Sabrinaa anatchula chifukwa chimodzi. Iye anati: “Anthufe timatanganidwa kwambiri. Tikhoza kumangoganizira za mavuto athu, n’kumangopemphera zokhudza ifeyo basi.” Kodi inunso nthawi zina zimenezi zimakuchitikirani? Ngati ndi choncho, nkhaniyi ikuthandizani. Ifotokoza (1) chifukwa chake timafunika kupempherera ena komanso (2) mmene tingachitire zimenezi.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUPEMPHERERA ENA?

4-5. Kodi mapemphero amene timapempherera ena ‘angagwire bwanji ntchito mwamphamvu kwambiri?’ (Yakobo 5:16)

4 Mapemphero amene timapempherera ena ‘amagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.’ (Werengani Yakobo 5:16.) Kodi zinthu zingasinthedi pa moyo wa munthu winawake chifukwa choti tamupempherera? Inde. Yesu atadziwa kuti Petulo amukana pasanapite nthawi, anamuuza kuti: “Ine ndakupempherera kuti chikhulupiriro chako chisathe.” (Luka 22:32) Paulo nayenso ankadziwa kuti kupempherera ena kungathandize kuti zinthu zisinthe pa moyo wawo. Atamangidwa popanda chifukwa ku Roma, Paulo anauza Filimoni kuti: “Ndikukhulupirira kuti chifukwa cha mapemphero anu, ndimasulidwa kuti ndidzakutumikireni.” (Fili. 22) Zimenezi zinachitikadi. Pasanapite nthawi, Paulo anatulutsidwa m’ndende ndipo anayambiranso kulalikira.

5 Koma zimenezi sizikutanthauza kuti tikamapemphera, timakhala tikumukakamiza Yehova kuti achite zinazake. Iye amaona zimene zikudetsa nkhawa atumiki ake ndipo nthawi zina amasankha kuchita zimene amupempha. Kudziwa zimenezi kungatithandize kuti tizipemphera kwa Yehova mobwerezabwereza za vuto limene tili nalo n’kumakhulupirira kuti atiyankha m’njira yoyenera.—Sal. 37:5; onani 2 Akorinto 1:11.

6. Kodi kupempherera ena kumakhudza bwanji mmene timawaonera? (1 Petulo 3:8)

6 Kupempherera ena, kumatithandiza kuti tizikhala ndi “chifundo chachikulu.” (Werengani 1 Petulo 3:8.) Munthu wachifundo amazindikira mavuto amene ena akukumana nawo ndipo amayesetsa kupeza njira zowathandizira. (Maliko 1:​40, 41) Michael yemwe ndi mkulu ananena kuti: “Ndikamapempherera ena, ndimadziwa bwino mavuto amene akulimbana nawo ndipo zimandithandiza kuti ndiziwakonda kwambiri. Ndimawaona kuti ndi anzanga apamtima ngakhale kuti mwina sangadziwe zimenezi.” M’bale Richard, yemwe ndi mkulu anafotokoza ubwino wina. Iye anati: “Tikapempherera munthu m’pamenenso timafunitsitsa kumuthandiza.” Ananenanso kuti: “Tikathandiza munthu amene timamupempherera, zimakhala ngati tathandizira kuyankha pemphero limene tinamupempherera lija.”

7. Kodi kupempherera ena kungatithandize bwanji kuti tisamangoganizira za mavuto athu? (Afilipi 2:​3, 4) (Onaninso zithunzi.)

7 Tikamapempherera ena, timaona mavuto athu moyenera. (Werengani Afilipi 2:​3, 4.) Tonsefe tikulimbana ndi mavuto enaake chifukwa tili m’dziko limene likulamuliridwa ndi Mdyerekezi. (1 Yoh. 5:19; Chiv. 12:12) Ndiye nthawi zonse tikamapempherera ena timakumbukira kuti “abale [athu] padziko lonse akukumananso ndi mavuto ngati omwewo.” (1 Pet. 5:9) Katherine yemwe ndi mpainiya, anati: “Ndikamapempherera ena, ndimakumbukira kuti anthu enanso akukumana ndi mavuto. Zimenezi zimandithandiza kuti ndisamangoganizira mavuto anga.”

Zithunzi: Abale ndi alongo amene akulimbana ndi mavuto awo akupempherera ena. 1. Kamtsikana kali pabedi ndipo kakupemphera; banja lili muboti ndipo likuthawa kunyumba kwawo chifukwa cha kusefukira kwa madzi. 2. Banja la muchithunzi choyambirira lija likupemphera pamodzi; chithunzi cha m’bale ali kundende. 3. M’bale wamuchithunzi chapita chija akupemphera mundende; chithunzi cha mlongo wachikulire yemwe akudwala ndipo wagona m’chipatala. 4. Mlongo wamuchithunzi chapita chija akupemphera; kamtsikana komwe tinakaona m’chithunzi choyambirira chija kakhala kokhakokha m’kalasi pamene anzake akukondwerera befide.

Tikamapempherera ena, zimatithandiza kuti tisamangoganizira za mavuto athu (Onani ndime 7)d


TIZIPEMPHERERA ENA

8. Perekani zitsanzo za anthu amene tingawapempherere.

8 Tingapempherere anthu a magulu osiyanasiyana. Mwachitsanzo, tingapempherere amene akudwala, achinyamata amene amanyozedwa komanso kukakamizidwa ndi anzawo kuti achite zinthu zolakwika kusukulu kapena amene akukumana ndi mavuto chifukwa cha uchikulire. Akhristu anzathu ambiri akuzunzidwa ndi achibale awo kapenanso maboma. (Mat. 10:​18, 36; Mac. 12:5) Abale ndi alongo athu ena anathawa m’nyumba zawo chifukwa cha mavuto obwera chifukwa cha zandale. Pomwe ena akuvutika chifukwa cha ngozi za m’chilengedwe. N’kutheka kuti abale ndi alongowa sitimawadziwa. Koma tikamawapempherera timasonyeza kuti tikumvera lamulo la Yesu lakuti, “muzikondana.”—Yoh. 13:34.

9. N’chifukwa chiyani tikuyenera kupempherera abale amene akutsogolera m’gulu la Yehova komanso akazi awo?

9 Tingapemphererenso abale amene akutsogolera m’gulu la Yehova. Abale amenewa akuphatikizapo a m’Bungwe Lolamulira komanso amene amawathandizira, abale a m’Makomiti a Nthambi, oyang’anira madipatimenti kumaofesi a nthambi, oyang’anira dera, akulu komanso atumiki othandiza. Ambiri mwa abalewa akulimbana ndi mavuto awo komabe amadzipereka kuti atithandize. (2 Akor. 12:15) Mwachitsanzo, Mark yemwe ndi woyang’anira dera ananena kuti: “Limodzi mwa mavuto akuluakulu amene amandidetsa nkhawa ndi lakuti ndimakhala kutali kwambiri ndi makolo anga omwe ndi achikulire ndipo onse ali ndi mavuto okhudza thanzi. Ngakhale kuti mchemwali wanga ndi mwamuna wake amawasamalira, zimandiwawa kwambiri kuona kuti sindingathe kuchita zambiri powathandiza.” Ngakhale kuti sitingadziwe zonse zimene zimadetsa nkhawa abale akhamawa, tizikumbukira kuwapempherera. (1 Ates. 5:​12, 13) Tingachitenso bwino kupempherera akazi a abalewa amene amathandiza amuna awo mokhulupirika kuti apitirize kuchita utumiki wawo.

10-11. Kodi Yehova angasangalale ndi mapemphero athu ngakhale kuti sitinatchule abale ndi alongo mwachindunji? Fotokozani.

10 Monga taonera, nthawi zambiri timapempherera magulu a abale ndi alongo osiyanasiyana. Mwachitsanzo, ngakhale kuti sitikuganizira winawake, tingapemphe Yehova kuti athandize abale ndi alongo amene ali m’ndende komanso kutonthoza amene aferedwa. Donald yemwe ndi mkulu anati: “Pali abale ndi alongo ambiri amene akukumana ndi mavuto moti nthawi zina ndimangowapempherera onsewo pamodzi.”

11 Kodi Yehova amasangalala ndi mapemphero amenewa? Inde. Ndipotu sitingathe kudziwa ndendende zimene m’bale kapena mlongo aliyense akufunikira. Choncho n’zoyenera kupempherera abale ndi alongo onse pamodzi. (Yoh. 17:20; Aef. 6:18) Mapemphero amenewa amasonyeza kuti ‘timakonda gulu lonse la abale.’—1 Pet. 2:17.

ZIMENE TINGANENE POPEMPHERERA MUNTHU ALIYENSE PAYEKHA

12. Kodi kuchita chidwi ndi ena kungatithandize bwanji kuti tizitchula zenizeni zimene zikuwachitikira tikamawapempherera?

12 Muzichita chidwi ndi ena. Kuwonjezera pa kupempherera abale ndi alongo monga gulu, tizipemphereranso aliyense payekha pomutchula dzina. Kodi mumpingo wanu muli aliyense amene akudwala matenda okhalitsa? Kodi muli wachinyamata amene ali ndi nkhawa chifukwa anzake amamukakamiza kuti azichita zoipa? Kodi pali kholo limene likuyesetsa kulera lokha mwana “mogwirizana ndi zimene Yehova amanena”? (Aef. 6:4) Tikamachita chidwi ndi ena, zidzatithandiza kuti tiziwachitira chifundo, tiziwakonda kwambiri ndipo zidzatilimbikitsa kuti tiziwapempherera.b—Aroma 12:15.

13. Tingatani kuti tizipempherera anthu amene sitikuwadziwa?

13 Muzipempherera ena powatchula dzina. Tikhoza kuchita zimenezi ngakhale kwa anthu amene sitinakumanepo nawo. Mwachitsanzo, taganizirani za abale ndi alongo amene ali m’ndende ku Crimea, Eritrea, Russia ndi Singapore. Mungapeze mayina a abale ndi alongo omwe ali m’ndende pa jw.org.c Woyang’anira dera wina dzina lake Brian ananena kuti: “Ndikalemba dzina la m’bale kapena mlongo amene ali m’ndende n’kuliwerenga mokweza, zimandithandiza kuti ndikumbukire munthuyo n’kumutchula ndikamapemphera.”

14-15. Tingatani kuti tikamapempherera ena tizitchula zenizeni zomwe tikufuna?

14 Muzitchula zinthu zenizeni zimene mukufuna. Michael amene tamutchula kale uja ananena kuti: “Ndikamawerenga pa jw.org za abale ndi alongo amene ali m’ndende, ndimayesa kuganizira mmene ndikanamvera zikanakhala kuti ineyo ndi amene ndamangidwa. Ndikudziwa kuti bwenzi ndikudera nkhawa za mkazi wanga komanso ndikanayesetsa kuti azipeza zofunika pa moyo wake. Zimenezi zimandithandiza kuti ndizidziwa zinthu zenizeni zimene ndingatchule ndikamapempherera abale okwatira omwe ali m’ndende.”—Aheb. 13:3.

15 Tikamaganizira zimene abale ndi alongo omwe ali m’ndende amakumana nazo tsiku ndi tsiku, zingatithandize kupeza zinthu zina zimene tingatchule tikamawapempherera. Mwachitsanzo, tingapemphere kuti oyang’anira ndende azichitira chifundo abale ndi alongo athu komanso kuti olamulira aziwalola kuti azilambira momasuka. (1 Tim. 2:​1, 2) Tingapempherenso kuti abale ndi alongo mumpingo alimbikitsidwe chifukwa cha kukhulupirika kwa m’bale kapena mlongo amene ali m’ndende. Komanso kuti anthu omwe si Mboni azichita chidwi ndi khalidwe lake n’kumvetsera uthenga wathu. (1 Pet. 2:12) Mfundozi zingatithandizenso tikamapempherera abale ndi alongo amene akukumananso ndi mavuto ena. Tikamachita chidwi ndi ena, kuwapempherera potchula mayina awo komanso kutchula zenizeni zimene tikufuna kuti Yehova awachitire, timasonyeza kuti ‘timakondana kwambiri.’—1 Ates. 3:12.

TIZIONA MOYENERA MAPEMPHERO ATHU

16. Kodi tingatani kuti tiziona moyenera mapemphero athu? (Mateyu 6:8)

16 Monga taonera, tikamapempherera ena zinthu zingasinthe pa moyo wawo. Komabe mfundo imeneyi tiyenera kuiona moyenera. Tizikumbukira kuti tikamapemphera timakhala tikuuza Yehova zinthu zimene akuzidziwa kale komanso sikuti iye amafuna malangizo athu a mmene angachitire zinazake. Yehova amadziwa zimene atumiki ake akufunikira, iwowo kapena ifeyo tisanazidziwe n’komwe. (Werengani Mateyu 6:8.) Ndiye n’chifukwa chiyani timapempherera anthu ena? Kuwonjezera pa zifukwa zimene taziona kale munkhaniyi, tikamapempherera ena timasonyeza kuti timawaganizira. Chikondi chimatilimbikitsa kuti tizipemphererana. Ndipo Yehova amasangalala akaona kuti atumiki ake akumutsanzira posonyeza ena chikondi.

17-18. Kodi mapemphero amene timapempherera abale ndi alongo tingawayerekezere ndi chiyani?

17 Ngakhale mapemphero athu atapanda kusintha zinthu pa moyo wa abale ndi alongo athu, amasonyeza kuti timawakonda ndipo Yehova amaona. Tingayerekezere zimenezi ndi banja limene lili ndi ana awiri aang’ono, wamwamuna ndi wamkazi. Mwana wamwamunayo akudwala ndipo ali chigonere. Kamtsikanako kakupempha bambo ake kuti: “Chonde muthandizeni mchimwene wangayu. Wadwalatu kwambiri.” Bambowo akudziwa kale mmene zinthu zilili, amamukonda kwambiri mwanayo ndipo akumusamalira bwino. Komabe bambowo akusangalala poona kuti mwanayo amamukonda kwambiri mchimwene wakeyo ndipo akupempha bambowo kuti amuthandize.

18 Zimenezitu ndi zimene Yehova amafuna kuti tizichita. Amafuna kuti tizikondana komanso tizipemphererana. Tikamachita zimenezi mapemphero athu amasonyeza kuti timakonda anzathu kuchokera pansi pa mtima ndipo Yehova amaona zimenezi. (2 Ates. 1:3; Aheb. 6:10) Monga taonera, nthawi zina mapemphero athu angathandize kuti zinthu zisinthe pa moyo wa anthu ena. Choncho tiyeni tichite zonse zomwe tingathe kuti tizikumbukira kupempherera anthu ena.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi mapemphero athu ‘angagwire bwanji ntchito mwamphamvu kwambiri’?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kupempherera abale ndi alongo athu monga gulu?

  • Kodi tingatani kuti tizitchula zenizeni zimene tikufuna tikamapempherera anthu ena?

NYIMBO NA. 101 Tizichita Zinthu Mogwirizana

a Mayina ena asinthidwa.

b Onerani vidiyo ya pa jw.org yakuti, Takeshi Shimizu: Yehova Ndi “Wakumva Pemphero.”

c Kuti mupeze mayina a Akhristu anzathu amene ali m’ndende, fufuzani pa jw.org mbali yakuti, “A Mboni za Yehova Anamangidwa Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira—Potengera Dera.”

d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Abale ndi alongo amene akukumana ndi mavuto pa moyo wawo akupemphereranso anthu ena.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena