INDONESIA
Ndinapulumuka Pamene Chipani cha Chikomyunizimu Chinkafuna Kulanda Boma
Ronald Jacka
CHAKA CHOBADWA 1928
CHAKA CHOBATIZIDWA 1941
MBIRI YAKE Anatumikira monga mtumiki wa nthambi ku Indonesia kwa zaka zoposa 25.
M’MAWA wa pa 1 October, 1965, asilikali amene ankagwirizana ndi chipani cha Chikomyunizimu ku Indonesia, anapha akuluakulu a asilikali a boma 6, omwe anali odziwika kwambiri n’cholinga chofuna kulanda boma. Zimenezi zitachitika, asilikali a boma anabwezera mwankhanza. Anthu pafupifupi 500,000 omwe ankawaganizira kuti anali m’chipani cha Chikomyunizimu anaphedwa ndipo kuchokera pa nthawiyi, ku Indonesia sikunachitikenso zinthu zoopsa ngati zimenezi.
Patapita milungu yochepa kuchokera pa nthawiyi, munthu wina yemwe anali mkulu wa asilikali anandiuza kuti dzina langa linalembedwa pa mayina a atsogoleri achipembedzo a m’dera lathu, omwe a chipani cha Chikomyunizimu ankafuna kuwapha. Anandiuzanso kuti akhoza kukandionetsa pamene anakumba manda omwe ankafuna kuti andiikepo akandipha, koma ndinakana. Chifukwa chakuti mavuto a zandale anali akupitirirabe, sindinafune kuti anthu ayambe kuganiza kuti ndayamba kulowerera za ndale akandiona ndili ndi mkuluyu.