51 Kenako azitenga nthambi ya mtengo wa mkungudza, kamtengo ka hisope,+ ulusi wofiira kwambiri ndi mbalame yamoyo ija. Zimenezi aziziviika m’magazi a mbalame imene yaphedwa pamwamba pa madzi otunga kumtsinje ija, ndipo azidontheza magaziwo+ maulendo 7+ cha kumene kuli nyumbayo.