51 Kenako azitenga nthambi ya mtengo wa mkungudza, kamtengo ka hisope, ulusi wofiira kwambiri ndi mbalame yamoyo ija. Zimenezi aziziviika mʼmagazi a mbalame imene yaphedwa pamwamba pa madzi otunga kumtsinje ija, ndipo azidontheza magaziwo maulendo 7+ cha kumene kuli nyumbayo.