17 Yehova Mulungu wathu ndi amene anatitulutsa mʼdziko la Iguputo pamodzi ndi makolo athu,+ kutichotsa kudziko lomwe tinali akapolo.+ Iye anachita zizindikiro zazikulu pamaso pathu+ ndi kutiteteza njira yonse. Anatitetezanso kwa anthu onse amene tinadutsa pakati pawo.+