Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 183
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yokhala Ndi Anzathu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yokhala Ndi Anzathu?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Kodi mnzathu wabwino tingamudziwe bwanji?
  • Kodi m’Baibulo muli zitsanzo ziti za anthu amene anali mabwenzi abwino?
  • Kodi n’zotheka kukhala mnzake wa Mulungu?
  • Mungathe Kukhalabe ndi Mabwenzi M’dziko Lopanda Chikondi Lino
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Nchifukwa Ninji Sindimakhala ndi Mabwenzi?
    Galamukani!—1996
  • Mungakhale ndi Maubwenzi Okhalitsa
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Anzanu Azikhala Anthu Amene Amakonda Yehova
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 183
Anthu amisinkhu yosiyanasiyana ali limodzi kuwotha moto ndipo wina akuimba gitala.

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yokhala Ndi Anzathu?

Yankho la m’Baibulo

Kukhala ndi anzathu kumathandiza kuti tikhale osangalala komanso kuti zinthu zizitiyendera bwino. Anzathu abwino angatilimbikitse komanso kutithandiza kukhala anthu abwino.—Miyambo 27:17.

Koma Baibulo limatsindika za kufunika kosankha mosamala anthu omwe tikufuna kuti akhale anzathu. Limatichenjeza za zimene zingachitike tikamacheza ndi anthu oipa. (Miyambo 13:20; 1 Akorinto 15:33) Anthu oterewa angachititse kuti tisankhe zinthu mopanda nzeru komanso kuti tisiye kukhala ndi makhalidwe abwino.

Zimene zili munkhaniyi

  • Kodi mnzathu wabwino tingamudziwe bwanji?

  • Kodi m’Baibulo muli zitsanzo ziti za anthu amene anali mabwenzi abwino?

  • Kodi n’zotheka kukhala mnzake wa Mulungu?

  • Mavesi a m’Baibulo okhudza kupeza anzathu abwino

Kodi mnzathu wabwino tingamudziwe bwanji?

Baibulo limaphunzitsa kuti sitiyenera kungopeza anzathu amene amakonda zosangalatsa zimene ifenso timakonda. Mwachitsanzo, lemba la Salimo 119:63 limanena kuti: “Ine ndine mnzawo wa anthu okuopani,a ndiponso wa anthu osunga malamulo anu.” Wolemba Baibuloyu ananena kuti iye ankasankha anzake amene ankaopa Mulungu komanso omwe ankafunitsitsa kutsatira mfundo zake.

Baibulo limafotokozanso makhalidwe abwino amene mnzathu wabwino ayenera kukhala nawo. Mwachitsanzo limati:

  • “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.

  • “Pali mabwenzi amene amafuna kuthyolana, koma pali bwenzi limene limamatirira kuposa m’bale wako.”—Miyambo 18:24.

Mavesiwa amasonyeza kuti mnzathu wabwino ndi munthu wokhulupirika, wachikondi, wokoma mtima komanso wopatsa. Mnzathu weniweni ndi munthu amene tingamudalire kuti atithandiza pa nthawi zabwino ndi zovuta zomwe. Komanso mnzathu weniweni amalimba mtima n’kutichenjeza tikafuna kuchita zinthu zosayenera kapena kusankha zinthu mopanda nzeru.—Miyambo 27:6, 9.

Kodi m’Baibulo muli zitsanzo ziti za anthu amene anali mabwenzi abwino?

M’Baibulo muli zitsanzo za anthu amene anali ndi anzawo abwino ngakhale kuti ankasiyana misinkhu, kochokera, chikhalidwe komanso udindo. Tiyeni tione zitsanzo zitatu.

  • Rute ndi Naomi. Rute anali mpongozi wa Naomi ndipo n’kutheka kuti ankasiyana kwambiri zaka. Komanso Rute anali wachikhalidwe chosiyana ndi cha Naomi. Ngakhale kuti ankasiyana chonchi, ankagwirizana komanso kukondana kwambiri.—Rute 1:16.

  • Davide ndi Yonatani. Ngakhale kuti zikuoneka kuti Yonatani anali wamkulu kwa Davide ndi zaka 30, Baibulo limanena kuti Davide ndi Yonatani ’ankagwirizana kwambiri.’—1 Samueli 18:1.

  • Yesu ndi atumwi ake. Yesu anali ndi udindo waukulu kuposa atumwi ake chifukwa anali mphunzitsi komanso mbuye wawo. (Yohane 13:13) Koma iye sankawaona kuti ndi osayenera kukhala anzake. M’malomwake, Yesu ankakonda kwambiri anthu amene ankatsatira zimene iye ankaphunzitsa. Iye anati: “Ndakutchani mabwenzi, chifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.”—Yohane 15:14, 15.

Kodi n’zotheka kukhala mnzake wa Mulungu?

Inde, n’zotheka anthu kukhala anzake a Mulungu. Baibulo limanena kuti: “Yehova amakonda anthu owongoka mtima.” (Miyambo 3:32) Choncho Mulungu amagwirizana ndi anthu amene ali ndi makhalidwe abwino, oona mtima, aulemu komanso amene amayesetsa kutsatira mfundo zake zokhudza zoyenera ndi zosayenera. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti Abulahamu, yemwe anali munthu wokhulupirika, anali bwenzi la Mulungu.—2 Mbiri 20:7; Yesaya 41:8; Yakobo 2:23.

a Mavesi ena a mu salimoli amasonyeza kuti mawu oti “okuopani,” amanena za anthu oopa Mulungu.

Mavesi a m’Baibulo omwe angatithandize kupeza anzathu abwino

Salimo 119:63: “Ine ndine mnzawo wa anthu okuopani, ndiponso wa anthu osunga malamulo anu.”

Mfundo yake: Tiyenera kupeza anzathu amene amakhulupirira Mulungu komanso omwe amafunitsitsa kutsatira mfundo zake.

Miyambo 3:32: “Munthu wochita zachiphamaso Yehovab amanyansidwa naye, koma amakonda anthu owongoka mtima.”

Mfundo yake: Anthu amene amafuna kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu ayenera kupewa chinyengo komanso ayenera kukhala ndi makhalidwe abwino.

Miyambo 13:20: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.”

Mfundo yake: Anthu amatengera anzawo pa nkhani ya makhalidwe abwino komanso oipa.

Miyambo 17:17: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”

Mfundo yake: Anzathu enieni ndi amene amatithandiza pa nthawi zabwino komanso zovuta..

Miyambo 18:24: “Pali mabwenzi amene amafuna kuthyolana, koma pali bwenzi limene limamatirira kuposa m’bale wako.”

Mfundo yake: Mnzathu weniweni sangatidyere masuku pamutu. Koma amakhala wokhulupirika, wodalirika komanso wachikondi.

Miyambo 27:6: “Zilonda zovulazidwa ndi munthu wokukonda zimakhala zokhulupirika.”

Mfundo yake: Mnzathu wabwino sangaope kutilangiza pakafunika.

Miyambo 27:17: “Chitsulo chimanola chitsulo chinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.”

Mfundo yake: Mnzathu weniweni amatithandiza kukhala munthu wabwino.

b Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena