Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 32
  • Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Nkhawa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Nkhawa?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Zimene Mulungu amapereka kuti atithandize
  • “Mulungu wa Chitonthozo Chonse” Amathandiza
    Galamukani!—2009
  • Chitonthozo kwa Opsinjika Maganizo
    Chitonthozo kwa Opsinjika Maganizo
  • Kupambana Nkhondo Yolimbana ndi Kuchita Tondovi
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Mmene mungathandizire Ochita Tondovi Kupezanso Chimwemwe
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 32

Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Nkhawa?

Yankho la m’Baibulo

Inde. Tikutero chifukwa chakuti Mulungu ndi amene angatithandize kwambiri. Pajatu Baibulo limati: “Mulungu, amene amatonthoza mtima wopsinjika, anatitonthoza ife mtima.”—2 Akorinto 7:6, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

Zimene Mulungu amapereka kuti atithandize

  • Mphamvu. Mulungu ‘amatitonthoza’ poyankha mapemphero athu opempha mphamvu kuti tipirire osati pongochotsa mavutowo. (Afilipi 4:13) Musakayikire kuti Mulungu ndi wokonzeka kumvetsera mapemphero anu. Baibulo limati: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.” (Salimo 34:18) Mulungu amamvetsa zimene mukufuna kunena ngakhale pamene mukusowa mawu oti mufotokozere mmene mukumvera mumtima.—Aroma 8:26, 27.

  • Zitsanzo za m’Baibulo. Munthu wina amene analemba nawo Baibulo anapemphera kuti: “Pa nthawi imene zinthu zinandivuta kwambiri ndinaitana pa inu.” Iye analimbikitsidwa atakumbukira kuti Mulungu amafunitsitsa kutikhululukira. Ananena kwa Mulungu kuti: “Mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa, ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova? Inu mumakhululukiradi, kuti anthu akuopeni.”—Salimo 130:1, 3, 4.

  • Chiyembekezo. Masiku ano, Mulungu amatitonthoza komanso walonjeza kuti adzachotsa mavuto onse amene amatidetsa nkhawa. Zimenezi zikadzachitika, “zinthu zakale [monga nkhawa] sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.”—Yesaya 65:17.

Dziwani izi: A Mboni za Yehova amadziwa kuti Mulungu amathandiza anthu amene ali ndi nkhawa koma nawonso amapita kuchipatala ngati akudwala matenda a maganizo. (Maliko 2:17) Sitilimbikitsa anthu kulandira chithandizo chinachake kuchipatala chifukwa munthu aliyense ayenera kusankha yekha pa nkhani ngati zimenezi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena