7 Ndiyeno Mose anatenga tenti yake nʼkukaimanga kunja kwa msasa, chapatali ndi msasawo ndipo tentiyo anaipatsa dzina lakuti chihema chokumanako. Aliyense amene ankafuna kufunsa malangizo kwa Yehova+ ankapita kuchihema chokumanako chimene chinali kunja kwa msasa.